Zomwe Msilamu sakuyenera kuti asazidziwe (Chichewa)

Zomwe Msilamu sakuyenera kuti asazidziwe

  • earth Chiyankhulo
    (Chichewa)
  • earth Kulemba buku:
    اللجنة العلمية برئاسة الشؤون الدينية بالمسجد الحرام والمسجد النبوي

Zomasulira zina 61

nl هولندي- Nederlands mk مقدوني- македонски te تلغو- తెలుగు sw سواحيلي- Kiswahili rw كينيارواندا- Kinyarwanda ru روسي- Русский es إسباني- español ms ملايو- Melayu ka جورجي- ქართული tl فلبيني تجالوج- Tagalog zh صيني- 中文 gu غوجاراتية- ગુજરાતી fr فرنسي- Français ps بشتو- بشتو id إندونيسي- Indonesia hi هندي- हिन्दी ar عربي- العربية bn بنغالي- বাংলা ha هوسا- Hausa ky قرغيزي- Кыргызча fa فارسي- فارسي ur أردو- اردو en إنجليزي- English da دنماركي- dansk hu هنجاري مجري- magyar tg طاجيكي- тоҷикӣ ta تاميلي- தமிழ் th تايلندي- ไทย ml مليالم- മലയാളം si سنهالي- සිංහල uz أوزبكي- Ўзбек ne نيبالي- नेपाली om أورومو- afaan oromoo am أمهري- አማርኛ tr تركي- Türkçe ti تجريني- ትግርኛ so صومالي- Soomaali vi فيتنامي- Tiếng Việt ff فولاني- Pulaar kk كازاخي- қазақ тілі no نرويجي- Norwegian mfe كريولي- créole ko كوري- 한국어 bs بوسني- bosanski mg ملاغاشي- Malagasy sn الشونا- Shona mos موري- Mõõré ro روماني- română yo يوربا- Èdè Yorùbá prs دري- فارسی دری dyo جوالا- Jóola st سوتي- Sesotho ig إيجبو- Igbo az أذري- azərbaycanca cs تشيكي- čeština lt ليتواني- lietuvių sv سويدي- svenska af أفريقاني- Afrikaans wo ولوف- Wollof zu زولو- isiZulu ny شيشيوا- Chichewa
PHPWord

 

مَا لَا يَسَعُ المُسْلِمَ جَهْلُهُ

 

 

Zomwe Msilamu sakuyenera kuti asazidziwe

 

 

 

 

اللَّجْنَةُ العِلْمِيَّةُ

بِرِئَاسَةِ الشُّؤُونِ الدِّينِيَّةِ بِالمَسْجِدِ الحَرَامِ وَالمَسْجِدِ النَّبَوِيِّ

 

Komiti yoona za maphunziro pansi pa utsogoleri wa za chipembedzo ku Mzikiti olemekezeka wa ku Makka ndi Mzikiti wa Mtumiki ku Madina

بِسْمِ اللهِ الرَّحمَنِ الرَّحِيمِ

Zomwe Msilamu sakuyenera kuti asazidziwe

MAU OYAMBA:

Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo madalitso ndi mtendere zikhale pa amene anatumizidwa monga chisoni ku zolengedwa zonse, ndiponso pa aku banja kwake ndi omutsatira ake, ndi pa aliyense amene adatsata chiphunzitso chake, ndi kuongoka ndi chiongoko chake mpaka tsiku lachiweruzo, pambuyo pa mau awa:

Uwu ndi uthenga wachidule, wofotokoza zofunika kwambiri zomwe Msilamu amazifuna pa chikhulupiliro chake, mapemphero ake, ndi pa kachitidwe kake ndi anthu. Tidausonkhanitsira alendo aamuna ndi aakazi a Malo awiri olemekezeka, kuti adziwe ndi kuzindikira nkhani za chipembedzo chawo. Tikupempha kwa Mulungu olemekezeka, opatsa, kuti apindule nawo anthu, ndipo auchite kukhala wabwino,ochitidwira iye yekha basi. Ndithudi, iye ndiye wabwino koposa opemphedwa, ndiponso olemekezeka koposa oyembekezedwa.

Komiti yoona za maphunziro pansi pa Utsogoleri wa Nkhani zachipembedzo ku Mzikiti olemekezeka waku Makkah ndi Mzikiti wa Mtumiki.

M’dzina la Mulungu, wachifundo chambiri, wachisoni.

Gawo Loyamba:

Zokhudzana ndi chikhulupiliro

Mutu woyamba: Tanthauzo la Chisilamu ndi nsanamira zake:

Chisilamu: Ndi kuzipeleka mwa Mulungu popembedza Mulungu m'modzi yekha, ndikumutsatira Mulungu pomvera malamulo ake a Mulungu, ndikupewa za mchitidwe omuphatikiza ndi zinthu zina ndi kuwapewa anthu opanga mchitidwe umenewu.

Ndipo nsanamila zake zilipo zisanu:

1- Kuikira umboni kuti palibe wina oyenera kupembezedwa mwachoonadi koma Mulungu yekha basi ndikuti Muhammad ndi Mtumiki wake.

2- Kupemphera kasanu pa tsiku.

3- Kupereka Zakah(chalulele cha pa chaka)

4- Kusala kudya mwezi wa Ramadhan

5- Kupanga Hajj ku ku nyumba yopaturika ya Mulungu kwa yemwe ali ndi kuthekela kopita kumeneko.

 

 

 

Kufunika kwa chikhulupiliro cha umodzi wa Allah:

Dziwa kuti Mulungu wamphamvu zonse komanso olemekezeka adalenga zolengedwa kuti azimupembedza, ndipo asamphatikize naye china chilichonse. Mulungu adati:

﴿وَمَا خَلَقۡتُ ٱلۡجِنَّ وَٱلۡإِنسَ إِلَّا لِيَعۡبُدُونِ 56﴾

"Sindidalenge ziwanda ndi anthu koma kuti zizindipembedza ine". [Surat Al-Dhariyaat:56] Ndipo mapemphero amenewa sangadziwike kupatula ndi kuzindikira. Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿فَٱعۡلَمۡ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱللَّهُ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لِذَنۢبِكَ وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مُتَقَلَّبَكُمۡ وَمَثۡوَىٰكُمۡ 19﴾

"Dziwa kuti palibe ompembedza m’choonadi koma Mulungu, ndipo pempha chikhululuko pa zolakwa zako ndi zolakwa za okhulupirira aamuna ndi aakazi; ndipo Mulungu akudziwa malo anu opita ndi kubwera ndi malo anu okhazikika". [Surat Muhammad:19]، Adayamba ndi kuzindikira kusanabwere kuyankhula ndi kugwira ntchito. Chinthu chofunika kwambiri kwa Msilamu kuphunzira ndi kukhulupilira umodzi wa Mulungu; chifukwa ndicho chiyambi cha chipembedzo ndi tsinde lake, Ndipo chipembedzo sichikhazikika koma ndi chikhulupiliro cha umodzi wa Mulungu, ndipo chimenechi ndi chinthu choyamba chokakamiza kwa Msilamu, ndipo ndi chinthu chotsiriza chokakamiza. Ndipo chikhulupiliro cha umodzi wa Mulungu ndi nsanamila yoyamba mwa nsanamira za Chisilamu yomwe Msilamu aliyense wakakamizidwa kuidziwa ndi kuigwiritsa ntchito, ndipo nsanamirazo ndi zisanu. Monga mmene zabwerera mu nkhani yomwe ikuchokera kwa Abdul-Allah mwana wa Umar, Mulungu asangalasidwe nawo awiriwa, amene adanena kuti: Ndidamumva Mtumiki wa Mulungu-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- akunena kuti:

«بُنِيَ الإسْلَامُ عَلَى خَمْسٍ: شَهَادَةِ أنْ لَا إلَهَ إلَّا اللَّهُ وأنَّ مُحَمَّدًا رَسُولُ اللَّهِ، وَإقَامِ الصَّلَاةِ، وَإيتَاءِ الزَّكَاةِ، وَحَجِّ البَيْتِ، وصَوْمِ رَمَضَانَ».

«Chisilamu chinamangidwa pa nsanamira zisanu: kuikira umboni kuti palibe woyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu mmodzi yekha, ndikuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu, kupemphera mapemphero okakamizidwa, kupereka Zakat yokakamizidwa, kukachita mapemphero a Haji ku nyumba yolemekezeka, ndi kusala kudya mwezi wa Ramadhan»1.

Ndi koyenera kwa Msilamu kuphunzira tanthauzo la Tauhid; limene ndiko kumpatula Mulungu pomupembedza iye yekha basi. Asaphatikizidwe ndi wina aliyense m'mapemphero ake; ngakhale mngelo oyandikitsidwa, ngakhalenso mneneri otumidwa.

Tanthauzo la kuikira umboni kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu mmodzi yekha:

Ndiko kuti kapolo avomereze motsimikiza kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu wamphamvu zonse komanso olemekezeka, Choncho am'pembedze Mulungu yekha, ndikuchita mitundu yonse ya mapemphero pofuna kusangalatsa Iye yekha yemwe ndiwoyera; monga pemphero, kuopa, kukhala ndi chiyembekezo, kuyezamira ndi zina zotero.

Mau oikira umboni za umodzi wa Mulungu poyenera kupembedzedwa mwa choonadi komanso za utumiki wa Muhammad,samakwaniritsidwa kupatula patapezeka nsanamila ziwiri:

Choyamba: Kukana umulungu ndi kupembedzedwa kwa zinthu zina zonse kusiya Mulungu mmodzi yekha; monga mafano, milungu yaboza, ndi chopembedzedwa china chilichonse.

Chachiwiri: Kutsimikizira za umulungu ndi kupembedzedwa koona kwa Mulungu mmodzi yekha osati china chilichonse. Muklungu wapamwamba adayankhula kuti:

﴿‌وَلَقَدۡ بَعَثۡنَا فِي كُلِّ أُمَّةٖ رَّسُولًا أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱجۡتَنِبُواْ ٱلطَّٰغُوتَ...﴾

{Ndipo ndithu ku mtundu uliwonse tidatumiza Mtumiki amene amawauza kuti: “Pembedzani Mulungu mmodzi yekha ndi kupewa kupembedza Satana}. [Al-Nahl:36].

Tsono malamulo a mau a umboni oti: palibe oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu mmodzi yekha ndi awa:

Choyamba: Kuzindikira komwe kotsutsana ndi umbuli.

Chachiwiri: Chikhulupiliro chotsutsana ndi chikaiko.

Chachitatu: Kugwira ntchito pofuna kusangalasa Mulungu komwe ndikotsutsana ndikumphatikiza Mulungu ndi zina

Chachinayi: Kunena zoona komwe ndi kotsutsana ndi bodza.

Chachisanu: Chikondi chotsutsana ndi kunyasidwa.

Chachisanu ndi chimodzi: Kutsatira komwe kumatsutsana ndi kuleka.

Chachisanu ndi chiwiri: Kuvomereza kotsutsana ndi kukana.

Chachisanu ndi chitatu: Kukana chilichonse chimene chimapembedzedwa posakhala Mulungu mmodzi wapamwamba

Malamulo amenewa ndi ofunika kuwagwiritsa ntchito, ndipo asonkhanitsidwa m'ndime ziwiri za ndakatulo yotsatirayi:

Kuzindikira, chitsimikizo, kuyeretsa mtima, ndi kuyankhula zoona kwako, pamodzi ndi chikondi, kutsatira, ndiponso kuwavomereza.

Ndipo chachisanu ndi chitatu chowonjezeredwa n'chakuti ukanire zinthu zonse zopembedzedwa posakhala Mulungu mmodzi.

Kukwaniritsa kwa mau oikira umboniwa kumachitika pom'pembedza Mulungu wapamwamba yekha popanda omuphatikiza naye, ndikuyeretsera mapemphero onse kwa Mulungu mmodzi yekha. Kotero munthu asampemphe wina koma Mulungu mmodzi yekha, ndipo asayezamire mwa wina koma mwa Mulungu mmodzi yekha, komanso asayembekezere zabwino koma kuchokera kwa Mulungu mmodzi yekha, komanso asapemphere mapemphero kupatula pofuna kusangalatsa Mulungu mmodzi yekha, komanso asazinge zinyama koma pofuna kusangalatsa Mulungu mmodzi yekha mwini ulemelero ndi upamwamba.

Choncho, zomwe amachita anthu ena monga kuzungulira manda, kupempha chipulumutso kwa amene ali m'mandamo, komanso kuwapempha zosowa kumusiya Mulungu mmodzi yekha; ndi mchitidwe omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina umenewo mu mapemphero, Choncho, n'kofunika kusamala ndi kuchenjera ndi zimenezo, chifukwa zimenezo zili m'gulu la zochita za anthu omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina, monga kupembedza mafano, miyala, ndi mitengo posiya Mulungu wapamwamba. Ndipo umenewu ndi mtumu wa mchitidwe omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina omwe kamba kake mabuku adavumbulutsidwa ndipo Atumiki adatumizidwa kuti achenjeze anthu za mchitidwe umenewu ndi kuletsa za mchitidwewu.

Tanthauzo la mau oikira umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu ndi loti:

Kumulola zimene adalamula, ndikumuvomereza zimene adanena, ndikupewa zimene adaletsa ndi kuzizuzula, ndikuti Mulungu asapembedzedwe koma kupatula pozera mu njira yokhayo imene adalamulira. Potero, Msilamu amavomereza kuti Muhammad mwana wa Abdul-Allah, wa fuko la chi Quraysh ndi la Hashim, ndi Mtumiki wa Mulungu mwini mphamvu zonse komanso olemekezeka, otumidwa kwa zolengedwa zonse; ziwanda ndi anthu. Monga momwe Mulungu wapamwamba akuyankhulira:

﴿قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡ جَمِيعًا...﴾

{Nena: “E inu anthu! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mulungu kwa inu nonse...} [Al-A'raf: 158].

Ndikutinso Mulungu adamutumiza kuti afalitse chipembedzo chake ndi kuongola zolengedwa, Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿‌وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا كَآفَّةٗ لِّلنَّاسِ بَشِيرٗا وَنَذِيرٗا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ28﴾

{Ndipo sitidakutume iwe koma kwa anthu onse kuti ukhale m’neneri wa nkhani yabwino ndi wochenjeza, koma anthu ambiri sadziwa}. [Saba: 28]. Monga momwe adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿‌وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا رَحۡمَةٗ لِّلۡعَٰلَمِينَ 107﴾

{Ndipo sitidakutumize iwe koma monga chifundo kwa zolengedwa zonse}. [Al-Anbiya:107].

Ndipo chofunika cha umboni umenewu n'chakuti usakhulupirire kuti Mtumiki wa Mulungu-madalitso ndi mtendere wa Mulungu zikhale pa iye- ali ndi gawo la Umbuye ndi ulamuliro oyendetsera chilengedwe, kapena kuyenera kupembedzedwa, Koma iye ndi kapolo osapembedzedwa, ndiponso Mtumiki osayenera kutsutsidwa. Ndipo alibe mphamvu zodzipatsa yekha kapena kupatsa wina zabwino kapena zovuta, pokhapokha chimene Mulungu wafuna, Monga adanenera Allah wapamwamba:

﴿‌قُل لَّآ أَقُولُ لَكُمۡ عِندِي خَزَآئِنُ ٱللَّهِ وَلَآ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ وَلَآ أَقُولُ لَكُمۡ إِنِّي مَلَكٌۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ...﴾

{Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe za Allah kapena kuti ndikudziwa zamseri, ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine...}.

[Surat Al An'am:50].

Mutu Wachiwiri: Tanthauzo la Chikhulupiliro ndi Nsanamila zake:

Chikhulupiliro: Ndi kuvomereza ndi mtima, kulankhula ndi lilime, ndi kuchita ndi mtima ndi ziwalo, chimawonjezeka ndi kumvera, ndipo chimapunguka ndi kunyoza.

Chikhulupiliro ndi choyenera kuti mapemphero avomerezedwe ndi kulandiridwa, Monga mmene ulili mchitidwe omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina,kukanira mwa Mulungu zimaononga ntchito zonse zabwino. Monga momwe Mulungu salandira mapemphero popanda udhu, momwemonso salandira mapephero popanda chikhulupiliro. Mulungu adayankhula kuti:

﴿وَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ نَقِيرٗا 124﴾

{Ndipo amene angachite ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, pomwe iye ali wokhulupirira, iwo ndiamene adzalowa ku Munda wamtendere. Ndipo sadzaponderezedwa pa chilichonse, ngakhale chochepetsetsa kwambiri ngati kamphako ka nthangala ya tende}.

[Al-Nisa:124].

Ndipo adalongosola kuti kumuphatikiza Mulungu kumaononga ntchito zabwino, Monga adanena Allah wapamwamba:

﴿وَلَقَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ لَئِنۡ أَشۡرَكۡتَ لَيَحۡبَطَنَّ عَمَلُكَ وَلَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ 65﴾

{Ndipo ndithu kwavumbulutsidwa kwa iwe, ndi kwa amene adalipo patsogolo pako mau awa: “Ngati umphatikiza Mulungu ndi milungu yabodza ndithu ntchito zako zionongeka, ndipo ukhala mwa oluza-otaika}” [Az-Zumar:65].

Ndipo nsanamila za chikhulupiliro zilipo zisanu ndi chimodzi: Kukhulupilira mwa Mulungu, Angelo Ake, Mabuku Ake, Atumiki Ake, Tsiku Lomariza, komanso kukhulupilira za Chikonzero chake pa chilichonse, chabwino chake ndi choipa chake.

1) Kukhulupilira mwa Mulungu wapamwamba ndipo mkati mwake muli zinthu zitatu:

1- Kukhulupilira mwa Umbuye wake:

Kumeneko ndiye kumpatula Mulungu wapamwamba mu zochita zake; monga kulenga, kupereka zosowa, kupereka moyo, ndi kupereka imfa, Palibe Mlengi wina koma Mulungu mmodzi yekha, palibe opereka zosowa wina koma Mulungu mmodzi yekha palibe opatsa moyo wina koma Mulungu, palibe ochotsa moyo wina koma Mulungu, ndipo palibe amene amayendetsa zinthu zonse za m'chilengedwe koma Iye yekha, oyeretsedwa komanso wapamwamba.

Ndipo sikunadziwike kuti wina aliyense mwa zolengedwa adakana Umbuye wa Mulungu pokhapokha atakhala munthu wamakani chabe, osakhulupirira zimene akuyankhula. Monga momwe zidachitikira kwa Farao, pamene adati kwa anthu ake:

﴿‌...أَنَا ‌رَبُّكُمُ ‌الْأَعْلَى﴾

{...Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba} [Al-Nazi’at:24] Koma zimenezo sizinachokere m'chikhulupiliro chenicheni, monga adanenera Mulungu wapamwamba zokhuza Mussah-mtendere ukhale pa iye:

﴿‌قَالَ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَآ أَنزَلَ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ بَصَآئِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰفِرۡعَوۡنُ مَثۡبُورٗا 102﴾

Mûssa adati: Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza mitsutso iyi kupatula Mbuye wa thambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farao kuti waonongeka.” [Al-Isra:102] Muluingu wapamwamba wanenanso kuti:

﴿‌وَجَحَدُوا بِهَا وَاسْتَيْقَنَتْهَا أَنْفُسُهُمْ ظُلْمًا وَعُلُوًّا... ﴾

{Ndipo adazitsutsa zisonyezozo mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Allah...} [Surat Al-Naml:14].

Chifukwa ndithu, zolengedwa zonsezi ziyenera kukhala ndi Mlengi, Popeza sizingathe kudzipanga zokha; Chifukwa chinthu sichidzilenga chokha, ndiponso n’kosatheka kuti chipezeke mwazizizi; Chifukwa chinthu chilichonse chokhala ndi chiyambi, chiyenera kukhala ndi wochiyambitsa, Ndipo chifukwa chakuti kupezeka kwake kuli m’ndondomeko yodabwitsa ndiponso yogwirizana bwino, zimenezi zimalepheretsa kuti zikhale zoti zidangochitika mwazizizi, Choncho, nzosapeweka kuti zikhale ndi Mlengi, ndipo Iyeyo ndi Mulungu Mbuye wa zolengedwa zonse. Mulungu wapamwamba wati:

﴿‌أَمۡ خُلِقُواْ مِنۡ غَيۡرِ شَيۡءٍ أَمۡ هُمُ ٱلۡخَٰلِقُونَ 35 أَمۡ خَلَقُواْ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ 36﴾

{Kodi iwo adalengedwa popanda kanthu kowalenga, kapena iwo ndiwo olenga?}

Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza zoyenera kumchitira Mlengi}. [Al-Tur:35-36].

Ndipo ophatikiza Mulungu adali kuvomereza umulungu wake pa zochita zake, pomwe amamphatikiza iye ndi mafano pa nkhani ya kupembedzedwa, ndipo kuvomereza kumeneko sikunawalowetse mu Chisilamu. Ndipo mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- anawamenya nkhondo, ndipo analoleleza magazi awo ndi chuma chawo; chifukwa chakuti anamuphatikiza Mulungu ndi mafano m'mapemphero. Ndipo anapembedza zina momuphatikiza ndi iye; monga mafano, miyala, Angelo, ndi zina.

2- Kukhulupilira zoyenera kupembedzedwa kwake:

Kukhulupilira zakuyenera kopembedzedwa kwake: Kukhulupilira kuti iye yekha ndiye opembedzedwa mwachoonadi, opanda ophatikizana naye, Ndipo amatanthauza opembedzedwa ndiko kuti, opembedzedwa pomukonda,pomulemekeza, ndiponso podzichepetsa.

Mulungu wapamwamba wati:

﴿‌وَإِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۖ لَّآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلرَّحۡمَٰنُ ٱلرَّحِيمُ 163﴾

{Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha}. [Al-Baqarah:163].

Ndipo aliyense amene wadzichitira mulungu wina yemwe amamupembedza posakhala Mulungu, ndithudi umulungu wake ndi olakwika, Mulungu wapamwamba wati:

﴿ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ هُوَ ٱلۡبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ 62﴾

Zimenezo nchifukwa chakuti Mulungu ndi owona alipo ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe.Ndipo Mulungu ndi wa pamwamba mwamba wamkulu. [Al Hajj: 62].

Ndi chifukwa chake Atumiki -mtendere wa Mulungu ukhale pa onsewo- kuyambira Noah mpaka kwa Muhammad -mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- amawaitanira anthu awo kuti azipembedza Mulungu yekha ndi kumpatulira Iye mapemphera kusiya zomwe zisali iye. Ndipo Mulungu wapamwamba adatsutsa chizolowezi cha anthu omphatikiza iye ndi zolengedwa zina, chopanga milungu imene amaipembedza pamodzi ndi Mulungu oyera komanso wapamwamba, ndi kupempha thandizo ndi chipulumutso kwa iyo; ndipo adatsimikiza izi ndi umboni uwiri wa nzeru:

Choyamba: kuti milungu imene aipangayi ilibe chilichonse cha makhalidwe a Umulungu; iyo ndi yolengedwa, siilenga, ndipo siingapereke phindu kwa opembedza ake, kapenanso kuwachotsera vuto, ndipo ilibe mphamvu yopereka moyo kapena imfa, kapenanso kuukitsa akufa, Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗ لَّا يَخۡلُقُونَ شَيۡـٔٗا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ وَلَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ ضَرّٗا وَلَا نَفۡعٗا وَلَا يَمۡلِكُونَ مَوۡتٗا وَلَا حَيَوٰةٗ وَلَا نُشُورٗا 3﴾

Ndipo m’malo mwa iye Mulungu weniweni, osakhulupirira adzipangira milungu yomwe silenga chilichonse koma iyo ndi yomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza.Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera imfa kapena moyo, ngakhale kuukitsa akufa. [Al-Furqan:3].

Chachiwiri: ndichoti ophatikiza Mulungu aja ankavomereza kuti Mulungu wapamwamba ndiye Mlengi ndi oyendetsa zinthu yekha basi osati zinazo, ndipo izi zikufunikira kuti ampatule iye yekha pomupembeza monga momwe amampatulira mu Umbuye wake. Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿قُل لِّمَنِ ٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهَآ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ 84 سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ85 قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلسَّبۡعِ وَرَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ 86 سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ 87 قُلْ مَنْ بِيَدِهِ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيْءٍ وَهُوَ يُجِيرُ وَلَا يُجَارُ عَلَيْهِ إِنْ كُنْتُمْ تَعْلَمُونَ 88 سَيَقُولُونَ لِلَّهِ قُلْ فَأَنَّى تُسْحَرُونَ 89﴾

{Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa kanthu}

Adzanena kuti: “ndi za Mulungu!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira kuti iye Ngokhoza chilichonse}

Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Mpando wachifumu wa ukulu?}

Anena (kuti): “ndi za Mulungu” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?

Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.”

Adzayankha kuti : mwini wake zonse ndi Mulungu, nena kwa iwo kuti: zitheka bwanji nzeru zanu kusiya kugwira ntchito ndikumanyengeka, ndikumasiya kukhulupilira Mulungu mmodzi ndikumamutsatira komanso ndikumakhulupilira zakuka kwa akufa? [Al-Muminuna:84-89] Choncho ngati avomereza za umodzi wa Mulungu; akuyenera kumpatula iye pomupembedza yekha, ndipo asamuphatikize ndi wina aliyense m'mapemphero ake.

 

 

 

3- Kukhulupilira mu maina a Mulungu ndi mbiri zake:

Ndiko kuti: Kutsimikizira zimene Mulungu wadzitsimikizira yekha m'buku mwake, Kapena adazitsimikiza Mtumiki wa Mulungu -Madalitso ndi mtendere zipite kwa iye- mu zochita ndi zoyankhula zake ; Mwa maina ndi mbiri, m'njira yoyenerana ndi Mulungu wapamwamba, Popanda kusintha matanthauzo a mau, kapena kukana ena mwa maina a Mulungu kapena mbiri zake, Popanda kulongosola mmene zilili, kapenanso kufanizira, Mulungu wapamwamba akuyankhula kuti:

﴿‌وَلِلَّهِ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ فَٱدۡعُوهُ بِهَاۖ وَذَرُواْ ٱلَّذِينَ يُلۡحِدُونَ فِيٓ أَسۡمَٰٓئِهِۦۚ سَيُجۡزَوۡنَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ 180﴾

{Ndipo Mulungu ali nawo maina abwino. Choncho, muitaneni ndi mainawo. Alekeni amene akupotoza maina Ake posachedwapa alipidwa zomwe akhala akuchita}. [Al-Araf: 180], Mulungu wapamwamba watinso:

﴿‌...لَيۡسَ كَمِثۡلِهِۦ شَيۡءٞۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ﴾

{Palibe chilichonse chofanana ndi iye, iye ndi wakumva zonse ndiponso owona zonse}.

[Al-Shura:11].

Mitundu ya Shirk ilipo itatu:

1- Shirk yaikulu.

2- Shirk yaing'ono.

3- Shirk yobisika.

1- Shirk yaikulu:

Mfundo yake: kufananiza chosakhala Mulungu ndi Mulungu pa zinthu zomwe amachita iye yekha Mulungu. Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿‌إِذۡ نُسَوِّيكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ 98﴾

{Pamene timakufananizani ndi Mbuye wa zolengedwa}. [Al-Shu’ara:98].

Ndipo mu shirk yaikulumu mumapezeka zinthu izi: kupemphera mapemphero pofuna kusangalatsa chomwe sichili Mulungu, kapena kupereka mbali ina ya mapemperowo kwa wina osakhala iye mwini ulemelero, monga kupempha thandizo, kupempha chipulumutso, kupanga lonjezo pogwiritsa ntchito mafano, kuzinga, ndi mitundu ina ya ntchito zabwino.

Kapena mukupezekamonso: kuloleza zinthu zomwe Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka adaletsa, kapena kuletsa zomwe adaloleza, Kapena kuchosa lamulo lomwe Mulungu wamphamvu zonse komanso olemekezeka adalamulira, Monga kuchichita kukhala chololedwa chinthu chodziwika bwino m'chipembedzo kuti ndicholetsedwa; monga chigololo, kapena mowa, kapena kunyoza makolo awiri, kapena katapira kapena zinthu zina zofanana ndi zimenezo.

Kapena kuletsa zinthu zabwino zomwe Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka adaziloleza, kapena kugwetsa zomwe Mulungu adazilamulira; Monga kukhulupilira kuti kupemphera kasanu pa tsiku si kokakamizidwa, kapena kuti kusala si kokakamizidwa, kapena kuti kupereka Zakat si kokakamizidwa.

Shirk yaikulu imachititsa kuwonongeka kwa ntchito yabwino, ndikukhazikika ku moto mpaka muyaya kwa amene wamwalira akumuphatikizabe Mulungu ndi zinthu zina, Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿‌...وَلَوۡ أَشۡرَكُواْ لَحَبِطَ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ﴾

{......Akadakhala kuti Atumiki tawatchulawa adamphatikiza Mulungu ndi zina, ntchito zawo zabwino zikadaonongeka}. [Surat Al-An'am: 88].

Ndipo kuti amene wamwalira ali pa shirk yaikuluyo sadzakhululukidwa ndi Mulungu, ndipo ku mparadiso kwa iye ndi yoletsedwa, Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿‌إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَغۡفِرُ أَن يُشۡرَكَ بِهِۦ وَيَغۡفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَآءُ...﴾

{Ndithudi Mulungu sadzakhululuka mchimo lomuphatikiza ndi china chake, koma adzakhululuka machimo ena osakhala omuphatikiza ndi zinthu zina kwa amene wamfuna...}. [Al-Nisa:48] Mulungu wapamwamba watinso:

﴿إِنَّهُۥ مَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَقَدۡ حَرَّمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ ٱلۡجَنَّةَ وَمَأۡوَىٰهُ ٱلنَّارُ...﴾

{Ndithudi, amene aphatikize Mulungu ndi chinthu china, ndithudi Mulungu waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto...} [Al-Maidah:72].

2- Shirk yaing'ono:

Izi ndizomwe zatchulidwa m'malemba kuti ndi Shirk, koma sizidafike pa mlingo wa shirk yaikulu, ndiye zimenezi zimatchedwa shirk yaing'ono. Monga kulumbilira zinthu zina posakhala Mulungu wapamwamba; Monga ngati kuilumbilira nyumba ya Mulungu Kaaba, Aneneri, kukhulupirika, moyo wa munthu wina wake ndi zina zotero, Monga adanenera Mtumiki-madalitso ndi mtendere zipite kwa iye:

«مَنْ حَلَفَ بِغَيرِ اللهِ فَقَدْ كَفَرَ أَو أَشرَكَ».

“Munthu amene angazilumbire zinthu zina posakhala Mulungu ndiye kuti wakanila kapena wapanga shirk wamphatikiza Mulungu ndi zinthu zina)”2.

Ndipo ikhoza kukhala shirk yaikulu potengera zomwe zili mu mtima mwa mwini wake. Ngati mu mtima mwa omulumbira Mneneri kapena Sheikh wina wake muli chikhulupiliro chakuti iye ali ngati Mulungu, kapena kuti amayenera kupemphedwa posakhala Mulungu, kapena kuti ali ndi mphamvu yoyendetsa chilengedwe; ndiye kuti kulumbirako kukhala shirk yaikulu, Koma ngati ochilumbira china chosakhala Mulungu alibe cholinga chimenecho, koma zangochitika kuti wayankhula chifukwa wazolowera kutero; ndiye kuti ikhala shirk yaying'ono, Ndipo zimenezi zimachitika kwambiri m'madera ena, choncho ndi kofunika kukhala ozindikira za zimenezi, ndiponso kuchenjeza anthu za izo, posamalira chikhulupiliro cha umodzi wa Mulungu ndikuchiteteza.

3- Shirk yobisika:

Kumeneko ndiko kudzionetsera komwe kumakhala m'mitima; Monga amene amapemphera kapena amawelenga (Quran) kuti adzionetsere kwa anthu, kapena amapanga tasibeeh kuti amuyamikire, kapena amapereka sadaka kuti amutamande, Ndipo zimenezi zimaononga ntchito imene adadzionetsera nayo, osati ntchito zake zina zonse zomwe adazichita modzipereka kwa Mulungu wapamwamba.

Adanena (Mtumiki) -madalitso ndi mtendere zipite kwa iye:

«الشِّرْكُ فِي هَذِهِ الْأُمَّةِ أَخْفَى مِنْ دَبِيبِ النَّمْلَةِ السَّودَاءِ عَلَى الصَّفَاةِ السَّودَاءِ فِي ظُلْمَةِ اللَّيْلِ، وَكَفَّارَتُهُ أَنْ يَقُولَ: "اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ أَنْ أُشْرِكَ بِكَ شَيْئًا وَأَنَا أَعْلَمُ، وَأَسْتَغْفِرُكَ مِنَ الذَّنْبِ الَّذِي لَا أَعْلَمُ».

“Shirk mu mtundu uno ndi yobisika kwambiri kuposa nyerere yakuda yomwe yabisala pamwala wakuda pa nthawi yomwe kuli mdima wa usiku, ndipo chiwombolo chake n’chakuti anene kuti: "Allahumma 'inni 'audhu bika' an 'ushrika bika shay'an waana 'aelamu, wa'astaghfiruka min aldhanbi alladhi la 'aelamu". Tanthauzo lake: Ambuye Mulungu ndikuzitchinjiriza mwa inu kuti ndisakuphatikizeni ndi kena kalikonse kumachita kuti ine ndikuziwa, komanso ndikupempha chikhululuko ku zochimwa zomwe ndapanga ndisakuziwa»3."

Mitundu ya Kusakhulupirira:

Mtundu Oyamba: Kusakhulupirira Kwakukulu:

Ndipo ndikomwe kumachititsa kukhala muyaya ku Moto, ndipo kuli mitundu isanu:

1- Kusakhulupilira kotsutsa:

Ndiko kukhulupirira kunama kwa Atumiki, Ndipo izi ndi zochepa kwa osakhulupirira; chifukwa Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka adawalimbikitsa Atumiki ake ndi zitsonyezo zoonekera, Koma mkhalidwe wa anthu okanira awa ndi monga momwe Mulungu adawasimbira:

﴿‌وَجَحَدُوا ‌بِهَا ‌وَاسْتَيْقَنَتْهَا أَنْفُسُهُمْ ظُلْمًا وَعُلُوًّا...﴾

Ndipo adazitsutsa (zisonyezozo) mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Mulungu)... [Al-Nahl:14].

2- Kukanira pokana ndikuzitukumula:

Chitsanzo cha ichi ndi kusakhulupirira kwa Ibilisi, pakuti iye sadalikanire lamulo la M kapena kulitsutsa, koma adangolikana ndi kudzitukumula. Mulungu wapamwamba wati:

﴿وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰ وَٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ 34﴾

{Ndipo (akumbutse anthu ako nkhani iyi) pamene tidawauza Angelo: “Mgwadireni Adam.” Onse adamugwadira kupatula Iblisi (Satana); anakana nadzitukumula. Tero adali m’modzi mwa osakhulupirira}. [Al-Baqarah:34].

3- Kukanira kofulatira:

Ndipo zimenezo ndizoti munthu amafulatira kutsatira choonadi ndi makutu ake ndi mtima wake, osachitembenukira, ndiponso osachisamala. Mulungu wapamwamba wati:

 

﴿وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ ثُمَّ أَعۡرَضَ عَنۡهَآۚ إِنَّا مِنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ مُنتَقِمُونَ22﴾

{Kodi ndani wachinyengo kwambiri, woposa yemwe akukumbutsidwa Ayah za Mbuye wake, kenako nkuzikana? Ndithu Ife, tidzawabwezera zoipa anthu oipa}. [Al-Sajdah:22].

Pamene kufulatira kwa mbali ina (yachipembedzo osati chonde); ndiye kunyozera osati kukanira; monga amene amanyalanyaza kuphunzira zina mwa zinthu zokakamizidwa kuzichita mchipembedzo; monga malamulo a kusala kapena Hajj ndi zina zotero.

4- Kukanira kokaikira:

Ndipo kumeneko ndiko kuzengeleza, osachitsimikiza choonadi, koma kumachikaikira, monga mmene zilili m’mau ake Mulungu wapamwamba:

﴿وَدَخَلَ جَنَّتَهُ وَهُوَ ظَالِمٌ لِنَفْسِهِ قَالَ مَا أَظُنُّ أَنْ تَبِيدَ هَذِهِ أَبَدًا 35 وَمَا أَظُنُّ السَّاعَةَ قَائِمَةً وَلَئِنْ رُدِدْتُ إِلَى رَبِّي لَأَجِدَنَّ خَيْرًا مِنْهَا مُنْقَلَبًا 36﴾

Ndipo adalowa m’munda mwake uku akudzichitira yekha zoipa. Adati: “Sindiganiza ngakhale mpang’ono pomwe kuti munda uwu udzaonongeka.”

“Ndiponso sindiganiza kuti Qiyâma chimaliziro idzachitikadi. Ngati itapezekadi Kiyamayo, ine nkubwezedwa kwa Mbuye wanga, ndithu ndikapeza malo abwino wobwererako kuposa awa. Monga momwe ndapezera mwayi kuno, ukonso ndikapeza, ngati Kiyamayo ilikodi.”

[Al-Kahf: 35-36].

5- Kukanira kwa umthira kuwiri:

Ndiko kuonetsela ndi lilime lake chikhulupiliro, ndikubisa ndi mtima wake kukanira, Mulungu wapamwamba wati:

﴿وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَقُولُ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَبِٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَمَا هُم بِمُؤۡمِنِينَ 8﴾

{Pakati pa anthu alipo anthu achinyengo amene akunena: “Takhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chimaliziro,” pomwe iwo sali okhulupilira}.

[Al-Baqarah:8].

Ndipo iyi ndiyo mitundu ya kukanira kwakukulu otulutsa munthu m'Chisilamu.

Mtundu wachiwiri: Kusakhulupilira kwakung'ono:

Ndipo mtundu uwu siuchititsa kukhala kwamuyaya m'moto, Izo ndi zomwe zili mu Quran ndi chiphunzitso cha Mtumiki ponena kuti kumeneko ndikukanira posagwiritsa ntchito zizindikiro zomwe zingasonyeze kuti zikukamba zinthu zapadera,koma adagwiritsa zipangizo zakalembedwe zosonyeza kukamba kalikonse kokhuza kukanira. Zitsanzo zake zilipo zochuluka, mwa izo: Nkhani ikuchokera kwa Abu Hurairah-Mulungu asangalasidwe naye, adati: Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-amene adati:

«اثْنَتَانِ فِي النَّاسِ هُمَا بِهِمْ كُفْرٌ: الطَّعْنُ فِي النَّسَبِ، وَالنِّيَاحَةُ عَلَى المَيِّتِ».

"«Pali zinthu ziwiri mwa anthu zimene zili gulu la kukanira: kunyozana kamba ka fuko, ndiponso kulira maliro mwa mokumba»4."

2) Kukhulupilira mwa angelo

ndipo iwo ndi zolengedwa zobisika, Mulungu wapamwamba adawalenga kuchokera ku kuwala, Ndipo iwo amapembedza Mulungu wapamwamba, Ndipo alibe kena kalokonse kokhuzana ndi Umbuye kapena Umulungu, Ndipo iwo samapandukira Mulungu pa zimene wawalamula, Amachita zimene amalamulidwa, Ndipo iwo ndi ochuluka kwambiri, palibe amene angakwanitse kuwawerenga kupatula Mulungu yekha.

Ndipo kukhulupilira mwa angelo kumatenga mfundo zinayi:

1- Kukhulupilira kuti alipo.

2- Kukhulupilira mwa omwe mayina awo timawadziwa; monga: Gabulieli, Mikaeli, Israfili ndi ena. Ndipo amene sitidziwa maina awo timawakhulupilira mchigulugulu.

3- Kukhulupilira mbiri zawo zomwe tazidziwa, zomwe zabwela m'buku la Mulungu ndi mu sunnah za Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye. Monga mbiri za Gabulieli, Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-adanena kuti adamuona m'maonekedwe ake amene Mulungu adamulengera, ali ndi mapiko mazana asanu ndi limodzi, amene adatseka mlengalenga.

4- Kukhulupilira zochita zawo zomwe tazidziwa; monga kumuyeretsa kwawo Mulungu wapamwamba, ndi kumupembedza Iye usiku ndi usana popanda kutopa kapena kufooka.

Mwachitsanzo: Gablieli: ndi amene adamupatsa udindo ofikitsa mau a Mulungu kwa Atumiki.

Israfili: anapatsidwa udindo woliza Lipenga tsiku lotsiriza.

Ndipo mngelo wa Imfa: adapatsidwa ntchito yochotsa mizimu ya akapolo nthawi yomwalira yakwanira.

Ndipo Malik: msungi wa Moto, ndipo Ridwan ndimsungi wa Jannah, ndi ena.

3) Kukhulupilira mabuku:

Ndipo tanthauzo la mabukuwa ndi mabuku a Mulungu amene wapamwamba adawavumbulutsa kwa Atumiki ake, Kukhala chiongoko ndi chifundo kwa anthu onse, kuti afike ku chisangalalo cha padziko lapansi ndi tsiku lomariza.

Ndipo kukhulupilira mabuku kumatenga mfundo zinayi:

1- Kukhulupilira kuti adavumbulutsidwa kuchokera kwa Mulungu mwachoonadi.

2- Kukhulupilira mabuku omwe tikudziwa maina ake; monga Qur’an yomwe idavumbulutsidwa kwa Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye. Komanso Torah yomwe idavumbulutsidwa kwa Mussa-mtendere wa Mulungu ukhale pa iye, Komanso Uthengau wabwino womwe unavumbulutsidwa kwa Issah-mtendere ukhale kwa iye, Ndi Zaburi yomwe adapatsidwa Daud-mtendere ukhale kwa iye.

Tsono mabuku omwe sitikudziwa mayina awo, timawakhulupirira mchigulugulu.

3- Kuvomereza nkhani zake; monga nkhani za mu Qur’an, ndi nkhani za m’mabuku akale zomwe sizidasokonezedwe.

4- Kugwiritsa ntchito malamulo ake omwe sanachotsedwe, ndikukhutira nawo komanso kuwagonjera, khaya tazindikira zolinga zake kapena sitinazindikire. Ndipo mabuku onse akale adachosedwa malamulo ake ndi buku lolemekezeka la Quran, Motero sikuloledwa kugwiritsa ntchito lamulo lililonse la m'mabuku akale, pokhapokha lomwe lili lolondola, ndipo Qur'an yolemekezeka kapena Sunnah za mtumiki zalivomereza.

4) Kukhulupilira mwa Atumiki-mtendere ukhale pa iwo:

Atumiki: Ndi mau ochuluka a Mtumiki; ndipo iye ndi munthu amene adavumbulutsidwira lamulo ndipo adalamulidwa kulifalitsa, Oyamba mwa iwo ndi Nowa - mtendere ukhale pa iye, ndipo otsiriza mwa iwo ndi Muhammad - mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye, Ndipo iwo ndi anthu olengedwa, Alibe mbiri iliyonse ya umbuye ngakhale ya umulungu.

Ndipo kukhulupilira mwa Atumiki kumatenga:

1- Kukhulupilira kuti uthenga wawo ndi owona ochokera kwa Mulungu. Munthu amene angakanire uthenga wa m'modzi wa iwo, ndiye kuti wakanira onse.

2- Kukhulupilira mwa amene tawadziwa ndi mayina awo, monga: Muhammad, Abraham, Mose, Yesu, ndi Nowa, mtendere ukhale pa iwo. Ndipo iwo ndi atumiki okhala ndi chitsimikizo chachikulu.

Koma za amene sitikudziwa mayina awo; timawakhulupilira mchigulugulu, Mulungu wapamwamba adayankhula kuti:

﴿‌وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا رُسُلٗا مِّن قَبۡلِكَ مِنۡهُم مَّن قَصَصۡنَا عَلَيۡكَ وَمِنۡهُم مَّن لَّمۡ نَقۡصُصۡ عَلَيۡكَ...﴾

{Ndipo dithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira nkhani zawo ndi maina awo. Ena mwa iwo sitidakusimbire...}

[Ghafir: 78].

3- Kuvomereza nkhani zawo zotsimikizika-mtendere ukhale pa iwo.

4- Kugwiritsa ntchito malamulo a yemwe anatumidwa kwa ife mwa iwo, ndipo ndiye otsiriza wawo Muhammad-mtendere ndi madalitso zipite kwa iye.

5) Kukhulupilira za tsiku lomariza:

Ndilo tsiku lotsiriza limene anthu adzaukitsidwe kuti akawerengedwe ntchito zawo ndi kulipidwa, Ndipo latchedwa ndi dzina limeneli chifukwa kulibe tsiku lina pambuyo pake, tero anthu a ku minda ya mtendere adzakhanzikika m'malo mwawo, komanso a ku Moto adzakhanzikika m'malo mwawo.

Ndipo kukhulupilira za tsiku lomariza kumatenga mfundo zitatu:

A- Kukhulupilira za kuukitsidwa:

Ndiko kuukitsa akufa pamene lipenga lidzaimbidwa kachiwiri, Anthu adzaimirira pamaso pa Mbuye wa zolengedwa zonse, ali opanda nsapato kumapazi, ali maliseche wopanda chovala, ndiponso osachitidwa mdulidwe, Mulungu wapamwamba adayankhula kuti:

﴿كَمَا بَدَأْنَا أَوَّلَ خَلْقٍ نُعِيدُهُ ‌وَعْدًا ‌عَلَيْنَا إِنَّا كُنَّا فَاعِلِينَ 104﴾

{Monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pa zomwe adali kuchita ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu Ife ndi Ochita zomwe tikunena}. [Al-Anbiya:104].

B- Kukhulupilira za chiwerengero ndi malipiro:

Pomwe kapolo adzawerengesedwa pa ntchito yake, ndipo adzalipidwa pa iyo,Mulungu wapamwamba adanena kuti:

﴿إِنَّ إِلَيۡنَآ إِيَابَهُمۡ 25 ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا حِسَابَهُم 26﴾

{Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi(25)

Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife}. [Al-Ghashiya:25-26].

C- Kukhulupilira zoti kuli Minda ya mtendere ndi Moto:

Ndipo kuti zonse ziwirizi ndi malo omalizira amuyaya a zolengedwa; Tsono Jannah ndiyo malo achisangalalo amene Mulungu wapamwamba wawakonzera anthu okhulupirira oopa Mulungu, omwe adali kumvera Mulungu ndi Mtumiki wake-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye. M'menemo muli zomwe maso sanayambe aona, komanso makutu sanayambe atamva, komanso sizinayambe zafika m'maganizo a munthu.

Tsono Moto; ndi malo a chilango, umene Mulungu wapamwamba wakonzera anthu osakhulupilira amene adakanira Mulungu ndi kusamvera Atumiki ake. M'menemo muli mitundu ya mazunzo ndi zilango zomwe sizingathe kubwera m’maganizo.

6) Kukhulupilira za Chikonzero zabwino ndi zoipa zake:

Ndipo tanthauzo la Chikonzero: Chikonzero cha Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka pa zonse zomwe zidzachitike, malinga ndi kudziwa kwake koyambirira, komanso monga m'mene nzeru zake zidafunira.

Ndipo kukhulupilira za chikonzero kukutenga zinthu zinayi:

1- Kuzindikira: kumeneku ndiko kukhulupilira za kuzindikira kwa Mulungu wapamwamba, ndi kuti amadziwa zonse zomwe zidalipo kale, ndi zomwe zidzachitike mtsogolo, ndi mmene zidzakhalire, zonse mwakamodzi ndi motambasula, kuyambira kalekale mpaka muyaya. Ndipo Iye oyeretsedwa, ndi wodziwa za zomwe sizidakhalepo, kuti zikadakhala, zikadakhala bwanji, Monga adanenera Mulungu oyeretsedwa kuti:

﴿‌وَلَوۡ رُدُّواْ لَعَادُواْ لِمَا نُهُواْ عَنۡهُ ...﴾

{Ndipo akadabwezedwa akadakabwerezanso kuchita zimene adaletsedwa..}.

[Surat Al-An'am: 28].

2- Kulemba: Ndiko kuti ndithu Mulungu wapamwamba adalemba chikonzero cha chinthu chilichonse kufikira tsiku lotsiriza, Monga adanenera Mulungu wapamwamba:

﴿أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّ ذَٰلِكَ فِي كِتَٰبٍۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ﴾

{Kodi sudziwa kuti Mulungu akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu zonsezo zili m’kaundula wake, ndithu kudziwika kwa zimenezo kwa Allah nzosavuta}. [Al-Hajj: 70].

3- Chifuniro: ndiko kukhulupilira kuti sichichitika chilichonse mu chilengedwe ichi pokhapokha chomwe adachifuna Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka, Mulungu wapamwamba akunena kuti:

﴿وَرَبُّكَ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُ وَيَخۡتَارُ ...﴾

{Ndipo Mbuye wako amalenga chimene wafuna ndi kuchisankha ...} [Al-Qasas: 68]. Ndipo munthu ali ndi Chifuniro chimene sichituluka kunja kwa Chifuniro cha Mulungu, monga Mulungu wapamwamba wanenera:

﴿وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ 29﴾

{Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Mulungu Mbuye wa zolengedwa zonse}. [Surat Al-Takwir: 29].

4- Kulenga: Ndiko kukhulupilira kuti Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka adalenga zolengedwa, ntchito zawo ndi zochita zawo zabwino ndi zoipa. Mulungu wapamwamba akuyankhula kuti:

﴿ٱللَّهُ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ وَكِيلٞ﴾

{Mulungu ndiye Mlengi wa chilichonse, ndipo iye ndi Myang’aniri wa chilichonse}. [Al-Zumar:62].

Ndipo magawo amenewa asonkhanitsidwa m'ndime iyi ya ndakatulo:

Kudziwa, kulemba kwa Mbuye wathu, kufuna kwake, ndi kulenga kwake, komwe ndiko kupezetsa ndi kupanga.

Mutu wachitatu: Kupanga ubwino:

Kupanga bwino: kuli ndi nsanamira imodzi; kumpembedza Al ngati ukumuona, ndipo ngati siukumuona, ndithu Iye akukuona.

Ndiko kuti: munthu achite zomwe Mulungu adamulamulira kuti ampembedze nazo ngati kuti waima pamaso pa Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka, Ndipo zimenezo zimafuna kumuopa kwathunthu ndiponso kubwerera kwa Iye woyeretsedwa. Komanso zimafunika kuti mapemphero azichitidwa mogwirizana ndi zochita za Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye.

Ndipo kuchita zabwino kuli ndi misinkhu iwiri, ndipo ochita zabwino ali pa masitepe awiri osiyana:

Sitepe yoyamba: ndipo ndi yapamwamba kwambiri, ndiyo sitepe ya kupenya; Kumeneko ndiko kuti kapolo azigwira ntchito zake ngati kuti akumuona Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka ndi mtima wake, ndipo mtima umayamba kuwunikiridwa ndi chikhulupiriro, kufikira kuti zinthu zobisika zimakhala ngati zooneka ndi maso.

Sitepe yachiwirii: ndisitepe yakuyeretsa ndi kukumbukira Mulungu, uku ndiko kuti kapolo ayenera kugwira ntchito akukumbukira kuti Mulungu akumuona ndiponso akudziwa za iye, ndipo ngati atakumbukira izi, ndiye kuti azagwira ntchito momuyeretsera Mulungu wapamwamba.

Nkhani yachinayi: Chidule cha maziko a ahali sunnah wal jamaa:

Choyamba: kutsatila zomwe zabwera mu Quran ndi mu zochita za Mtumiki zobisika ndi zoonekera. Komanso osatsogoza mau a munthu aliyense kuposa mau a Mulungu wamphamvu zonse komanso wolemekezeka, komanso mau a mtumiki wa Mulungu-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye.

Chachiwiri: Kuyera kwa mitima yawo ndi malirime awo pa zokhuzana ndi Maswahaba a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye, ndipo amaona kuti Khalifa pambuyo pa Mtumiki wa Mulungu-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye ndi Abubakar, kenako Umar, kenako Uthmaan, kenako Ali-Mulungu asangalasidwe nawo onsewo.

Chachitatu: Kuwakonda akubanja kwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- ndi kuwapanga kukhala abwenzi; ndipo akubanja kwake ake omwe ali olungama okha mwa iwo.

Chachinayi: Osaukira atsogoleri ndi olamulira, ngakhale atapondereza, koma kumawapemphera kulungama ndi umoyo wabwino, ndipo asatembeleredwe. Ndipo kuwamvera iwo ndi mbali ya kumumvera Mulungu ndipo ndikokakamizidwa, bola ngati sakulamula za kusamvera. Koma ngati atalamula za kusamvera ndithudi iwo sayenera kumveredwa pa lamulo limenelo. Ndipo kumatsalira kuwamvera pa zabwino mu zinthu zina.

Chachisanu: Kuvomereza za zozizwitsa za mawali; Ndipo izi ndizomwe Mulungu amazichititsa pa manja awo mu zinthu zosiyana ndi zomwe anthu anazolowera.

Chachisanu ndi chimodzi: Samawaweruza anthu omwe amayang'ana ku qibla (popemphera) kuti ndi makafiri chifukwa chongochita machimo wamba ngakhale machimo akulu akulu, Monga momwe amachitira Akhawariji, koma ubale wachikhulupiliro umakhalabe okhazikika ngakhale pali machimo, ndipo amanena za ochimwa kuti: ndi okhulupilira chifukwa cha chikhulupiliro chake, komanso onyoza chifukwa cha tchimo lake lalikulu.

Gawo lachiwiri: Zokhudzana ndi mapemphero

Mutu Woyamba: Kudziyeretsa:

Tanthauzo la Twahara pa chiyankhulo ndi : ukhondo ndi kuziyeretsa ku zonyansa zoonekera ndi zosaonekera.

Tsono pa chilamulo: ndiko kuchotsa uve ndi nyasi Ndipo kuziyeretsa ndi makiyi a mapemphero, Pa chifukwa chimenechi, kuphunzira zimenezi ndi imodzi mwa nkhani zofunika kwambiri zachipembedzo, zimene Msilamu aliyense ayenera kuziphunzira ndi kuzisamalira.

CHOYAMBA: MAGAWO A MADZI:

1- Madzi oyera; awa ndimadzi omwe ali ovomerezeka kudziyeretsera, Khaya akadali pa kalengedwe kake; monga madzi a mvula, a mmitsinje, kapena a mnyanja, kapena asakanikirana ndi chinthu choyera chosawapotsa madzio (kuchuluka kwake), ndiponso chosalanda dzina lake (loti ndimadzi).

2- Madzi oti ali ndi nyasi; ndipo sayenera kuwagwiritsa ntchito, ndipo samachotsa uve, komanso samachotsa nyasi awa ndimadzi omwe mtundu wake, kapena fungo lake, kapena kakomedwe kake kasintha chifukwa cha najisi.

CHACHIWIRI: NYASI

Najisi: ndi nyansi zapadera, zomwe zimamuletsa munthu kuti aimikemapemphero ; monga mkodzo, chimbudzi, magazi ndi zina zotero, ndipo zimakhala pathupi, pamalo, ndiponso pachovala.

Ndipo maziko a zinthu ndikuti zili zololedwa ndi zoyera, choncho amene anena kuti chinthu chinachake ndinajisi, akuyenela kupeleka umboni. Ndipo mu najisi simulowa zinthu izi: makholodo, thukuta la munthu, ndi thukuta la bulu, koma ndizoyela ngakhale zitaoneka ngati zonyansa Nyasi iliyonse ndi yonyansa, koma osati chonyansa chilichonse ndi nyansi.

Ndipo nyasi ili ndi masitepe atatu:

Yoyamba: Nyasi yaikulu;

Monga: Nyansi ya pamene panyambita galu, Ndipo njira yopayeretsera: ndiyakuti patsukidwe kasanu ni kawili, nthawi yoyamba ndi mchenga.

Yachiwiri: Nyansi yopepuka:

Monga mkodzo wa mwana wamwamuna wakhanda pamene wagwera pa chovala kapena china chofanana nacho. Tsono njira yopayeretsera ndiyo kuwazira madzi mpakana afike ponseponse, ndipo palibe chifukwa chopukutira kapena kufinya.

Yachitatu: Nyansi yapakatikati:

monga mkodzo wa munthu ndi chimbudzi chake, ndi zonyansa zambiri, zikagwera pansi kapena pa chovala ndi zina zotero. Njira yoyeretsera ndiyo kuchotsa nyansi yeniyeniyo ngati ilipo, komanso kuyeretsa pomwe inali ndi madzi kapena ndi zinthu zina zoyeretsera.

Tsono mwa zomwe umboni ulipo zokhuza nyansi ndi:

1- Mkodzo wa munthu ndi chimbudzi chake.

2- Al-Madhiyyu (Madzi onanda otuluka poganiza zogonana) ndi Al-Wadiyyu (Madzi oyera otuluka munthu akatha kukodza)5.

3- Ndowe za chomwe sichimadyedwa nyama yake.

4- Magazi a matenda a kumwezi ndi a uchembere.

5- Malovu a galu.

6- Chakufa chokha, kupatulapo:

a- Munthu akamwalira.

B- Nsomba ndi dzombe zomwe zafa zokha.

C- Tizilombo takufa tokha tomwe tilibe magazi omachucha, monga ntchentche, nyerere, njuchi, ndi zina zotere.

d- Fupa la nyama yakufa yokha, nyanga yake, chikhadabo chake, tsitsi lake ndi nthenga zake.

Kayeretsedwe ka nyansi kali motere:

1- Kuyeretsa ndi madzi, ndipo ndiwo maziko poyeretsa zonyasa, kotero kuti asasiyidwe ndikuyeretsa ndi china.

2-Zomwe lamulo limanena pa njira yoyeretsera zinthu zonyansa kapenanso zomwe zakhudzidwa ndi zonyansa:

A- Chikopa cha nyama yakufa yokha chimayera pokhula.

b- Kayeretsedwe ka chiwiya ngati chitanyambitidwa ndi galu; chitsukidwe kasanu ndi kawili; koyambilira ndi mchenga.

C- Kuyeretsa chovala ngati atagwerapo magazi a kumwezi; kutikitapo, kenako kufinyapo uku ukuthira madzi, kenako kusukuluzapo. Ndipo ngati pambuyo pochita izi ndikutsalapo banga, palibe vuto.

D- Kuyeretsa nsonga ya chovala cha mkazi (yomwe ikukhwekhwerezeka pa nthaka ya nyansi) ndinthaka yoyera yomwe ingagunde pambuyo pake.

E- Kuyeretsa chovala ku mkodzo wa mwana wamwamuna woyamwa; pongowazirapo madzi, koma pamene pagwera mkodzo wa mwana wamkazi pachapidwe.

F- Kuyeretsa chovala ku madhiy; powaza madzi pamalopo.

G- Kuyeretsa pansi pa nsapato, poyikhwekhwereza nsapatoyo pa nthaka yoyera.

H- Kuyeretsa nthaka ku zonyansa; pothira ndowa ya madzi pamalopo, kapena kupasiya kuti paume ndi dzuwa kapena mphepo. Ndipo ngati chizindikiro cha zonyansa chachoka, ndekuti nthakayo yayera.

CHACHITATU: ZIMENE ZILI ZOLETSEDWA KUCHITA KWA MUNTHU AMENE ALI NDI UVE:

Zinthu zomwe ndizoletsedwa kwa munthu yemwe ali ndi uve waung'ono kapena waukulu:

1- Kupemphera mapemphero okakamizidwa kapena osakakamizidwa; Chifukwa cha nkhani yomwe yalandiridwa kuchokera kwa Abdul-Allah mwana wa Umar-Mulungu asangalasidwe nawo onse awiri, Mneneri -mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-adanena kuti:

«لَا يَقْبَلُ اللَّهُ صَلَاةً بِغَيْرِ طُهُورٍ».

"Mulungu salandira mapemphero popanda kudziyeresa)6.

2- Kugwira buku la Quran; Malinga ndi zomwe zidalembedwa m'kalata yomwe Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-adamulembera Amr bin Hazm, momwe mudali mau oti:

«لَا يَمَسُّ الْقُرْآنَ إِلَّا طَاهِرٌ».

''Asagwire Qur'an kupatula munthu oyeresedwa''7.

3- Kuzungulira nyumba Mulungu (Kaaba); Kamba ka Mau ake-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-:

«الطَّوَافُ بِالْبَيْتِ صَلَاةٌ، إِلَّا أَنَّ اللَّهَ أَبَاحَ فِيهِ الْكَلَامَ».

«Kuzungulira Nyumba ya Kaaba ndiswala, kungoti Allah waloleza kulankhula pozungulirapo»8. Ndipo Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- adapanga udhu chifukwa cha kuzungulira Kaaba. Ndipo zidatsimikizika kuchokera kwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kuti adaletsa akazi amene akudwala kumwezi kuzungulira nyumba ya Allah kufikira atayera.

Tsono zinthu zimene zimaletsedwa makamaka kwa munthu amene ali ndi uve waukulu ndi izi:

1- Kuwerenga Qur'an; Chifukwa cha nkhani yochokera kwa Ali-Mulungu asangalasidwe naye: "Palibe chomwe chinkamuletsa iye-kutanthauza Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye- kuwerenga buku la Quran, posakhala umve wa ukulu odza kamba kokhala limodzi ndi mkazi wake."9

2- Kukhala mu mzikiti popanda udhu; Malinga ndi kuyankhula kwake Allah wapamwamba:

﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَقۡرَبُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنتُمۡ سُكَٰرَىٰ حَتَّىٰ تَعۡلَمُواْ مَا تَقُولُونَ وَلَا جُنُبًا إِلَّا عَابِرِي سَبِيلٍ حَتَّىٰ تَغۡتَسِلُواْ...﴾

{E inu amene mwakhulupirira! Musaiyandikire Swala uku muli oledzera, mpaka mudziwe chimene mukunena; ngakhalenso pamene muli ndi janaba (musapemphere kufikira mutasamba) kupatula amene ali pa ulendo...} [Surat Al-Nisa:43].

Ndipo ngati munthu amene ali ndi umve waukulu apanga udhu, zikhala zololedwa kwa iye kukhala mu Mzikiti. Momwemonso, munthu amene ali ndi uve waukulu amaloledwa kudutsa mu Mzikiti, koma pongodutsa basi, popanda kukhalamo pansi.

CHACHINAYI: MIYAMBO YA NTHAWI YODZITHANDIZA KUCHIMBUZI:

Ndi chiphunzitso cha Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-kuti panthawi yodzithandiza ku chimbudzi munthu azichita izi:

1- Kukhala patali komanso kudzibisa kwa anthu pokhala pamalo achinsinsi (pochita chimbudzi).

2- Kunena pemphero lolowera ku chimbudzi,lomwe ndi ili:

«اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ مِنَ الْخُبْثِ وَالْخَبَائِثِ».

"Allahumma inni au'dhu bika minal-khubuthi wal-khabaithi" O Allah! Ndithudi ine ndikubisala mwa Inu ku zonyansa (Asatana) zachimuna ndi zachikazi.10.

Zinthu zimene zili zokakamiza pa nthawi yodzithandiza ndi izi:

1- Kudzitalikitsa ku mkodzo.

2- Kubisa umaliseche

Zinthu zoletsedwa pa nthawi yozithandiza:

1- Kulunjika ku Qiblah kapena kuifulatira.

2- Kudzithandiza m'njira za anthu ndi m'malo awo a pagulu.

3- Kukodza m'madzi osayenda.

Zimadedwa pa nthawi yozithandiza:

1- Kukhudza umaliseche wachimuna ndi dzanja lamanja podzithandiza.

2- Kudziyeretsa ndi madzi kapena mapepala ndi dzanja lamanja.

3- Nkodana kulankhula, makamaka potchula dzina la Allah wamphamvu zonse komanso wolemekezeka podzithandiza.

CHACHISANU: MALAMULO A KUDZISUKA NDI KUDZIPUKUTA:

AL-ISTINJA-U: Kumeneko ndiye kuchotsa chotsalira cha chotuluka m'njira ziwiri (yotulukita chimbuzi ndi yotulukita mkodzo) ndi madzi.

AL ISTIJMAR: Kumeneko ndiye kuchotsa chotsalira cha chotuluka m'njira ziwiri pogwiritsa ntchito zinthu zina osati madzi, monga miyala ndi zopukutira.

Malamulo a zinthu zodzipukutira (ukadzithandiza):

1- Chikhale chololedwa.

2- Chikhale chaukhondo.

3- Chikhale choti chingayeretse.

4- Chisakhale fupa kapena ndowe.

5- Asagwiritse ntchito chinthu cholemekezeka; monga mapepala omwe lalembedwamo dzina la Allah wamphamvu zonse komanso wolemekezeka.

Zimaloledwa kudziyeretsa pogwiritsa ntchito zodzipukutira zokha ndimalamulo awiri:

1- Chonyansa chisapitilire malo ake achizolowezi.

2- Kupukuta kukufunika kuchitidwe ndi miyala itatu yoyeretsa (kapena zodzipukutira zina zitatu), kapena kupitilira apo.

CHACHISANU NDI CHIMODZIMODZI: MALAMULO A UDHU:

Kuchita Udhu n'kofunikira pa mapemphero atatu:

1- Swala; kaya ndi yokakamiza kapena yosakakamizidwa.

2- Kugwira buku la Quran

3- Kuzungulira Kaaba.

Zofunikira kuti udhu ukhale wolondola:

1- Chisilamu

2- Nzeru.

3- Kuzindikira.

4- Chitsimikizo: malo ake ndi mu mtima, ndipo kuchiyankhula ndi bida, Stono aliyense wafuna kuchita udhu ndekuti watsimikiza. Koma kusambisa ziwalo za wudhu ndi cholinga chozizilitsa kapena kudziyeretsa chabe, kutero sikuchita wudhu.

5- Kukhalabe ndi cholinga chopanga udhu: kotero kuti asasimikize zosintha maganizo a udhu kufikira kutafika kumapeto kudziyeretsako.

6- Chisakhalepo chowononga udhu, kupatula munthu amene akudwala matenda okozakoza ndi mkazi amene akudwala matenda a kumwezi wosalekeza.

7- Kuyamba kaye wadzitsuka kapena kudzipukuta kwa yemwe watuluka kuchokera kwa iye mkodzo kapena chimbudzi.

8- Madzi akhale aukhondo ndi ololedwa.

9- Kuchotsa zinthu zoletsa madzi kufika pakhungu.

10- Kulowa kwa nthawi ya Swala kwa iye amene uve wake ndi wosalekeza.

Magawo a udhu okakamiza:

1-Kusambitsa nkhope: mulinso mmenemo kuchukucha mkamwa ndi kutsuka m'phuno.

2- Kusambitsa mikono iwiri kuphatikizapo zigonkhono.

3- Kupaka madzi pa mutu wonse, m'menemo muli kupakanso makutu awiri.

4- Kusambisa miyendo iwiri kuphatikizapo misomali iwiri.

5- Kulondoloza pakati pa ziwalo za udhu.

6- Kusatiza: Osadukiza nthawi yaitali pakati posambisa ziwalo.

KACHITIDWE KA UDHU:

1- Kuchita Bismillah.

2- Kusamba mmanja katatu.

3- Kusambitsa nkhope katatu, mulinso mmenemo kuchukucha mkamwa ndikutsuka mphuno.

4- Kusambitsa mikono iwiri kufikira mu zigonkhono katatu, kuyamba ndi mkono wamanja, kumalizira wamanzere.

5- Kupaka madzi pa mutu pamodzi ndi makutu awiri.

6- Kusambitsa miyendo iwiri kufikira mmisomali katatu, kuyamba ndi mwendo wamanja kumalizira wamanzere.

Zoononga udhu:

1- Zotuluka mu njira ziwiri, monga: mkodzo, kutulutsa mphweya ndi chimbuzi.

2- Chotuluka pathupi chochuluka nachikhala chaunve.

3- Kuchoka nzeru chifukwa cha kugona kapena zina.

4- Kugwira maliseche akutsogolo kapena akumbuyo ndi dzanja popanda chotchinga chilichonse.

5- Kudya nyama ya ngamila.

6- Kutuluka Chisilamu, Allah atitalikitse ife ndi asilamu ku zimenezo..

CHACHISANU NDI CHIWIRI: MALAMULO A KUPAKA MADZI PA KHUFFU NDI SOKOSI:

1- Khuffu: Ndi chinthu chilichonse chovala kumapazi chochokera ku chikopa ndi zofanana nacho (m'malo mwa sokosi).

2- Jaurab: Ndichilichonse chimene chimavalidwa mmapazi chochokera ku ubweya kapena thonje ndi zina zokhala ngati zimenezo (sokosi).

Malamulo a kupukuta pa zimenezo:

1- Zivalidwe pambuyo pokwaniritsa ukhondo.

2- Zibise mapazi awiri pamodzi ndi misomali.

3- Ziyenera kukhala zaukhondo.

4- Kupaka kumafunika kukhale mu nthawi yodziwika.

5- Kupakako kuyenera kuchitidwa pa udhu, osati pakusamba.

6- Khuffu ndi zina zofanana nazo ziyenera kukhala zololedwa (mubah). Ngati zili zolanda kapena za silika kwa amuna, sikololedwa kupaka pa izo, chifukwa chilolezo chopeputsira (rukhsa) sichipezeka kudzera m'chinthu choletsedwa (haramu).

Nthawi ya kupaka:

Kwa munthu wapakhomo: usana ndi usiku wake, ndipo kwa munthu wapaulendo: masiku atatu ndi usiku wake.

Kapakidwe kake:

Amanyowetsa dzanja ndi madzi, n’kupukuta pamwamba pa masokosi kapena ma Khuff, kuyambira pa zala za mmapazi mpaka ku mwendo, kamodzi.

Zoononga kupaka:

1- Kutha kwa nthawi yopakira

2- Kuvula masokosi onse awiri kapena imodzi.

3- Kupeza umve waukulu.

Lamulo lakupaka pa makhuffu:

Ichi ndi chilolezo, ndipo kuchita chilolezocho ndikwabwino kuposa kuvula masokosi ndi kutsuka mapazi; potsatira chilolezo cha Allah Wamphamvu zonse komanso Wolemekezeka, komanso potsanzira Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- ndi kusiyana kachitidwe ndi anthu opeka zinthu mu chipembedzo.

3- Kupaka madzi pa zikhakha, mabandeji ndi mapulasitala:

Zikhakha ndizomwe zimamangidwa pa mafupa othyoka; monga jipsamu kapena timitengo ndi zina zofananira nazo.

Bandeji: Ndichilichonse chimene chimamangidwa pachilonda, pabala kapena popsa ndi Moto; chochokela ku nsalu ndi zina zofanana nazo.

Pulasitala: Ndichomwe amamata pazilonda kapena zithupsa pochiritsa.

Lamulo lopaka pezimenezo:

Ndizololedwa: pakafunika kuti zikhalebe, ndi lamulo loti zisapitirire malo ofunikirawo.

Ndizosaloledwa: ngati kufunikira kwake kwatha, kapena kuvula kwake sikubweretsa zokhoma kapena vuto lililonse.

Kapakidwe kake pa izo:

Atsuke malo omwe azungulira chopakacho, kenako apake madzi pamwamba pake mbali zake zonse. Ndipo asapake komwe kwaonjezereka (kupotsa malo omwe ali vutowo) chikakhala chiwalo chosambitsa pochita udhu.

CHACHISANU NDI CHITATU: MALAMULO A TAYAMMAM:

Tayammamu: kumeneko ndiye kupukuta nkhope ndi manja pogwiritsa ntchito dothi la pamwamba pa nthaka, ndi cholinga choziyeretsa, m'njira yapadera.

Lamulo lake:

Ndikokakamizidwa kupanga Tayammamu m'malo mwa udhu ndi kusamba, pamene madzi asowa kapena akalephera kuwagwiritsa ntchito.

Cholinga cholamulila Tayammamu:

Tayammamu ndi chimodzi mwa zinthu zopezeka mu mpimgo wa Muhammad yekha basi-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye. Ndipo m'mipingo yakale sizinali kudziwika, kupepusa kochokera kwa Allah pa mpingo uwu, ndi ubwino wake pa iwo.

Nthawi zomwe Tayammamu imalamulidwa:

1- Ngati madzi asowa, khaya munthuyo ali pamudzi kapena paulendo, ndipo wawasakasaka nkusawapeza.

2- Ngati ali ndi madzi amene akuwafuna kuti aziwamwa kapena kuphikira, moti atawagwiritsa ntchito podziyeretsa zingasokoneze zofunika zakezo, m’njira yoti akudziopera ludzu iye mwini, kapena wina aliyense, kaya ndi munthu kapena chinyama cholemekezeka.

3- Akaopa kuti kugwiritsa ntchito madzi kungampatse vuto m'thupi mwake chifukwa cha matenda ake, kapena kuti kungachedwetse kuchira.

4- Ngati atalephera kugwiritsa ntchito madzi chifukwa cha kudwala komwe saakukwanitsa nako kugwedezeka, ndekulibe kwa iye yemwe angampangitse udhu, ndewaopa kudutsa nthawi.

5- Ngati akuopa kuzizira pogwiritsa ntchito madzi, ndesadapeze chotenthetsera, achite Tayammamu ndikuswali.

KACHITIDWE KA TAYAMMAMU:

Amenye dothi ndi manja atasiyanitsa zala, kenako apake nkhope yake ndi mkati mwa zala, komanso apake pamwamba pa manja ake pogwiritsa ntchito zikhato zake, ndi kufalitsa kupaka madela onse a nkhope ndi pamwamba ponse pa manja.

ZOWONONGA TAYAMMAMU:

1- Kupezeka kwa madzi, ngati Tayammamu yachitidwa chifukwa cha kusowa madzio, kapena kukwanitsa kugwiritsa ntchito madzi, ngati tayammamu yachitika chifukwa chosatha kugwiritsa ntchito madziwo.

2- Imaonongeka ndi chilichonse mwa zinthu zoononga udhu, kapenanso ndi chilichonse chimene chimakakamiza munthu kusamba, monga janaba, matenda akumwezi, komanso matenda a uchembere.

Lamulo la munthu wolephera kugwiritsa ntchito madzi ndi Tayammamu:

Ngati palibe madzi ndi dothi, kapena ali pamkhalidwe woti sangakhudze khungu lake ndi madzi kapena dothi, ndiye apemphera monga momwe alili, popanda wudhu kapena tayammum; chifukwa Allah sapatsa munthu zolemera kuposa zomwe angathe. Ndipo ngati atapeza madzi ndi dothi pambuyo pake, kapena atakwanitsa kuzigwiritsa ntchito, sabwerezanso Swala imene wapempherayo, chifukwa wachita zimene walamulidwa. Malinga ndi Mau ake (Allah ) wapamwamba:

﴿...فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ مَا ٱسۡتَطَعۡتُمۡ...﴾

Choncho muopeni Allah mmene mungathere. [At-Taghabun:16] Ndi mawu ake (Mtumiki) -madalitso ndi mtendere zipite kwa iye oti:

«إِذَا أَمَرْتُكُمْ بِأَمْرٍ فَأْتُوا مِنْهُ مَا اسْتَطَعْتُمْ».

Ndikakulamulani kuchita chinthu, chitani monga momwe mungathere.11.

Phindu: Ngati munthu wachita Tayammamu chifukwa cha janaba, kenako n'kupeza madzi, asambe.

CHACHISANU NDI CHINAYI: MALAMULO A MSAMBO NDI MAGAZI A PAMBUYO POBEREKA

CHOYAMBA: MATENDA A MSAMBO:

Ndi magazi achilengedwe, otuluka mkati mwenimweni mwa chiberekero panthawi zodziwika. Ndipo nthawi zambiri amatuluka masiku asanu ndi limodzi kapena asanu ndi awiri mwezi uliwonse, ndipo akhoza kuwonjezereka kapena kuchepa. Mwezi wa mkazi umatalika ndi kufupika, malinga ndi mmene Allah wapamwamba adamulengera m'chibadwidwe chake.

Malamulo a mkazi amene ali pa msambo:

1. Mkazi yemwe akudwala matenda a msambo sapemphera komanso sasala, ndipo kupemphera kapena kusala kwake sikovomerezeka.

2- Mkazi yemwe ali ku msambo akuyenera kulipira kusala, koma osati kuswali, pamene wayeretsedwa ku msambo wake.

3- Saloledwa kuzungulira nyumba ya Kaaba, Ndipo asawerenge Qur'an, Komanso asakhale mu mzikiti. 4- Ndipo ndi koletsedwa kwa mwamuna wake kugonana naye mpaka matenda ake a msambo atatha kenako ndikusamba.

5- Ndizololedwa kwa mwamuna kusangalala ndi mkazi wake yemwe ali kumsambo popanda kuchita naye ukwati, monga kupyopyonana, kugwirana ndi zina zotero.

6- Sikuloledwa kwa mwamuna wake kumusudzula ukwati uku ali ku msambo.

Ndipo kuyera ndiko kuduka kwa mwazi, choncho mwazi ukaduka; ndiye kuti wayera, ndipo nthawi yake ya msambo yatha, motero ayenera kusamba, Kenako ayambirenso kuchita zimene analetsedwa chifukwa cha msambo.

Ndipo ngati apenya pambuyo pa kuyera kwake madzi otuwa kapena achikasu; asasamale zimenezo.

Chachiwiri: matenda a uchembere:

Awa ndimagazi amene chiberekero chimatulutsa pa nthawi yobereka komanso pambuyo pake, ndipo ndi magazi otsala amene anasungidwa pa nthawi ya mimba.

Ndipo matenda a uchembere ali ngati msambo pa zinthu zololedwa; monga kusangalala naye popanda kulowa m'maliseche.

Komanso pa zinthu zoletsedwa; monga kugonana, kusala ndi kupemphera, kupereka chilekano, kuzungulira nyumba ya Kaaba, kuwerenga Qur'an, ndi kukhala mu msikiti, Ndi kukakamizidwa kusamba pamene magazi ake atha, mofanana ndi mkazi amene akudwala msambo.

Ndipo akuyenera kulipira kusala osati Swala, choncho salipira Swala monga mkazi amene ali kumsambo.

Ndipo nthawi yake yochuluka ndi masiku 40, Ndipo magazi a pambuyo pobereka (nifasi) akasiya kutuluka masiku makumi anayi asanakwane, ndiye kuti nthawi ya nifasiyo yatha, choncho mayiyo ayenera kusamba, akatero atha kupemphera, ndiponso kuyambiranso zinthu zonse zimene analetsedwa chifukwa cha nifasiyo.

Mutu Wachiwiri: Swala:

CHOYAMBA: MALAMULO A ADHANA NDI IQAMA

Adhan idakhazikitsidwa m'chaka choyamba cha kusamuka kwa Mtumiki kuchokera ku Makka kupita ku Madina. Ndipo chifukwa chokhazikitsira adhan nchakuti: pamene kudavuta kwa iwo kudziwa nthawi, adakambirana zokhazikitsa chizindikiro chake. Ndipo Abdullah mwana wa Zaid - Allah asangalasidwe naye -adaonetsedwa Adhan kumaloto, ndipo Chibvumbulutso chinavomereza.

Ndipo Adhan ndi chidziwitso cha kulowa kwa nthawi ya Swala. Iqama:kumeneko ndiye kulengeza za kuima kuswali.

Adhan ndi Iqamah ndi chokakamizidwa pa gulu la amuna (Faradhwi Kifayah) pa ma swallah olamulidwa, Ndipo ziwirizi ndi zina mwa machitidwe aakulu a Chisilamu oonekera, choncho nkosaloledwa kuleka kuwachita.

Zoyenera za Adhan:

1- Wochita adhan azikhala mwamuna.

2- Adhan ichitidwe mwadongosolo.

3- Kutsatizanitsa Adhan.

4- Adhan ikhale pambuyo pa kulowa kwa nthawi, Ndipo kupatula pa zimenezi ndi: Adhan yoyamba ya Fajir ndi Jum'a

Ma Sunnah a Adhan:

1- Kuika zala zake ziwiri m'makutu mwake.

2- Kuchita adhan kumayambiliro kwa nthawi.

3- Kutembenukira kumanja poyankhula mau oti: -hayiyya ala as swalaah - ndi kumanzere poyankhula mau oti: hayiyya alal falah.

4- Kukhala ndi mawu abwino.

5- Azinena mawu a Adhan modekha, mosawakokomeza kapenanso kuwatalikitsa mopitilira muyeso.

6- Kuyima pa chiganizo chilichonse cha adhan yo.

7- Alunjike ku Qiblah panthawi ya Adhan.

Ndipo Adhaan ili ndi ziganizo khumi ndi zisanu, monga momwe Bilal (Allah asangalale naye) ankachitira pamaso pa Mtumiki wa Allah (mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye) nthawi zonse.

Mawu a Adhan:

(Allah akbar): kanayi.

(Ash-hadu an-laa ilaaha illa-Allah): kawiri.

(Ash-hadu Anna Muhammadan rasulu llah): kawiri.

(Hayya ala Swala): kawiri,

(Hayya alal falah): kawiri.

Kenako anene kuti: (Allah Akbar) kawiri.

Kenako amalizire ndi (La Ilaha Illa Allah): kamodzi.

Ndipo pa Fajir amawonjezera pambuyo pa Hayya ala al-Falah: (As Swalaatu khairun mina annaum - swala ndiyabwino kupotsa tulo) kawiri; Chifukwa ndi nthawi imene kawirikawiri anthu amagona.

Ndipo Iqamah ili ndi mawu khumi ndi limodzi (11), amaichita mwachangu, ndiko kuti: amaifulumizitsa; chifukwa cholinga ndikudziwitsa omwe alipo kale, choncho palibe chifukwa choichedwetsa.

Mawu ake ndi monga akubwera mmusimu:

(Allah akbar): kokwana kawiri.

(Ash-hadu an-laa ilaaha illaallah): Kamodzi.

(ash-hadu anna Muhammadan rasulu llah): kamodzi.

(Hayya 'alas-Swala): kamodzi.

(Hayya 'alal-Falah): kamodzi.

(Qad Qaamati Swalah): kawiri.

(Allah Akbar): kokwana kawiri.

(La Ilaha Illa Allah): kamodzi.

Ndisunnah kwa amene wamva adhan kuti abwereze zomwe muadh-dhin akuyankhula, kupatula pomwe wafika mau oti: “Hayya a'la s-swalath” ndi “Hayya a'la al-falah,” nthawi imeneyo ayankhule kuti: “La haula wala quwwata illaa billah”, Kenako amufunire zabwino Mtumiki -madalitso ndi mtendere zipite kwa iye-. Kenako pambuyo pake anene kuti:

«اللهمَّ رَبَّ هَذِهِ الدَّعْوَةِ التَّامَّةِ، وَالصَّلَاةِ القَائِمَةِ، آتِ مُحَمَّدًا الوَسِيلَةَ وَالفَضِيلَةَ، وَابْعَثْهُ مَقَامًا مَحْمُودًا الَّذِي وَعَدْتَهُ، إِنَّكَ لَا تُخْلِفُ الْمِيعَادَ».

"Allahumma rabba hadhihi da'awati-taammah, was-swalatu al-qaaimah, aati muhammadan al-wasilata wal-fadhwiilah, wabua'thuhu maqaman mahmudan alladhi wa'adtahu, innaka la tukhlifu al-mi'ad."12

Kenako anene kuti:

«رَضِيتُ بِاللَّهِ رَبًّا، وَبِالْإِسْلَامِ دِينًا، وَبِمُحَمَّدٍ ﷺ نَبِيًّا».

"Ndasangalala ndi Allah monga Ambuye, ndi Chisilamu monga chipembedzo, ndiponso ndi Muhammad (s.a.w) monga Mneneri."13

Ndikoletsedwa kutuluka mu msikiti pambuyo pa Adhan popanda chifukwa kapena cholinga chobwelera.

Ndipo pophatikiza maswala awiri, amapanga adhan imodzi, ndipo amapangira iqama swala iliyonse.

CHACHIWIRI: ULEMELERO WA SWALA NDI UBWINO WAKE:

Swallah ndi nsanamila yofunika kwambiri ya Chisilamu pambuyo pa Shahada ziwiri, Ndipo ilii ndi ulemelero wapadera, Kotero kuti Allah adaikhazikitsa kwa mtumiki wake-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-pa usiku wa MIRAJ ali kumwamba, Choncho, izi zikusonyeza kulemekezeka kwake, kutsimikizika kwa kukakamizidwa kwake, komanso ulemelero wake pamaso pa Allah wamphamvu zonse komanso wolemekezeka.

Ndipo kwadza mahadisi ambiri ofotokoza ubwino wake ndi kukakamizika kwake kwa munthu aliyense, Ndipo kukakamizidwa kwake ndi kodziwika kwambiri m'chipembedzo cha Chisilamu.

Ndipo ma umboni osonyeza kukakamizidwa kwake ndi kufunika kwake ndi ochuluka kuchokera m'buku la Allah ndi Sunnah, ndipo ena mwa iwo ndi:

1- Mau a Allah wapamwamba:

﴿...إِنَّ ٱلصَّلَوٰةَ كَانَتۡ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ كِتَٰبٗا مَّوۡقُوتٗا﴾

{Ndithudi, Swala ndi lamulo lokhala ndi nthawi kwa okhulupirira}. [Surat Al-Nisa:103]. Ndiko kuti: nchokakamizika munthawi zomwe adazilongosola mtumiki wa Allah mtendere ndi madalitso zipite kwa iye.

2- Komanso mau a Allah wapamwamba oti:

﴿وَمَا أُمِرُوا إِلَّا لِيَعْبُدُوا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ حُنَفَاءَ وَيُقِيمُوا الصَّلَاةَ...﴾

{Ndipo sadalamulidwe china koma kuti ampembedze Allah mmodzi yekha ndi kuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona ndi kusiya njira zonama ndi kuti ayimike Swala moyenera...} [Al-Bayyinah:5].

3- Ndi mau a Allah oti:

﴿فَإِنْ تَابُوا وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَآتَوُا الزَّكَاةَ فَإِخْوَانُكُمْ فِي الدِّينِ...﴾

{Koma ngati alapa nayamba kupemphera Swala ndikupereka chopereka (Zakat), ndiye kuti ndi abale anu pa chipembedzo...} [Surat Al-Tauba:11].

4- Nkhani ikuchokera kwa Jabir, Allah asangalasidwe naye-amene anena kuti Mtumiki wa Allah-mtendere ndi madalitso a Allah zipite kwa iye-adanena kuti:

«إِنَّ بَيْنَ الرَّجُلِ وَبَيْنَ الشِّرْكِ وَالْكُفْرِ تَرْكُ الصَّلَاةِ».

“Ndithudi, chomwe chili pakati pa munthu ndi machitidwe omphatikiza Allah ndi zinthu zina, komanso kusakhulupirira, ndiko kusiya Swala”14

5- Ndipo Hadisi idachokera kwa Buraidah - Allah asangalare naye - adati: adanena mtumiki wa Allah madalitso ndi mtendere zipite kwa iye anati:

«العَهْدُ الَّذِي بَيْنَنَا وَبَيْنَهُمُ الصَّلَاةُ، فَمَن تَرَكَهَا فَقَدْ كَفَرَ».

"Pngano lomwe lili pa pakati pathu ndi anthu okanila, ndi swala ndipo amene asiye swala ndiye kuti wakanila."15.

Ndipo maulama onse adagwirizana pa kukanira kwa munthu amene amakana chikakamizo chake, Koma amene angasiye (Swala) chifukwa cha ulesi ndi mphwayi, maganizo olondola kwambiri ndi akuti naye ndi wokanila, chifukwa cha Hadisi yolondola yomwe yatsogola, ndiponso chifukwa cha mgwirizano wa maswahaba pa nkhaniyi.

CHACHITATU: MALAMULO A SWALA:

1- Kulowa kwa nthawi yake:

- Malinga ndi Mau ake Allah wapamwamba oti:

﴿...إِنَّ ٱلصَّلَوٰةَ كَانَتۡ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ كِتَٰبٗا مَّوۡقُوتٗا﴾

{Ndithudi, Swala ndilamulo lokhala ndi nthawi kwa okhulupirira}. [Al-Nisa]. Kutanthauza: chokakamizidwa mu nthawi zodziwika.

Ndipo nthawi za swala zokakamizidwa, ndi izi:

A- Fajir: Kuchokera pakutuluka kwa m'bandakucha mpaka kutuluka kwa dzuwa.

B- Dhuhr: Kuyambira kupendeka kwa dzuwa mpaka mthunzi wa chinthu chilichonse ulingane nacho pakutalika kwake.

C- Asr: Kuyambira nthawi ya Dhuhr ikatha kufikira pomwe dzuwa lasanduka lachikasu, ndipo nthawi yake yosimidwa ndempaka kulowa kwa dzuwa.

D- Maghrib: kuyambira kulowa kwa dzuwa mpaka kutha kwa mtambo wofiira.

E- Swala ya Isha: kuyambira pa kutha kwa nthawi ya Maghrib mpaka pakati pa usiku.

2- Kubisa umaliseche:

Ichi ndicho chinthu chofunika kubisidwa, ndipo kuonekera kwake ndikoipa, komanso nkoyenera kuchitanacho manyazi. Tsono maliseche a mwamuna ndikuyambila pa mchombo mpaka pa bondo. Ndipo mzimayi yense ndi maliseche pa swala, kupatula nkhope yake, Ndipo aphimbe nkhope yake akakhala pamaso pa amuna adera, ndiko kuti: omwe si achibale ake a pamtima.

3- Kupewa nyansi:

Najisi ndiye nyansi zapadera zimene zimalepheretsa Swala; monga mkodzo, chimbuzi, mwazi, ndi zina zotero, ndipo zimapezeka pa nthupi, pa malo opempherera komanso pa nsalu.

4- Kuyang'ana ku Qiblah:

Qiblah ndi Kaaba yolemekezeka, idatchedwa Qiblah chifukwa cha kulunjika kwa anthu ku iyo.

Swala siyingalongosoke popanda kulunjika ku Qibla, Malinga ndi Mau a Allah wapamwamba oti:

﴿...وَحَيۡثُ مَا كُنتُمۡ فَوَلُّواْ وُجُوهَكُمۡ شَطۡرَهُ...﴾

{Ndipo paliponse pamene mulipo yang’anitsani nkhope zanu kumene kuli mzikitiwo}.

[Surat Al-Baqarah :144].

5- Chitsimikizo:

M'chiyankhulo: Ndi cholinga, ndipo m’malamulo a chipembedzo: Ndi kutsimikiza chifuniro chochita ntchito yopembedza pofuna kuyandikira kwa Allah wapamwamba. Ndipo malo ake ndi mu mtima, sipafunika kuitchula, koma kuitchulako ndi zinthu zopeka.

Chachinayi: Nsanamira za Swala:

Zilipo nsanamira khumi ndi zinayi:

Nsanamira yoyamba: Kuima kwa munthu amene angakwanitse:

- Malinga ndi Mau a Allah wapamwamba:

﴿‌...وَقُومُواْ لِلَّهِ قَٰنِتِينَ﴾

{....Imilirani modzichepetsa kwa Allah}. [Al-Baqarah:238] Ndi nkhani yochokera kwa Imraan -Allah asangalasidwe naye yomwe idachokera kwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye:

«صَلِّ قَائِمًا، فَإِن لَمْ تَسْتَطِعْ فَقَاعِدًا، فَإِن لَمْ تَسْتَطِعْ فَعَلَى جَنْبٍ».

“Pemphera utaima, ngati sukwanitsa khala, ngati sukwanitsa gona chambali”16.

Ngati sakwanitsa kuima chifukwa cha matenda; aswali molimgana ndi mmene alili; atakhala pansi, kapena atagona chambali. Mofanana ndi wodwala ndi: wochita mantha, wopanda chovala, ndi amene akufunika kukhala kapena kugona chifukwa cholandira chithandizo chomwe chimafuna kuti asaime. Momwemonso, amakhululukidwa kusiya kuyimirira amene akupemphera kumbuyo kwa Imamu wanthawi zonse wolephera kuyimirira, choncho ngati apemphera atakhala pansi, ndiye kuti amene ali kumbuyo kwake nawonso apemphere atakhala pansi potsatira Imamu wawo. Nkololedwa kupemphera mapemphero osakakamizidwa ali chikhalire, ngakhale ali womakwanitsa kuimirira, koma malipiro ake sakhala ofanana ndi malipiro a wopemphera ataimirira.

Nsanamira yachiwiri: Takbiira yotsegulila swala kumayambiliro kwake (swala):

Kamba ka mau ake Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-oti:

«ثُمَّ اسْتَقْبِلِ الْقِبْلَةَ، وَكَبِّرْ».

"Kenako yang'ana Ku Qiblah, ndipo nenani Allah akbar"17.

Ndipo katchulidwe kake ndi kunena kuti: (Allah Akbar), ndipo mau ena alionse sakukwanira.

Nsanamila yachitatu: Kuwerenga Fatiha:

Kamba ka mau ake Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- onena kuti-:

«لَا صَلَاةَ لِمَنْ لَمْ يَقْرَأْ بِفَاتِحَةِ الْكِتَابِ».

"Swala siyingalongosoke ngati munthu sawerenga surah Fatiha"18.

Nsanamila yachinayi: Kuwelama pa raka iliyonse:

- Malinga ndi mau ake Allah wapamwamba oti:

﴿يَاأَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا ارْكَعُوا وَاسْجُدُوا...﴾

{E inu amene mwakhulupilira! Weramani ndikugwetsa nkhope pansi...} [Al-Hajj: 77].

Nsanamila ya chisanu ndi ya chisanu ndi chimodzi:

Kuwelamuka kuchokera pa Ruku, ndi kuongoka mutaima monga momwe zinalili poyamba, chifukwa iye (Mtumiki) adali kupitiliza kuchita zimenezi.

Ndipo adanena Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kwa wolakwitsa mu swala yake kuti:

«ثُمَّ ارْفَعْ حَتَّى تَعْتَدِلَ قَائِمًا».

«Kenako welamuka mpaka utaima mowongoka»19.

Nsanamira yachisanu ndi chiwiri: Kusujudu pa ziwaro zisanu ndi ziwiri:

Izi ndichipumi pamodzi ndi mphuno, manja awiri, mawondo awiri, ndi nsonga za zala za mapazi awiri Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-oti:

«أُمِرْنَا أَنْ نَسْجُدَ عَلَى سَبْعَةِ أَعْظُمٍ: الجَبْهَةِ، وَأَشَارَ بِيدِهِ عَلَى أَنْفِهِ، وَالكَفَّيْنِ، وَالرُّكْبَتَيْنِ، وَأَطْرَافِ القَدَمَيْنِ».

«Tidalamulidwa kupanga Sajida pa ziwaro zisanu ndi ziwiri: Chipumi, ndipo adaloza ku mphuno yake ndi dzanja lake, manja awiri, maondo awiri, ndi nsonga za zala za kumapazi awiri»20.

Nsanamila yachisanu ndi chitatu: Kuchoka pa sajida ndi kukhala pakati pa ma Sajida awiri:

Malinga ndi nkhani yochokera kwa Aisha-Allah asangalasidwe naye -yoti:

«كَانَ النَّبِيُّ ﷺ إِذَا رَفَعَ رَأْسَهُ مِنَ السَّجْدَةِ، لَمْ يَسْجُدْ حَتَّى يَسْتَوِيَ جَالِسًا».

«Anali Mneneri (s.a.w) akakweza mutu wake kuchokera pa Sajida, sankachita Sajida ina mpaka awongoke atakhala»21.

Nsanamila yachisanu ndi chinayi: kudekha mu nsanamira zonse:

Ndiko kukhanzikika ngakhale pang'ono, kamba ka Mau ake Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kwa wolakwitsa mu swala yake:

«حَتَّى تَطْمَئِنَّ».

"Mpaka utadekha"22.

Nsanamila ziwiri: yakhumi ndi yakhumi ndi chimozi:

Al Tashahhud yomariza ndi kukhala kwake: umboni ni nkhani yochokera kwa mwana Masud - Allah asangalasidwe naye - yomwe ikuchokera kwa Mtumiki-mtendere ndi Madalitso a Allah zikhale pa iye-:

«إِذَا صَلَّى أَحَدُكُمْ فَلْيَقُلْ: التَّحِيَّاتُ لِلَّهِ وَالصَّلَوَاتُ وَالطَّيِّبَاتُ، السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللَّهِ وَبَرَكَاتُهُ، السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللَّهِ الصَّالِحِينَ، أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا عَبْدُهُ وَرَسُولُهُ».

"Pamene m'modzi mwa inu apemphera, anene kuti: «at-tahiyyaatu lilah was-swalawat wat-twayyibaatu, as-salam alayka 'ayyuha nnabiyyu warahmatuallah wabarakatuhu, as-salam alayna waalaa ibadillah as-swaalihina, 'ashhadu 'an la 'ilaha 'illallah, wa'ashhadu 'anna muhammadan abduh warasuluhu»23.

Nsanamira ya khumi ndi ziwiri: Kumupemphera chifundo Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- mu Tashahhud yomariza:

Anene kuti:

«اللَّهُمَّ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ».

"Allahumma swalli a'la Muhammad"24, Ndipo zomwe angaonjezere pamenepo ndi zosakakamizidwa

Nsanamila ya khumi ndi zitatu: Kulondoloza pakati pa nsanamila:

Chifukwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-ankazichita molondoloza, Iye adati:

«صَلُّوا كَمَا رَأَيْتُمُونِي أُصَلِّي».

""Muzipemphera monga momwe mwandionera ine ndikupemphera".25 Ndipo adamphunzitsa nsanamirazo molondoloza wolakwitsa swala yake pogwiritsa ntchito liwu la «kenako».

Nsanamila ya khumi ndi zinayi: Kupereka salam:

Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-:

««‌وَخِتَامُهَا ‌التَّسْلِيمُ».

""Ndipo kutsiriza kwake ndi kupereka salamu", Komanso mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- oti:

«وَتَحْلِيلُهَا التَّسْلِيمُ».

«Ndipo kuthetsa kwake ndi kupereka salamu»26.

Chachisanu: Zinthu Zokakamizidwa Kuchita Popemphera:

Alipo asanu ndi atatu

1- Ma TAKBIRA onse kupatula Takbira yotsegulira swala (yoyamba).

2- Mau onena kuti: "Subhana rabbiyal adhwim" kamodzi powerama, Ndipo ndisunnah kuonjezera kufika katatu, ndipo umenewu ndi mulingo wochepa wokwanira. Ndipo kufikira ka khumi, ndiwo mulingo wapamwamba wake.

3- Mau oti: "Samia Allah liman hamidahu" powelamuka; kwa Imaam ndiyemwe akupemphera payekha.

4- Mau onena kuti: "Rabbana wa lakal hamdu" poyima njoo kuchokera powerama.

5- Mau oti: "Subhana rabbiyal a'ala" kamodzi pa Sajida, Ndi sunnah kuonjezera kufika katatu.

6- Mau oti: "Rabbi gufirli" pakati pa ma sajida awiri kamodzi, Ndi sunnah kuonjezera kufika katatu.

7- Al-Tashahhud yoyamba; ndipo anene mau awa:

«التَّحِيَّاتُ لِلَّهِ، وَالصَّلَوَاتُ وَالطَّيِّبَاتُ، السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللَّهِ وَبَرَكَاتُهُ، السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللَّهِ الصَّالِحِينَ، أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا عَبْدُهُ وَرَسُولُهُ».

"At-tahiyyaatu lillaah was-swalawatu wat-twayyibaatu, As-salaamu alayka ayyuha nnabiyyu warahmatullaahi wabarakaatuhu, As-salaamu alaynaa wa alaa ibaadillaahi s-swaalihiin, Ash-hadu an laa ilaaha illallaah wa ash-hadu anna Muhammadan abduhu warasuuluh"27

8- Kukhala kuti achite Al-Tashahhud yoyamba

Chachisanu ndi chimodzi: ma Sunnah a Swala:

Kusiya masunnah a swala, sikumaononga swala. Ndipo zili magulu awiri: ma Sunnah a mau, ndi ma Sunnah a zichitochito.

CHOYAMBA: SUNNAH ZA MAU

1- Duwa yotsegulira Swala, ndipo ili ndi kayankhulidwe kosiyanasiyana, kena mwa iko ndi aka:

«سُبْحَانَكَ اللَّهُمَّ وَبِحَمْدِكَ، وَتَبَارَكَ اسْمُكَ، وَتَعَالى جَدُّكَ، وَلَا إِلٰهَ غَيْرُكَ».

"Subuhanaka Allahumma wabihamdika, watabaaraka ismuka, wataalaa jadduka, walaa Ilaaha ghairuka"28 .

2- Kudzitchinjiriza mwa Allah isanawerengedwe Al-Fatiha, Ndipo ndi mawu akuti: "Au'dhu billah mina al-shaitwan rajim".

3- Kuwerenga Basmala, isanawerengedwe Al-Fatiha, Ndipo ndi mawu akuti: "Bismillahir Rahmanir Raheem".

4- Zoonjezera pa kamodzi mu Tasbiih ya powerama (Rukuu) ndi ya Sajida.

5- Zowonjezera pa kamodzi m'mau oti:

«رَبِّ اغْفِرْ لِي».

"Rabbi ghufir li" pakati pa ma masajida awiri

6- Mau oti:

«مِلْءَ السَّمَاوَاتِ، وَمِلْءَ الْأَرْضِ، وَمِلْءَ مَا بَيْنَهُمَا، وَمِلْءَ مَا شِئْتَ مِنْ شَيْءٍ بَعْدُ».

«Miliussamawaati, wamiliul-arudhwi, wamiliu maa baynahumaa, wamiliu ma shiita min shay-in baadu» Pambuyo pa mau oti:

«رَبَّنَا ولَكَ الحَمْدُ».

"Rabbana wa lakal hamdu"29.

7- Kuwerenga (Surah ina) pambuyo pa Fatiha.

8- Mau oti:

«اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ مِنْ عَذَابِ جَهَنَّمَ، وَمِنْ عَذَابِ الْقَبْرِ، وَمِنْ فِتْنَةِ الْمَحْيَا وَالْمَمَاتِ، وَمِنْ فِتْنَةِ الْمَسِيحِ الدَّجَّالِ».

"Allahumma inni a'udhubika min adhaab jahannam, wamin adhaabi-lqabri, wamin fitnat almahya walmamati, wamin fitnat almasih aldajjali"30. Ndi zomwe zawonjezeka pa zimenezo zokhuzana ndi Duwa mu Tashahhud yomaliza.

Chachiwiri: Ma Sunnah a Zichitochito:

1- Kutukula manja awiri molingana ndi mapewa kapena makutu m'malo anayi:

a- Pochita Takbiira yoyamba.

b- Popita pa Rukuu (kuwelama).

c- Poima kuchokera pa Rukuu.

d- Ponyamuka kupita ku Raka yachitatu.

2- Kuyika dzanja lamanja pa lamanzere pachifuwa pa nthawi yoyima, asanapite pa Rukuu ndiponso atachokapo.

3- Kuyang'ana pamalo opangira sajida.

4- Kulekanitsa mikono ndi nthiti pochita Sajida.

5- Kulekanitsa mimba ndi ntchafu m'ma Sajdah aŵiri.

6- Kukhalira mwendo m'makhalidwe onse a pa Swala, kupatula pa Tashah-hud yomaliza ya Swala za maraka atatu kapena anayi.

7- Kukhalira thako pa Tashah-hud yachiwiri pa swala ya ma Raka atatu kapena anayi.

CHACHISANU NDI ZIWIRI: KAPEMPHEREDWE KA SWALA:

1- Mtumiki wa Allah-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- akamaima kuswali, ankayang'ana ku Qibla, n’kunyamula manja ake, n’kulozetsa zikhato zake ku Qibla, ndipo ankanena kuti:

«اللهُ أَكْبَرُ».

"ALLAH AKBAR."

2- Kenako ndikugwira dzanja lake lamanzere ndi dzanja lake lamanja, n’kuwayika pachifuwa pake.

3- Kenako ndikutchula pemphero lotsegulira Swala, ndipo sanali wokhanzikika pa pemphero limodzi lotsegulira swala, Choncho, mapemphero onse otsegulira Swala otsimikizika kuchokera kwa iye ndi ololedwa, ena mwa iwo ndi awa:

«سُبْحَانَكَ اللَّهُمَّ وَبِحَمْدِكَ، وَتَبَارَكَ اسْمُكَ، وَتَعَالى جَدُّكَ، وَلَا إِلٰهَ غَيْرُكَ».

«Subuhanaka Allahumma wabihamdika, watabaaraka ismuka, wataalaa jadduka, walaa Ilaaha ghairuka».

4- Kenako ndikunena kuti:

«أَعُوذُ بِاللَّهِ مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّجِيمِ، بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ».

""Au'dhu billah mina al shaitwan al rajimi, Bismillahi al rahman al rahim"."

5- Kenako ndikuwerenga surat Faatiha, ndipo akamaliza, amanena kuti: «Aameen».

6-Kenako ndikuwerenga ndime zomwe zingampepukire za mu Quran, Ndikuwerenga mokweza mawu pa swala ya Fajr, ndi m'maraka awiri oyamba a swala ya Maghrib ndi Isha, Ndikuwerenga chapansipansi monse mosakhala mmenemo. Ndikutalikitsa raka yoyamba ya swala iliyonse kuposa yachiwiri.

7- Kenako ndikutukula manja ake monga anawatukulira pochita Istiftaah, Kenako ndikuyankhula kuti: «Allah Akbar», Kenako ndikuwerama, Ndipo ndikuika manja ake pa maondo ake atatambasula zala, ndi kuwakanikiza, n’kuwongola nsana wake, ndi kupanga mutu wake ufanane ndi nsanawo; osaukweza kapena kuutsitsa. Ndikunena kuti:

«سُبْحَانَ رَبِّيَ الْعَظِيمِ» مرةً.

"Subuhana Rabii Al-Adhwiimu" kamodzi, Ndipo kukwanira koyamdikira: ndikatatu, monga zatchulidwira kale.

8- Kenako ndikutukula mutu wake uku akunena kuti:

«سَمِعَ اللَّهُ لِمَنْ حَمِدَهُ».

"Samia Allah liman hamidahu." Nkunyamula manja ake monga mmene amachitira powelama.

9- Akayima mowongoka bwino amanena kuti:

«اللَّهُمَّ رَبَّنَا وَلَكَ الْحَمْدُ، حَمْدًا كَثِيرًا طَيِّبًا مُبَارَكًا فِيهِ، مِلْءَ السَّمَاءِ، وَمِلْءَ الْأَرْضِ، وَمِلْءَ مَا بَيْنَهُمَا، وَمِلْءَ مَا شِئْتَ مِنْ شَيْءٍ بَعْدُ، أَهْلَ الثَّنَاءِ وَالْمَجْدِ، أَحَقُّ مَا قَالَ الْعَبْدُ، وَكُلُّنَا لَكَ عَبْدٌ، لَا مَانِعَ لِمَا أَعْطَيْتَ، وَلَا مُعْطِيَ لِمَا مَنَعْتَ، وَلَا يَنْفَعُ ذَا الْجَدِّ مِنْكَ الْجَدُّ».

«Allahumma rabbana wa lakal-hamdu, hamdan kathiiran twayyiban mubaarakan fiihi, mil-as-samaa-i wa mil-al-ardhi, wa mil-a maa baynahumaa, wa mil-a maa shi'ta min shay-in ba'du, ahlath-thanaa-i wal-majdi, ahaqqu maa qaalal-'abdu, wa kullunaa laka 'abdun, laa mani'a limaa a'atwaita, wala muutwiya limaa mana'ita, walaa yanfau dhal-jaddi minkal-jadd»31 . Anali kutalikitsa kuima moongokaku.

10-Kenako anene "Allah akbar" ndikugwada pansi kupanga sajida, Ndipo asatukule manja ake awiri, Ndipo agunditse pansi chipumi chake ndi mphuno yake, manja ake, mawondo ake, ndi nsonga za zala za mapazi ake. Ndipo alunjike ku Qiblah ndi zala za manja ndi mapazi ake, Ndipo awongoke pa Sajida yakepo, Ndikukanikiza chipumi chake ndi mphuno yake pansi, Ndipo ayazamire pa manja ake n’kukweza zigongono zake, Ndipo atalikitse mikono yake ku nthiti zake, Komanso atalikitse mimba yake ku ntchafu zake, Ndi kutalikitsa ntchafu zake ku myendo yake, Pochita Sajida n’kunena kuti:

«سُبْحَانَ رَبِّيَ الأَعْلَى».

"Subhana rabbiyal a'ala" kamodzi, Ndipo kukwanira koyandikira ndiko kubwereza katatu, monga zatchulidwa kale, Ndipo apemphe ndi mapemphero omwe alandiridwa.

11- Kenako adzutse mutu wake akunena kuti: "Allah Akbar", Kenako ayale mwendo wake wamanzere ndi kuwukhalira, ndi kuimika phazi la kumanja, Ndipo aike manja ake pa ntchafu zake kenako anene kuti:

«اللَّهُمَّ اغْفِرْ لِي، وَارْحَمْنِي، وَاجْبُرْنِي، وَاهْدِنِي، وَارْزُقْنِي».

"«Allahumma ighifir Lii, warhamuni, wajburuni, wahdini, warzuquni»32."

12- Kenako anene kuti: "Allahu Akbar" ndikupanga sajida, ndipo achite mu Sajida yachiwiri monga momwe anachitira mu yoyamba.

13-Kenako adzutse mutu wake akunena kuti:”Allah Akbar”, ndipo ayimilire ndi nsonga za mapazi ake, uku akuyazamira pa mawondo ake ndi ntchafu zake.

14- Kenako akayima bwinobwino, ayambe kuwerenga, Ndipo apemphere Raka yachiwiri monga momwe apempherera yoyamba.

15- Kenako akhale pansi kuti achite Al Tashahhud yoyamba, moyala mwendo wamanzere pansi ndi kuwukhalira, monga amakhalira pakati pa masajida awiri Ndipo ayike dzanja lake lamanja pa ntchafu yake yamanja, ndi dzanja lake la manzere pa ntchafu ya manzere, Ndipo ayike chala chake chachikulu pamwamba pa chala chapakati kungokhala ngati mphete, Ndikuloza ndi chala chake chamkomba phala ndikumachiyang'ana. Kenako anene kuti:

«التَّحِيَّاتُ لِلَّهِ وَالصَّلَوَاتُ وَالطَّيِّبَاتُ، السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللَّهِ وَبَرَكَاتُهُ، السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللَّهِ الصَّالِحِينَ، أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيكَ لَهُ، وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا عَبْدُهُ وَرَسُولُهُ».

"At-tahiyyaatu lillaah was-swalawatu wat-twayyibaatu, assalam alaika ayyuha nnabiyyu, warahmatullah wabarakaatuh, assalam alaina waalaa i'baadillah sswalihiina, Ash-hadu an-laa ilaaha illaallah wahdahu laa shariika lahu, wa ashihadu anna Muhammadan abduhu warasuuluhu." Ndipo adali kufupikitsa kukhala kumeneku.

16-Kenako ayimilire akunena kuti 'Allah Akbar', ndipo apemphere Raka yachitatu ndi yachinayi, ndipo azipeputse kuposa ziwiri zoyambilira. Ndipo awerenge m'menemo Surat Fatiha.

17- Kenako azakhala pa Tashah-hud yotsiriza mokhalila thako, Tawarruk ndi kuyala phazi lake lamanzere nkulitulutsira ku mbali ya kumanja, ndikuimika phazi lake lamanja, ndikugunditsa thako lake pansi.

18- Kenako apange Al-Tashahhud yomaliza, ndipo ili ngati Al-Tashahhud yoyamba, Ndipo awonjezerepo mau oti:

«اللَّهُمَّ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ وَعَلَى آلِ مُحَمَّدٍ، كَمَا صَلَّيْتَ عَلَى آلِ إِبْرَاهِيمَ، إِنَّكَ حَمِيدٌ مَجِيدٌ، وَبَارِكْ عَلَى مُحَمَّدٍ وَعَلَى آلِ مُحَمَّدٍ، كَمَا بَارَكْتَ عَلَى آلِ إِبْرَاهِيمَ، إِنَّكَ حَمِيدٌ مَجِيدٌ».

"Allahumma swalli a'la Muhammad wa a'la ali Muhammad, kama swallaita a'la ali Ibrahima, Innaka hamidun Majid, wabaarik a'la Muhammad wa a'la ali Muhammad, kama barakta a'la ali Ibrahima, Innaka Hamidun Majiid."

19- Ndipo apemphe chitetezo kwa Allah ku chilango cha Jahannama, ndi ku chilango cha m'manda, ndi ku mayesero a moyo ndi imfa, ndiponso ku mayesero a Masiih Dajjal. Komanso apemphe maduwa amene adatchulidwa mu Qur'an ndi mu Sunnah.

20- Kenako apereke salam kumanja kwake, ponena kuti:

«السَّلَامُ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَةُ اللَّهِ».

"As-salam Alaikum Warahmatu Allah", Ndipo kumanzere kwake chimodzimodzi; Ayambe salaam ali wolunjika ku Qibla, ndipo ayimalize pamene akumaliza kutembenuka.

Chachisanu ndi chitatu: zonyasa kuchita nthawi ya swala:

1- Kutembenukatembenuka popanda chifukwa.

2- Kutukula maso kuyang'ana kumwamba.

3- Kutseka maso popanda chifukwa.

4- Kuyala mikono iwiri pochita Sajida.

5- Kuphimba pakamwa ndi mphuno popanda chifukwa.

6- Kupemphera swala uku akulimbana ndi mkodzo kapena chimbudzi, kapenanso chitabwera chakudya chomwe akuchikhumba.

7- Kupukuta chipumi chake ku zomwe zatsalirapo chifukwa cha kusujudu, ndipo palibe vuta kupukuta zimenezo pambuyo pa swala.

8- Kutsamila ku khoma ndi zina zotero poimilira popanda chifukwa.

Chachisanu ndi chinayi: zowononga swala:

1- Kudya ndi kumwa.

2- Kuyankhula zosakhudzana ndi swala.

3- Kuseka ndi kuseka mwa chikhakhali.

4- Kusiya mwadala chimodzi mwa nsanamira zake kapena zokakamizidwa zake.

5- Kuonjezera mwadala nsanamila kapena Raka'a.

6- Kumutsogolera Imaam(munthu akupempheresa) mwadala popereka salaam.

7- Kugwedezeka kochuluka kosatizana kosakhala muzichitochito za swala mopanda chifukwa.

8- Kuchita chimene chimawononga chimodzi mwa zofunikira kuti swala itheke, monga: kudula Wudhu, kuvundukula maliseche mwadala, kupatuka kwambiri ndi thupi kuchoka ku Qiblah popanda chifukwa, ndiponso kudula Niyyah(chitsimikizo).

Chakhumi: Sujud ya kuiwala

Sahu: Ndi kuiwala, ndipo Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iwe-adaiwala ali mu swala; chifukwa kuiwala kumachokera ku chibadwa cha munthu, Ndipo kuiwala kwake kunali gawo la kukwaniritsidwa kwa chisomo cha Allah pa ummah wake, ndi kukwanilitsidwa kwa chipembedzo chawo, kuti azitsatira chitsanzo chake pa malamulo amene anawakhazikitsira pa nthawi yoiwala.

Zomwe zimayenereza kupanga Sujudu yoiwala:

1- Mkhalidwe woyamba:

Kuonjezera mu swala, ndipo kumakhala kuonjezera ntchito kapena kuonjezera mawu:

A- Kuwonjezera zochita: Ngati kuwonjezera kuli kwamtundu wa swala: monga kuimirira pamalo okhala, ndi kukhala pamalo oimirira, kapena wawonjezera kuwerama (Rukuu) kapena kusujudu, akachita izi moiwala; apange Sujudu ya kuiwala.

b- Kuonjezera mawu: monga Kuwerenga mu Rukuu ndi Sujud,

Ndipo akachita zimenezo; zili zabwino kwa iye kupanga Sujudu yoiwala.

2- Mkhalidwe wachiwiri:

Kupungula mu swala chifukwa choyiwala, ndipo kumachitika mu imodzi m’njira ziwiri:

A. Kusiya nsanamila: ngati nsanamira imeneyi ili Takbirat al-ihram, swala yake siimamangika, ndipo Sujud as-sahw siingalowe m'malo mwake. Ndipo ngati ili nsanamira ina osati Takbira yoyambira swala, monga kuwerama kapena kusujudu, ndipo wakumbukira asanayambe kuwerenga kwa Raka ina; n’chokakamizika kuti abwerere, ndikuchita nsanamirayo ndi zomwe zatsatira pambuyo pake.

Ndipo ngati akumbukira atayamba kuwerenga kwa Raka ina, Raka imene adaisiya ija iwonongeka, ndipo Raka yotsatira itenga malo ake.

b- Kusiya chinthu chokakamizika: Monga: kuyiwala Tashah-hud yoyamba, kapena Tasbih mu Rukuu. Zikatero: apange Sujuda ya kuiwala.

3- Mkhalidwe wachitatu: kukaikira:

Chitsanzo: Ngati wakayika kuti kodi wapemphera ma Raka atatu kapena anayi mu Swala ya Zuhur, ndipo pamenepa:

a- Ngati china chake chitatsimikizika kwa iye, achite chimenecho, ndi kupanga sajida yoiwala.

b- Pakakhala kuti palibe chomwe chatsimikizika kwa iye, angochimanga chomwe akuchiganizira kuti ndicholondola, kenako ndikusujudu sajida yoiwala.

Ngati chikaiko chadza pambuyo pomariza kupemphera, kapena ngati munthuyo amachulutsa kukayikira; sayenera kuchilabadira chikaiko chimenecho.

Phindu: Sajida ya kuiwala imachitidwa Salaam isadaperekedwe: ngati chifukwa chake ndi kupunguza, kapena kukayikira popanda kutsamira ku mbali iliyonse. Ndipo kumachitika pambuyo popereka salam: Ngati chinali chifukwa cha kuonjezera, kapena kukayika kumene adagwiritsa ntchito maganizo otsimikizika, Ndipo nkhaniyi ndi yotakasuka, Allah akafuna.

Chakhumi ndi chimozi: Nthawi zoletsedwa kupemphera swala:

Malamulo oyambilira ndi akuti swala ndiyololedwa munthawi zonse, Koma malamulo achisilamu adaletsa kupemphera munthawi zina, ndipo nthawizo ndi izi:

1- Kuyambira pambuyo pa swala ya Fajr mpaka kutuluka kwa dzuwa, ndipo ndikukwera kufika msinkhu wa nthungo kuchokera pansi m’mene maso amaonera.

2- Nthawi imene dzuwa limakhala pakati pa thambo mpaka litapendeka, ndipo iyi ndi nthawi yaifupi kwambiri mwa nthawi zoletsedwa.

3- Kuyambira swala ya Asir mpaka kulowa kwa dzuwa, ndipo imeneyi ndi nthawi yaitali koposa mwa nthawi zoletsedwa.

Swala zomwe zimaloledwa kuzichita mu nthawi zoletsedwa:

1- Kubweza mapemphero okakamizidwa omwe akudutsa.

2- Swala zokhala ndi zifukwa, monga: Swala ya Tahiyatul masjidi, Ma Raka awiri a Twawaf, Swala ya Kusuf, ndi Swala ya Janaza.

3- Kubweza pemphero losakakamizidwa pambuyo popemphera pemphero la Fajr.

Chakhumi ndi chiwiri: swala yapagulu:

Ndipo ndi chizindikiro chachikulu mu zizindikiro za chisilamu, chomwe ndi swala yapagulu m'mizikiti, Ndithudi Asilamu agwirizana kuti kupemphera swala zisanu m’mizikiti ndi zina mwa ntchito zosonyeza kumvera Allah zofunika kwambiri komanso zazikulu zodziyandikitsira kwa Allah, komanso kuti icho ndi chizindikiro chachikulu kwambiri cha chisilamu.

1- Lamulo la swala yapagulu:

Ndipo swala yapagulu ndi yokakamiza m'mizikiti pa swala zisanu kwa amuna amene angakwanitse, Pakhomo ndi paulendo, Pa nthawi ya mtendere ndi ya mantha, monga chokakamizidwa pa munthu aliyense.

Ndipo umboni wotsimikizira kulamulidwa kwa swala yapagulu ndi: Qur'an ndi Sunnah, ndi machitidwe a Asilamu, m'badwo ndi m'badwo, otsatira kutengera kwa amene adawatsogolera.

Umboni wochokera m'Buku ndi mau ake (Allah) wapamwamba oti:

﴿وَإِذَا كُنتَ فِيهِمۡ فَأَقَمۡتَ لَهُمُ ٱلصَّلَوٰةَ فَلۡتَقُمۡ طَآئِفَةٞ مِّنۡهُم مَّعَكَ...﴾

{Ndipo ngati uli pamodzi ndi iwo Asilamu pankhondo ndikuwatsogolera Swala, ndiye kuti gulu limodzi la iwo liimilire pamodzi ndi iwe...} [Surat Al-Nisa:102]. Chifukwa ndime imeneyi yatsindika za kukakamizidwa kwa swala yapagulu, Pakuti sipanaloledwe kwa Asilamu kuisiya pa nthawi ya mantha, Zikanakhala kuti sichinali chinthu chokakamizidwa kuchichita, ndiye kuti chifukwa chachikulu cholekera chikanakhala mantha. Ndipo kusiya swala ya pa gulu ndi kuchita ulesi pa iyo, ndi chimodzi mwa zizindikiro zodziwika kwambiri za ma munafiqun akamberembere.

Komaso kuchokera mu Sunnah muli ma nkhani zambiri, imodzi mwa iwo ndi iyi:

Zomwe zabwera mu buku la Sahih Muslim.

أَنَّ رَجُلًا أَعْمَى قَالَ: يَا رَسُولَ اللَّهِ، لَيْسَ لِي قَائِدٌ يَقُودُنِي إِلَى الْمَسْجِدِ، فَسَأَلَهُ أَنْ يُرَخِّصَ لَهُ أَنْ يُصَلِّيَ فِي بَيْتِهِ، فَرَخَّصَ لَهُ، فَلَمَّا وَلَّى دَعَاهُ فَقَالَ: «هَلْ تَسْمَعُ النِّدَاءَ؟» قَالَ: نَعَمْ، قَالَ: «فَأَجِبْ».

Kuti munthu wina wosaona adati: “E, Mtumiki wa Allah, ndilibe wonditsogolera wopita nane kumzikiti,” ndiye adampempha kuti amuloleze azipemphelera kunyumba kwake. Ndipo adamuloleza. Koma pamene adatembenuka kuti achoke, adamuyitana ndipo adati: “Kodi ukumva muitano Azan?” Adati: “Inde.” Adati: “Ndiye yankha (pobwera kuzapemphera).”33.

Ndipo Mtumiki-mtendere ndi madalitsoa Mulungu zikhale pa iye-adamulamula kuti azifika ku mzikiti kukapemphera Swala ya pagulu ndikuyankha kuitana(Azan), ngakhale kuti iye anali wakhungu komanso ndi zovuta zomwe amakumana nazo, Choncho izi zikusonyeza kukakamizika kwa Swala yapagulu.

2- Zimene zingampangitse munthu kuipeza swala yapa gulu:

Swala yapa gulu imapezedwa poipeza Raka imodzi ya swala pamodzi ndi Imam, Kamba ka Mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-onena kuti-:

«مَنْ أَدْرَكَ رَكْعَةً مِنَ الصَّلَاةِ فَقَدْ أَدْرَكَ الصَّلَاةَ».

«Yemwe wapeza Raka imodzi mu swala, ndiye kuti waipeza swalayo»34.

3- Kapezedwe ka Raka:

Raka imapezedwa poipeza Ruku, Choncho ngati wochedwa wapeza imamu wake ali pakuwerama: ayenera kupanga Takbira yoyambira swala (Takbiratu al-ihram) ali chiimire, kenako n'kuwelama uku akupanganso Takbira ina yowelamira, Ndipo ngati atangopanga Takbira yotsegulira ali choyima, imukwanira m'malo mwa Takbira ya Ruku.

4- Zifukwa zomwe munthu amaloledwera kusiya Swala ya yapa gulu:

1- Kudwala, ngati kuli kovuta kupita nako ku swala ya la chisanu ndi ya pagulu.

2- Kulimbana ndi mkodzo kapena chimbudzi; chifukwa kumachotsa kukhuzumuka kwa pa swala, komanso kumavulaza thupi.

3- Kupezeka kwa zakudya pomwe munthu ali ndi njala, kapena mtima wake ukulakalaka zakudyazo, koma chisakhaletu chizolowezi kapena ndale zosiyira Swala ya pagulu.

4- Mantha otsimikizika okhudza moyo, chuma, kapena zina zotero.

Chakhumi ndi chitatu: Swala ya mantha:

Swala ya mantha yalamulidwa pa nkhondo iliyonse yololedwa, monga kulimbana ndi makafiri, opandukira chilamuli ndi achifwamba, chifukwa cha mau a Allah wapamwamba oti:

﴿...إِنۡ خِفۡتُمۡ أَن يَفۡتِنَكُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ...﴾

{...ngati mukuopa kuti angakusokonezeni omwe sadakhulupilire...} [Surat Al-Nisa:101]. Ndipo yerekezerani ndi zimenezi ena onse otsala amene ndikololedwa kuwamenya nkhondo.

Swala ya mantha imaswalidwa patapezeka zinthu ziwiri:

1) M'daniyo akhale wololedwa kumupha.

2) Kuopa kuti angawambwandire Asilamu pa nthawi ya swala.

Kapempheredwe ka Swala ya mantha:

Ili ndi kapempheredwe kosiyanasiyana, ndipo kotchuka kwambiri ndi komwe kadanenedwa mu hadisi ya Sahl - Allah asangalasidwe naye:

أَنَّ طَائِفَةً صَفَّتْ مَعَ النَّبِي ﷺ، وَطَائِفَةً وِجَاهَ العَدُوِّ، فَصَلَّى بِالَّتِي مَعَهُ رَكْعَةً، ثُمَّ ثَبَتَ قَائِمًا، وَأَتَمُّوا لِأَنْفُسِهِمْ، ثُمَّ انْصَرَفُوا، وَصَفُّوا وِجَاهَ العَدُوِّ، وَجَاءَتِ الطَّائِفَةُ الأُخْرَى، فَصَلَّى بِهِمُ الرَّكْعَةَ الَّتِي بَقِيَتْ مِنْ صَلَاتِهِ، ثُمَّ ثَبَتَ جَالِسًا، وَأَتَمُّوا لِأَنْفُسِهِمْ، ثُمَّ سَلَّمَ بِهِمْ.

Kuti gulu lina linapanga mzere pamodzi ndi Mneneri-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- ndipo gulu lina lili moyang'anizana ndi adani, ndipo anaswalitsa gulu limene linali naye rakaa imodzi, kenako anakhala chete ataimilira, ndipo iwo anadzimalizira okha, kenako anachoka ndikukapanga mzere moyang'anizana ndi adani, ndipo linadza gulu lina lija, ndipo anawaswalitsa rakaa yomwe inatsala mu swala yake, kenako anakhala chete atakhala pansi, ndipo iwo anadzimalizira okha, kenako anapereka salam pamodzi nawo35.

Ndipo tikupindula kuchokera mu Swala ya mantha:

1- Kufunikira kwa swala mu Chisilamu, ndi kufunikira kwa swala yapagulu, popeza siimasiyidwa ngakhale mu nthawi zovuta.

2- Kuchotsa zolemetsa pa mpingo uwu, ndiponso kupepuka kwa malamulo a chisilamu ndi kuyenera kwake pa nthawi iliyonse ndi malo alionse.

3- Kukwanira kwa malamulo a chisilamu, ndikuti pa nkhani iliyonse adakhazikitsa choyenerana nayo.

 

 

Chakhumi ndi chinayi: Swala ya tsiku la chisanu:

CHOYAMBA: LAMULO LAKE

Swala ya Ijumaa ndi yokakamizidwa (Faradhwi) payekha payekha kwa Msilamu aliyense wamwamuna, wokutha msinkhu, wanzeru, wosakhala paulendo, komanso wopanda chifukwa.

Chifukwa cha mau a Allah wapamwamba oti:

﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نُودِيَ لِلصَّلَوٰةِ مِن يَوۡمِ ٱلۡجُمُعَةِ فَٱسۡعَوۡاْ إِلَىٰ ذِكۡرِ ٱللَّهِ وَذَرُواْ ٱلۡبَيۡعَۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ 9﴾

{E inu amene mwakhulupirira! Kukaitanidwa ku Swala (pemphero la Ijuma) tsiku la Ijuma, pitani mwachangu kukamtamanda Allah. Ndipo siyani malonda; zimenezo (mwalamulidwazo) nzabwino kwa inu ngati mukudziwa-9}. [Surat Jumua:9].

Komanso chifukwa cha mawu a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- oti:

«لَيَنْتَهِيَنَّ أَقْوَامٌ عَنْ وَدْعِهِمُ الْجُمُعَاتِ، أَوْ لَيَخْتِمَنَّ اللَّهُ عَلَى قُلُوبِهِمْ، ثُمَّ لَيَكُونُنَّ مِنَ الْغَافِلِينَ».

"Anthu ena asiye ndithu kuleka mapemphero a JUMUA, apo ayi Allah adzadinda m'mitima mwawo, kenako adzakhala mwa osalabadira»36."

 

 

CHACHIWIRI: ZOYENERA KUTI SWALA YA LA CHISANU IKHALE YOVOMEREZEKA:

a) Nthawi yake: Ndipo nthawi yake ndi monga nthawi ya Swala ya Zuhur, Siyovomerezeka nthawi yake isanakwane, komanso itatha.

2- Kuti ipempheredwe mwa jama'ah(pagulu), ndipo gulu lochepa limayamba ndi anthu atatu, malinga,komwe ndikuyankhula kolondola mu mayankhulidwe a anthu ophunzira. Choncho,siyingakhale yolondola ngati itapempheredwa ndi munthu m'modzi kapena awiri.

3)Opempherawo afunika kukhala okhazikika pamudzi pomangidwa manyumba monga mwa chizolowezi cha m'deralo. Kaya zomangidwa ndi simenti olimba, kapena miyala, kapena dongo ndi zina zotero, Chifukwa cha zimenezi, pemphero la lachisanu siyingavomerezedwe kuchokera kwa anthu oyendayenda a kuchipululu, okhala m'mahema, amene sakhazikika pamalo amodzi, koma amangosamuka-samuka kutsatira malo a msipu wa ziweto zawo.

4-Kuti patsogole ma ulaliki awiri, chifukwa ichi chidali chizolowezi cha Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.

Chachitatu: Nsanamila za ma khutuba awiri a tsiku la chisanu:

1- Kumuyamika Allah ndi mau awiri a shahada (oyikira umboni pa umodzi wa Allah ndi utumiki wa Muhammad).

2- Kumufunira zabwino Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.

3- Kulangiza za kuopa Allah.

4- Kuwerenga gawo la m'Quran.

5- Kupereka ulaliki.

Chachinayi: Ma Sunnah a khutuba ziwiri za tsiku la chisanu:

1- Kuchitira khutuba pa Mimbari.

2- Kulekanitsa pakati pa ma khutuba awiri pokhala pansi pang'ono. 3- Kuwapempherera Asilamu ndi olamulira awo popanga duwa m'menemo.

4- Kufupikitsa m.

5- Kupereka salam wochita khutubayo kwa anthu pokwera pa mimbar.

Chachisanu: Masunnah a tsiku la chisanu:

1- Kutsuka mkamwa ndi mswachi.

2-Kudzola mafuta onunkhira ngati atapezeka.

3- Kulawira popita ku swala ya la chisan.

4- Kuyenda pansi popita ku mzikiti ndi kusakwera chokwera.

5- Kumuyandikira Imaam.

6- Kupanga duwa.

7-Kuwerenga Surat Al-Kahfi.

8- Kumufunira zabwino Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.

Chachisanu ndi chimodzi: Zinthu zoletsedwa kwa amene wabwera ku mapemphero a la chisanu:

1- Ndikoletsedwa kulankhula pamene Imam akupereka Khutuba patsiku la Jumua, chifukwa cha mau ake a Mneneri-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye--:

«إِذَا قُلْتَ لِصَاحِبِكَ يَوْمَ الْجُمُعَةِ: أَنصِتْ، وَالْإِمَامُ يَخْطُبُ، فَقَدْ لَغَوتَ».

«Ngati utanena kwa mnzako patsiku la Jumua kuti: "Khala chete," pamene Imam akupereka Khutuba, ndithu wachita zopanda pake»37. Ndiko kuti: Wayankhula mau achabechabe, ndipo mau achabechabe ndi tchimo.

2-Ndi zonyasa kuwakankha anthu mapewa kuti udutse kupita kusogolo, pokhapokha ngati ali Imamu(munthu olalikira), kapena kukankha popita pa mpata umene sangaufikire popanda kutero.

Kulipeza pemphero la lachisanu:

Amene wapeza Ruku pamodzi ndi Imamu mu Raka yachiwiri ya swala ya lachisanu(Jumua), ameneyo wapeza swala ya lachisanu(Jumua), ndipo aimarize ndi ma Raka awiri, Ndipo ngati sadapeze ruku ya raka yachiwiri, ndiye kuti pemphero la Jumua lamudutsa, ndipo alimarize ngati pemphero la Zuhr popemphera maraka anayi. Moteronso, amene waphonya pemphero la lachisanu(Jumua) chifukwa cha tulo kapena chifukwa china chilichonse, iye ayenera kupemphera pemphero la Zuhr.

Chakhumi ndi chisanu: Swala ya anthu oti ali ndi vuto:

Choyamba: Swala ya odwala:

Choyamba: odwala akuyenera kupemphera swala mmene angathere, Si zovomerezeka kwa iye kuichedwetsa kusiya nthawi yake mmene nzeru zake zikhalire zili mmalo.

Chachiwiri: kodi odwala angapemphere bwanji?

1- Odwala ayenera kupemphera ataima ngati angakwanitse kuimilira popanda chovuta kapena chovulaza, ndipo awelame ndi kugwetsa mphumi lake pansi (sajida).

2-Ngati kuwelama komanso kugwetsa mphumi lake pansi zikumampezesa vuto pomwe angakwanitse kuima,akuyenera kungowelama cholozera mutu , komanso kungogwetsa mphumi lake cholozera ali chikhalire.

3- Ngati sangakwanitse kuswali choimilira aswali chokhala, Ndipo Sunnah ndikuti akhale pansi chopiringiza miyendo m'malo moimilira, ndipo awelame posonyeza Ruku, ndipo asujudu pansi ngati n'kotheka. Apo ayi, awelamitse mutu posonyeza Sujud, ndipo kuwelamitsa kwake kukhale kotsika kuposa kwa Ruku.

4- Ngati sakwanitsa kuswali atakhala, aswali atagona chammbali, ndipo ayang'anitse nkhope yake ku Qiblah, Ndipo mbali ya kumanja ndi yabwino kwambiri ngati n'zotheka, ndipo awelamitse pang'ono mutu posonyeza Ruku ndi Sajida.

5- Ngati sangakwanitse kuswali cham'mbali, aswali atagona chagada, miyendo yake italoza ku Qibla, ndipo adziwelamitsa mutu wake posonyeza Ruku ndi Sajida.

6- Ngati sizingatheke kwa iye kusonyeza ndi thupi lake powerama ndi popanga sajida; asonyeze ndi mutu wake, ngati zimenezo zitamuvuta; kusonyezako kumuchokera, ndipo achite ntchito za swala mu mtima mwake, polingalira zochita za swala monga kuwelama, kupanga sajida, ndi kukhala pansi ali m’mene alili, ndipo azinena zonena za pa swala (adhikar).

7- Odwala apange pa malamulo a swala zomwe angakwanitse, monga: kulunjika ku Qibla, kuchita Udhu ndi madzi, kapena kupanga Tayammum akalephera kugwiritsa ntchito madzi, komanso adziyeretse ku zonyansa. Ndipo ngati walephera china mwa izi, udindo umamuchokera, ndipo apemphera malinga ndi momwe alili, ndipo asachedwetse swala pa nthawi yake.

8- Sunnah ndi yakuti wodwala azikhala chopiringa miyendo pamalo a Qiyam ndi Ruku, ndipo mwina monse adzikhalira mwendo.

Chachiwiri: Swala ya munthu wa pa ulendo:

1- Mwa anthu okhala ndi zifukwa zovomerezeka ndi munthu wa pa ulendo, ndipo amaloledwa kufupikitsa swala ya maraka anayi kukhala maraka awiri, Malinga ndi mau a Allah wapamwamba oti:

﴿وَإِذَا ضَرَبۡتُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَلَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَقۡصُرُواْ مِنَ ٱلصَّلَوٰةِ...﴾

{Ndipo ngati mukuyenda pa dziko, sikulakwa kwa inu kufupikitsa swala...}. [Surat Al-Nisa:101].

Ndipo nkhani idachokera kwa Anasi mwana wa Maliki-Allah asangalasidwe naye-amene adati:

«خَرَجْنَا مَعَ النَّبِيِّ ﷺ مِنَ الْمَدِينَةِ إِلَى مَكَّةَ، فَكَانَ يُصَلِّي رَكْعَتَيْنِ رَكْعَتَيْنِ، حَتَّى رَجَعْنَا إِلَى الْمَدِينَةِ».

«Tinanyamuka limodzi ndi Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kuchokera ku Madina kupita ku Makka, ankapemphera ma Raka awiri-awiri, mpaka pomwe tinabwerera ku Madina»38.

Ndipo kufupikitsa swala kumayamba kwa munthu wapaulendo akangosiyana ndi nyumba za m'mudzi wake; chifukwa Allah adalola kufupikitsa swala kwa amene akuyenda ulendo pa dziko, Ndipo asanatuluke m'mudzi mwake, sawerengedwa kuti ndimunthu wa pa ulendo, chifukwa choti Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-ankapungula swala akangoyamba ulendo.

2- Mtunda umene ngati wapaulendo akufuna kuuyenda amaloledwa kufupikitsa swala, ndi pafupifupi makilomita makumi asanu ndi atatu.

3- Wa paulendo amapungula swala pobwerera, kufikira atalowa m'mudzi wakwawo umene anatulukamo.

4- Ngati wa paulendo wafika m'mudzi ndipo akufuna kukhazikikamo, ndiye pali makhalidwe itatu:

a) Kukhala ndi cholinga chokhala masiku oposa anayi; ndiye ayenera kukwanilitsa swala yake kuyambira tsiku loyamba limene wakhazikika, ndipo saloledwa kugwiritsa ntchito zilolezo za pa ulendo.

b) Kukhala ndi cholinga chokhala masiku anayi kapena ocheperako, pamenepo amaloledwa kufupikitsa ndi kutenga zilolezo za pa ulendo.

c) Asakhale ndi cholinga chokhala nthawi yodziwika, koma akhoza kukhala tsiku limodzi kapena masiku khumi kutengera momwe zinthu zilili pamalopo, kapena ngati ali ndi chifukwa monga kupeza chithandizo cha mankhwala kapena kukatsiriza chinthu china, ndipo chifukwa chake chikadzatha amabwerera kwawo. Choncho munthu wotere amaloledwa kufupikitsa swala ndi kugwiritsa ntchito zilolezo za pa ulendo mpaka atabwerera, ngakhale nthawi yakukhala kwake itapitirira masiku anayi.

5-Ngati munthu amene ali paulendo apemphera kumbuyo kwa Imam okhala pakhomo; ayenera kukwaniritsa swala, ngakhale atangompeza ali mu Tashah-hud yomariza.

6-Ngati munthu wapa khomo wapemphera kumbuyo kwa munthu wa pa ulendo yemwe akufupikitsa swala, ndikokakamizika kwa iye kukwanilitsa swala yake Imaam atapereka salaam.

Cha Khumi ndi chisanu ndi chimodzi: Swala ya Eid ziwiri (Zisangalalo ziwiri):

Zisangalalo za Asilamu, ndi zisangalalo zopembedzera Mbuye, zomwe zidakhanzikitsidwa kwa iwo ndi Allah wapamwamba, osati kuti anazipeka okha ayi. Ndipo iwo alibe zisangalalo zina koma ziwiri zokha: Eidu Al-Fitr, ndi Eidu Al-Adhuha. Mosiyana ndi zisangalalo za anthu okanira kapena zisangalalo zopeka, zimene Allah sanazikhanzikitse ndiponso sanazilamulire, koma iwo anadzipangira okha.

Lamulo la Swala ya Eid ziwiri:

Ndi lamulo lokakamiza ku gulu, limene Mtumiki-mtendeere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- adalisamalira mosalekeza, komanso alowa m'malo owongoka, Allah akondwere nawo onse. Ndi zina mwa zizindikiro ndi ntchito zowonekera za chipembedzo.

Nthawi ya Swala za Eid: Imayamba dzuwa litakwera msinkhu wa mkondo, ndiko kuti: pafupifupi mphindi khumi ndi zisanu kuchokera pamene dzuwa latuluka, ndipo nthawi yake imathera dzuwa likapendeka.

Kapempheredwe ka Swala za Eid:

1- Mu Raka yoyamba anene Takbira yotsegulira swala, kenako awerenge pemphero lotsegulira swala, kenako anene ma Takbira asanu ndi imodzi, akweze manja ake pa Takbira iliyonse, ndipo amtamande Allah ndi kumchemerera, ndi kumswalira Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-pakati pa ma Takbira, kenako anene A’uudhu billah minash-shaitwan rajim ndi Bismillah Rahman Rahim, ndi kuyamba kuwerenga (Fatihah).

2-Ndipo mu Raka yachiwiri, atapanga Takbira yoimira, apangenso ma Takbira ena asanu. Kenako anene mau ozitchinjirizira mwa Allah ku zoipa za Satana ndikuyamba kuwerenga ndi Bismillah. Ndipo mwa Sunnah, mu raka yoyamba pambuyo pa Fatiha awerenge Sura Al-A’la, ndipo mu yachiwiri awerenge Sura Al-Ghashiyah.

3-Imam akapereka salamu; akwere pa Mimbar, ndipo apereke ma Khutuba awiri, ndipo akhale pansi pakati pawo kukhala kwapang'ono, monga mmene amachitira mu Khutuba ya Jumua.

Ma Sunna a Eid:

a-Kusamba.

b-Kudziyeretsa ndi kudzola mafuta onunkhira.

c-Kudya asanapite ku Swala pa Eidu Al-Fitr, ndipo pa Eidu Al-Adhuha atabwera, nkudya kuchokera ku nsembe yake ngati ali nayo.

d-Kutuluka moyenda wa pansi.

e-Kupita podzera njira ina, ndikubweranso ndi njira ina.

f-Kulawira kupita ku mzikiti kwa munthu wa mamuma osati Imam.

Takbira:

Ndipo ndisunnah kupanga Takbira m'mausiku a ma Eid awiri, ndi masiku khumi a Dhul-Hijjah, komanso masiku ozinga zinyama, ndipo ilipo mitundu iwiri:

Mtundu woyamba: Takbir yopanda malire: ndipo ndi imene sili yomangidwa ndi nthawi yake yoikidwiratu.

1-Pa Fitr: kuyambira kulowa kwa dzuwa usiku wa Eid mpaka kuyamba kwa Swala ya Eid.

2-Pa Eidul Adha: kuyambira dzuwa litalowa usiku wa tsiku loyamba la mwezi wa Dhul-Hijjah mpaka dzuwa litalowa pa tsiku lomaliza la masiku ozinga zinyama.

Mtundu wachiwiri: Takbira yomangidwa: ndipo ndi yomwe imapangidwa pambuyo pa Swala zokakamizidwa.

1-Kwa yemwe sali pa mapemphero a Hajj: Kuyambira m'bandakucha wa tsiku la Arafah mpaka madzulo a tsiku lomariza masiku ozinga zinyama.

2-Yemwe ali pa mapemphero a Hajj: Kuyambira pa pemphero la Dhuhr pa tsiku la Eid mpaka nthawi ya Asr pa tsiku lomariza la masiku ozinga zinyama.

Chakhumi ndi chisanu ndi chiwiri: Swala ya kadamsana:

Tanthauzo la Khusuf ndi Kusuf:

Al-Khusuf: ndiko kuchoka kuwala kwa mwezi kapena mbali ina ya mwezio usiku.

Al-Kusuf: ndiko kuchoka kuwala kwa dzuwa kapena mbali ina ya dzuwalo masana.

Lamulo la Swala ya Kadamsana:

Ndi Sunnah yotsimikizika, ndipo chisonyezo chake ndi chochita cha Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- amene anaiswali pamene kunachitika kadansana m'nthawi yake-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye, Monga momwe adasonyezera polamula kwake za iyo, ndipo maulama onse adagwirizana pa kukhanzikitsidwa kwake.

Nthawi yake:

Kuyambira kuyamba kwa kadamsana kapena kadausiku mpaka kuyera kwake, ndiko kutha kwa kadausiku kapena kadmsana.

Kaswalidwe kake:

Chiwerengero cha ma Raka ake ndi awiri, amawerenga mokweza mau m'ma Raka onsewo, ndipo kapempheredwe kake ndi motere:

a- Apange Takbirat Al-Ihram, ndikupanga ndikutsegulira pempherolo ponena pemphero lotsegulira, kenako kupempha chitchinjirizo cha Allah kuchokera ku zoipa za Satana,ndi kuwerenga Bismillah kenako kuwerenga Al-Fatiha motalikitsa.

b-Kenako awelame nthawi yaitali.

c-Kenako anyamuke kuchokera pa Ruku, ndipo anene kuti: (Sami'a Allahu liman hamidahu), kenako awerenge Al-Fatiha, ndi kuwerenganso (ndime zina) kuwerenga kwakutali koma kofupikirako osakufika kuwerenga koyamba kuja.

d-Kenako awelame kuwelama kwakutali, koma kofupikirako osakufika kuwelama koyamba kuja.

e-Kenako adzuke kuchokera pa Ruku, ndipo anene kuti: "Sami'a Allah liman hamidahu".

f- Kenako achite ma Sajda awiri atali.

g-Kenako anyamuke kukaswali raka yachiwiri, yomwe imapangidwa mofanana ndi yoyamba, koma siikhala yaitali monga yoyambayo.

Ma Sunnah ake:

A-Kuitanira ku swalayo ndi mau oti: (As-swalatu ja'amia-kutanthauza: tikapemphere pemphero la pagulu).

B- Ipempheredwe pagulu.

C-Kutalikitsa Swala pa kuima kwake, kuwelama kwake, ndi kusujudu kwake.

D-Raka yachiwiri ikhale yofupikirako kuposa yoyamba.

E-Kupereka ulaliki pambuyo pake, ndi kulimbikitsa kuchita ntchito zomvera Allah ndikusiya zoipa.

F-Kuchulutsa kumupempha Allah, kudzichepetsa, kupempha chikhululuko ndi kupereka chopereka cha ulere.

Chakhumi ndi chisanu ndi chitatu: Swala ya kupempha mvula:

1) Al-Istisqau: Kumeneko ndiye kupempha madzi kwa Allah pogwetsa mvula pa nthawi ya chilala.

Nthawi yolamulidwa Swala ya Istisqaa(pemphero lopempha mvula):

Swala yopempha mvula imakhazikitsidwa ngati nthaka yauma, mvula n’kuleka kugwa, ndipo mavuto n’kuyamba kuoneka chifukwa cha kusowa kwake. Choncho palibe chomwe angachite kupatula kupempha Mbuye wawo modzichepetsa, ndi kumpempha kuti awapatse mvula, ndi kupemphanso thandizo kwa Iye pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zopemphera.

A-Nthawi zina popemphera mapemphero a pagulu, kapena payekha payekha.

b-Kapenanso popanga duwa mu Khutuba(Ulaliki) wa tsiku la chisanu pomwe Mlaliki amakhala akupanga pemphero ndipo Asilamu akuvomereza pambuyo pake.

c-Nthawi zina popempha duwa nthawi iliyonse, popanda Swala kapena Khutuba.

Lamulo la Swala ya Istisqa'a:

Ndi Sunnah yotsimikizika pamene chifukwa chake chapezeka, potengera machitidwe a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-monga zilili mu nkhani yochokera kwa Abdul-Allah mwana wa Zayd, Allah asangalasidwe naye-amene adati:

«خَرَجَ النَّبِيُّ ﷺ إِلَى الْمُصَلَّى، فَاسْتَسْقَى، وَاسْتَقْبَلَ الْقِبْلَةَ، وَقَلَبَ رِدَاءَهُ، وَصَلَّى رَكْعَتَيْنِ».

«Mneneri (s.a.w) anatulukira kupita ku malo opemphelerako, adapempha mvula, anayang'ana ku Qibla, natembenuzira chovala chake chakunja, ndipo anapemphera maraka awiri»39.

Kapempheredwe ka Swala ya Istisqaa:

Kapempheredwe ka Swala yopempha mvula pamalo ake wopempherera, ndiofanana ndi malo opempherera Swala ya Eid. Ndibwino kuipemphera ku bwalo lopempherera monga Swala ya Eid, ndipo malamulo ake ali ngati a Swala ya Eid; pa chiwerengero cha ma Raka, kuwerenga mokweza mau, ndi kuipemphera khutuba isanachitidwe, komanso pa ma Takbira owonjezera a mu Raka yoyamba ndi yachiwiri, kuwerenga (Qur'an) kusanachitike, Monga momwe zalongosoledwera kale mu swala za Eid ziwiri. Ndipo apereke ulaliki umodzi.

Cha Khumi ndi Chisano ndi Zinayi: Malamulo a Maliro:

CHOYAMBA: KWA AMENE ALI PAFUPI NDI MUNTHU AMENE AKUTSIRIZIKA:

1-Ndi Sunnah kwa amene ali pafupi ndi munthu amene akutsirizika kuti amukumbutse kunena mau oti: «La ilaha illa Allah».

2- Ndi Sunnah kumuyang'anitsa ku Qibla.

3- Ndipo ndi bwino kumutseka maso ake.

4. Ndi Sunnah kuphimba thupi la wakufayo ndi nsalu pambuyo pomwalira.

5- Ndi zofunika kuchita changu pakumkonzekeretsa.

6-Ndi kofunikira kwambiri kufulumira kumulipilira ngongole zake.

7-Ndipo asambisidwe ndi kuvekedwa sanda, ndipo ziwirizi ndi zokakamizidwa kuchita gulu la anthu.

 

CHACHIWIRI: MALAMULO A SWALA YOPEMPHELERA WAKUFA:

Lamulo lake: Yokakamizidwa kuchitidwa ndi gulu

Zoyenera zake:

1) Kulunjika ku Qiblah.

2- Kubisa maliseche

3) Kupewa zonyasa.

4)Kuyera kwa opemphera ndi opempheleredwa.

5)Opemphera ndi opempheleredwa akhale Msilamu

6)Kukapezeka ku maliro ngati ali m'mudzimo.

7- Akhale opempherayo wafika pa msinkhu olamulidwa malamulo.

Nsanamila zake:

1)Kuima popempherapo.

2) Kuchita ma takbira anayi.

3) Kuwerenga Al-Fatiha.

4- Kumufunira zabwino Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.

5) Kumpemphera zabwino omwalira.

6.Kulondoloza

7) Kupereka Salamu.

Ma Sunnah ake:

1)Kunyamula manja pochita Takbira iliyonse.

2- Kunena: Audhu billah mina Al-Shaytwani Al-rajim.

3- Kudzipemphera zabwino wekha komanso Asilamu.

4) Kuwerenga motsitsa mau.

5- Ayime pang'ono pambuyo pa Takbira yachinayi, asanapereke salam.

6-Kuika dzanja la manja pamwamba pa dzanja la manzere pachifuwa.

7) Kutembenukira kumanja popereka salam.

Kapempheredwe kake:

Munthu opempheresa komanso amene akupemphera yekha aime ku mutu kwa maliro achimuna, ndi pakati pa maliro achikazi, achite Takbira yoyambilira, adzitchinjirize mwa Allah ku zoipa za Satana, asawerenge pemphero losegulira pemphero, awerenge Bismillah, ndi kuwerenga Al-Fatiha.

Kenako apange Takbira, ndipo pambuyo pake ampemphere madalitso Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kenako apangenso Takbira, ndipo ampemphere wakufayo zabwino pogwiritsa ntchito mapemphero omwe adaphunzitsa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa; Monga mau ake a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-oti-:

«اللَّهُمَّ اغْفِرْ لِحَيِّنَا وَمَيِّتِنَا، وَصَغِيرِنَا وَكَبِيرِنَا، وَذَكَرِنَا وَأُنثَانَا، وَشَاهِدِنَا وَغَائِبِنَا، اللَّهُمَّ مَنْ أَحْيَيْتَهُ مِنَّا فَأَحْيِهِ عَلَى الإِيمَانِ، وَمَنْ تَوَفَّيْتَهُ مِنَّا فَتَوَفَّهُ عَلَى الإِسْلَامِ، اللَّهُمَّ لَا تَحْرِمْنَا أَجْرَهُ، وَلَا تُضِلَّنَا بَعْدَهُ».

"Allahumma ighfir lihayyina wamayyitina, waswaghirina wakabirina, wadhakarina wa-unthana, washahidina wagha'ibina, Allahumma man ahyaytahu minna fa-ahyihi 'alal-iman, waman tawaffaytahu minna fatawaffahu 'alal-islam, Allahumma la tahrimna ajrahu, wala tudhillana ba'dahu"40.

Komanso mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye:

«اللَّهُمَّ اغْفِرْ لَهُ وَارْحَمْهُ، وَعَافِهِ وَاعْفُ عَنْهُ، وَأَكْرِمْ نُزُلَهُ، وَوَسِّعْ مَدْخَلَهُ، وَاغْسِلْهُ بِالْمَاءِ وَالثلْجِ وَالْبَرَدِ، وَنَقِّهِ مِنَ الْخَطَايَا كَمَا نَقَّيْتَ الثَّوْبَ الْأَبْيَضَ مِنَ الدَّنَسِ، وَأَبْدِلْهُ دَارًا خَيْرًا مِنْ دَارِهِ، وَأَهْلًا خَيْرًا مِنْ أَهْلِهِ، وَزَوْجًا خَيْرًا مِنْ زَوْجِهِ، وَأَدْخِلْهُ الْجَنَّةَ، وَأَعِذْهُ مِنْ عَذَابِ الْقَبْرِ، وَمِنْ عَذَابِ النَّارِ».

"Allahumma ighfir lahu warhamhu, wa 'aafihi wa'fu 'anhu, wa akrim nuzulahu, wa wassi' mudkhalahu, waghsilhu bil-maa'i wath-thalji wal-barad, wa naqqihi minal-khataayaa kamaa naqqaytath-thawbal-abyadha minad-danas, wa abdilhu daaran khayran min daarihi, wa ahlan khayran min ahlihi, wa zawjan khayran min zawjihi, wa adkhilhul-jannah, wa a'idh-hu min 'adhaabil-qabr, wa min 'adhaabin-naar."41 Kenako apange Takbira, ndipo ayime pang'ono, kenako apereke salam imodzi kumanja kwake.

Nkhani yachitatu: Zakat:

1- Tanthauzo la Zakat ndi ulemelero wake:

Zakat pachiyankhulo ndi kukula ndi kuwonjezereka.

Zakat pa malamulo: ndi gawo lokakamizidwa mu chuma chodziwika, chopereka ku gulu la anthu lodziwika.

Iyi ndi nsanamila yachitatu mu nsanamila za Chisilamu, Ndipo yatchulidwa limodzi ndi Swala mu Qur'an m'malo makumi asanu ndi atatu kudzanso malo awiri zimenezi zikusonyeza ukulu wa kufunikira kwake.

Allah wapamwamba akuyankhula kuti:

﴿وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ...﴾

{Ndipo pempherani Swala moyenera ndikupereka Zakat...} [Surat Al-Baqarah:43]

Ndipo Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-adati:

«بُنِيَ الإِسْلَامُ عَلَى خَمْسٍ: شَهَادَةِ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّـهُ، وَأَنَّ مُحَمَّدًا رَسُولُ اللَّـهِ، وَإِقَامِ الصَّلَاةِ، وَإِيتَاءِ الزَّكَاةِ، وَحَجِّ الْبَيْتِ، وَصَوْمِ رَمَضَانَ».

«Chisilamu chinamangidwa pa nsanamila zisanu: Kuikira umboni kuti palibe oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Allah, ndikuti Muhammad ndi mtumiki wa Allah, kupemphera Swala moyenera, kupereka Zakat, kukachita Hajj ku nyumba ya Allah, ndi kusala kudya mwezi wa Ramadhan»42.

Ndipo Asilamu onse anavomerezana kuti ndi yokakamizidwa (Faradhwi), Ndi kusakhulupilira kwa amene wakana kukakamizidwa kwake, Ndi kum'menya nkhondo amene akukana kupereka Zakat.

2- Zoyenera kuti Zakat ikhale yokakamizika:

a)Ufulu: siyokakamizidwa kwa kapolo; chifukwa iye alibe chuma, ndipo chuma chomwe chili m'manja mwake n'cha mbuye wake, choncho Zakat yake iperekedwe ndi mbuye wake.

b) Chisilamu: siyokakamizidwa kwa osakhulupirira; chifukwa ndi ntchito yamapemphero ndi yomumvera Allah, ndipo osakhulupilira sali m'gulu la anthu oyenera kupembedza ndi kumvera.

c-Kukwana mulingo: siyokakamizidwa pa chuma chomwe sichikukwana mulingo wake, ndipo uwu ndi mlingo wodziwika wa chuma.

d) Umwini okwanira: kuti chuma chikhale cha munthu ndi umwini wake wokwanira bwino, palibe Zakat pa chuma chimene umwini wake sunakhazikike, monga ngongole ya kapolo yodziombolela.

e)Chumacho chidzungulire chaka: Malinga ndi nkhani yomwe ikuchokera kwa Aisha, Allah asangalasidwe naye, yomwe ikukathera kwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-:

«لَا زَكَاةَ فِي مَالٍ حَتَّى يَحُولَ عَلَيْهِ الْحَوْلُ».

"Palibe Zakat pachuma mpaka chitadzungulira chaka"43.

3-Mitundu ya chuma imene Zakat imakakamizidwa pa iyo:

Choyamba: nyama zoweta,

Izi ndi ngamila, ng'ombe ndi mbuzi komanso nkhosa, ndipo Zakat imakhala yokakamizidwa pa ziwetozi pakapezeka zinthu ziwiri:

1-Zisungidwe ngati zamkaka ndi kuberekana, osati zozigwiritsa ntchito.

2- Zikhale zodyetsedwa kubusa, Choncho Zakat si yokakamiza pa ziweta zimene zimadyetsedwa chakudya chimene adachigula, kapena adachitolera kuchokera ku msipu kapena kwina. Zakat siyipelekedwa pa ziweto zimene zimadya kubusa kwa gawo la chaka, osati chaka chonse kapena gawo lake lalikulu.

4-Mulingo wa zinyama zoweta:

1- Zakat ya ngamila:

Ngati zofunikira zakwaniritsidwa; ndiye pa ngamila zisanu zilizonse pamatulutsidwa mbudzi imodzi, pa khumi mbudzi ziwiri, pa khumi ndi zisanu mbudzi zitatu, ndipo pa makumi awiri mbudzi zinayi, Monga momwe zatsimikizira zochita za Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-ndi mgwirizano wa anthu ophunzira maphunziro a Chisilamu. Ngati zakwana ngamira makumi awiri ndi zisanu, pamenepo Zakaat yake ndi Bintu Makhadh, yomwe ndi ngamira yaikazi imene yakwanitsa chaka chimodzi nkulowa m'chaka chachiwiri, ndipo ngati itasowa, ndiye Ibnu Labuun imakwanira m'malo mwake (iyi ndi ngamila yaimuna yazaka ziwiri).

Ndipo ngamila zikakwana makumi atatu ndi zisanu ndi imodzi, mwa izo mumafunika kupereka Bintu Labuun: amene ali ngamila yaikazi yokwanitsa zaka ziwiri.

Ndipo zikafika makumi anayi ndi zisanu ndi imodzi; chofunika m’menemo ndi hiqqah, ndipo iyo ndi yomwe yakwanitsa zaka zitatu.

Ngamila zikafika makumi asanu ndi imodzi(60), imodzi; ndiye pakufunika Jadh’a, amene ndiye ngamila yomwe yakwanitsa zaka zinayi.

Ndipo ngati chiwerengero chonse cha ngamila chafika pa makumi asanu ndi awiri ndi zisanu ndi imodzi; ndiye m'menemo m'pofunika kupereka Binta Labun ziwiri.

Ndipo ngamila zikakwana makumi asanu ndi anayi ndi imodzi; m'menemo mumatulutsidwa Hiqqah ziwiri.

Choncho, ngati chiwerengero cha ngamila chitapitilira zana limodzi ndi makumi awiri, powonjezereka ndi imodzi, ndiye ndikokakamizidwa kupereka ngamila zitatu zachikazi za zaka ziwiri. Kenako, pa ngamila makumi anayi zilizonse, iperekedwe ngamila imodzi yachikazi yazaka ziwiri, ndipo pa ngamira makumi asanu zilizonse, iperekedwe ngamira imodzi yachikazi yazaka zitatu.

2- Zakat ya Ng'ombe:

Zakat yake imakakamizidwa ngati malamulo ake akwaniritsidwa, ng'ombezo zikakwana makumi atatu: mwana wa ng'ombe wamwamuna kapena wamkazi; ndipo ndi chiweto chomwe chakwanitsa chaka chimodzi nkulowa m'chaka chachiwiri.

Ndipo palibe kalikonse pansi pa 30.

Ndipo zikafika makumi anayi; chofunika kupereka ndi ng'ombe yaikazi yotchedwa Musinna, iyi ndi imene yakwanitsa zaka ziwiri.

Ngati chiwerengero cha ng’ombe chaposa makumi anayi; ndiye pa ng’ombe makumi atatu zilizonse pamafunika kupereka mwana wa ng’ombe wa chaka chimodzi (wamwamuna kapena wamkazi), ndipo pa ng’ombe makumi anayi zilizonse, ng’ombe yaikazi ya zaka ziwiri.

3- Zakat ya Mbuzi ndi Nkhosa:

Chiwerengero cha nkhosa ndi mbuzi chikafika makumi anayi, Zakat yake imakhala chiweto chimodzi: chomwe chingakhale nkhosa yaimuna kapena mbuzi yaikazi.

Palibe Zakat pa nkhosa ngati chiwerengero chake sichinafike makumi anayi. Ndipo chiwerengero cha nkhosa chikafika 121; chopereka chake chimakhala mbudzi ziwiri. Zikakwana mazana awiri ndi imodzi; m'menemo mumayenera kuperekedwa mbudzi zitatu.

Kenako chokakamizidwacho chimakhazikika pambuyo pa chiwerengerochi, ndipo n’kokakamiza kupereka pa mbudzi zana lililonse mbudzi imodzi, motero pa mbudzi mazana anayi pamatuluka mbudzi zinayi, ndipo zikupitilira chomwecho.

Chachiwiri: Zakat ya zotuluka m'nthaka:

Zotuluka mu nthaka zili mitundu iwiri:

1) Mbewu ndi zipatso.

2) Mitapo (myala ya m'migodi)

Mtundu woyamba: Mbewu ndi zipatso:

Kupeleka Zakat ndi kokakamizika mu mbewu; monga: Tiligu, Balere, ndi Mpunga. Komanso mu zipatso; monga: tende ndi mphesa, Ndipo sikokakamizidwa pa zomera zina; monga zitheba ndi ndiwo zamasamba.

Zoyenera kuti Zakat ikhale yokakamiza mu mbewu ndi zipatso:

1) Kukhala chinthu chosungika: siyiperekedwa Zakat pa zinthu zosasungika monga zipatso ndi masamba.

2) Chikhale chopimidwa ndi muyeso: palibe Zakat pa zinthu zogulitsidwa powerenga kapena polemera; monga mavwende, anyezi, makomamanga, ndi zina.

3)Kuti zikwanire mulingo: ndipo ndi ma ausuqi asanu, potero palibe Zakat pa zomwe zachepera pamenepo.

4) Mulingo ukhale wa mwini wake pa nthawi ya kukakamizika kwa Zakat.

Choncho amene wapeza umwini wake pambuyo poti nthawi yokakamizika kupereka Zakat yadutsa, sakakamizidwa kupeleka Zakat, monga ngati adachigula kapena kupatsidwa ngati mphatso pambuyo pokolola.

Nthawi yokakamizika yoperekera Zakat yake:

Zakat pa mbewu ndi zipatso imakhala yokakamizika pamene zayamba kukhwima, Chizindikiro chosonyeza kukhwima ndi monga zilili m'musimu:

A- Pa mbewu: ikalimba ndi kuuma.

b-Pa zipatso za tende: poyamba kufiira kapena kusanduka zachikasu.

c-Pa zipatso zamphesa: ndiko kukhala yofewa ndi zotsekemera.

Mulingo wake:

Mulingo wa mbewu ndi zipatso: ma ausuqi asanu, Wasaqi imodzi ndi maswā'a makumi asanu ndi limodzi, Choncho mulingo umakhala mayezedwe omwe Mtumiki amayeza pogwiritsa manja ake awiri okwana mazana atatu, ndipo m'makilogilamu ukufanana ndi: pafupifupi 900 kg.

Mulingo okakamizika opereka Zakat m'menemo:

Ndi koyenera kupereka chakhumi pa zomwe zathiriridwa popanda mtengo kapena kuvutikira; monga zija zothiriridwa ndi madzi a mvula ndi akasupe.

Ndipo theka la cha khumi liyenera kuperekedwa pa zomwe zidathiriridwa pogwiritsa ntchito ndalama ndi mphamvu; monga zomwe zimathiriridwa ndi madzi otungidwa kuchokera ku zitsime ndi mitsinje kudzera mwa zinyama kapena makina amakono.

Mtundu wachiwiri: Mitapo:

Mwa mitundu ya zotuluka m'nthaka: Ndi mitapo ya m'migodi, Icho ndi chomwe chimatulutsidwa m'nthaka, chosakhala cha mtundu wa nthaka; monga ngati Golide, Siliva, Chitsulo, ndi miyala yamtengo wapatali.

Nthawi yokakamizika ya Zakat mu zimenezo:

Akapeza chumacho n’kukhala mwini wake; apereke Zakat yake pompo pompo, popeza pa ichi sikufunika kudikira kuti chikwanire chaka. Ndipo mulingo wake ndimulingo wagolide ndi siliva, ndipo kumatulutsidwa mmenemo chachinayi cha chakhumi cha mtengo wake.

CHACHITATU: ZAKAT YA NDALAMA

Ndalama ndi izi: Golide, Siliva, ndi ndalama zamapepala, ndipo Zakat yake ndi yokakamizidwa, Umboni wake : ndi mau a Allah wapamwamba:

﴿...وَالَّذِينَ يَكْنِزُونَ الذَّهَبَ وَالْفِضَّةَ وَلَا يُنْفِقُونَهَا فِي سَبِيلِ اللَّهِ فَبَشِّرْهُمْ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ﴾

{Ndipo amene akusonkhanitsa golide ndi siliva popanda kuzipereka pa njira ya Allah, auze nkhani ya chilango chowawa}. [Surat Al-Tauba:34].

Umboni ochokera mu nkhani ya Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye:

«مَا مِنْ صَاحِبِ ذَهَبٍ وَلَا فِضَّةٍ لَا يُؤَدِّي فِيهَا حَقَّهَا؛ إِلَّا إِذَا كَانَ يَوْمَ الْقِيَامَةِ صُفِّحَتْ لَهُ صَفَائِحُ مِنْ نَارٍ».

«Palibe mwini golide kapena siliva amene sapereka choyenera chake; koma likadzafika tsiku la chiweluzo, zidzasandulitsidwa kukhala mapepala a moto»44.

Ndipo anthu ophunzira pa zachipembedzo cha Chisilamu adagwirizana onse kuti Zakat ndi yokakamizika pa golide ndi siliva, ndipo ndalama zamapepala zili ndi lamulo lofanana ndi la golide ndi siliva; chifukwa zatenga malo a zinthu ziwirizi pogwiritsidwa ntchito ngati ndalama.

Mulingo wa Zakat pa ndalama ndi mulingo wake okakamizika kupereka:

Mulingo wake ndi wa golide kapena siliva; chifukwa ndalama zinalowa m'malo mwa ziwirizi pa mtengo wake, ndipo zikafika pa mlingo wa chimodzi mwa izi ndiye Zakat imakhala yokakamizika, ndipo kawirikawiri masiku ano mlingo wa ndalama zamapepala amayerekezera ndi siliva; chifukwa ndi yotsika mtengo kuposa golide, choncho mulingo wake umafika msanga usanafike wa golide. Ndipo ngati Msilamu wapeza chuma chofikira mtengo wa (595) ma giramu a siliva, ndipo nachikwanitsa chaka chimodzi, ndiye kuti Zakat yakakamizidwa m'chumacho. Mtengo wa giramu ya siliva umasintha nthawi ndi nthawi, choncho amene ali ndi ndalama zochepa ndipo sakudziwa ngati zakwana mulingo kapena ayi, afunse amalonda a siliva za mtengo wa giramu ya siliva, kenako nkuuchulukitsa ndi (595), ndipo chotuluka pamenepo ndiye mulingo.

Phindu:Akafuna kupereka zakaat ya chuma chake; agawe mulingo ndi 40, ndipo chomwe chituluke ndiye mulingo okakamizika kupereka.

Cha Chinayi:Zakat ya katundu wa malonda:

Ndi katundu okonzedwera kugulitsa ndi kugula, ndi cholinga chofuna kupeza phindu, Ndipo zinthu za malonda imalowamo mitundu yonse ya chuma kupatula ndalama; monga magalimoto, zovala, nsalu, zitsulo, matabwa, ndi zina zomwe zakonzedwela malonda.

Zoyenera kuti Zakat ya malonda ikakamizidwe:

1-Chikhale chake kudzera m'zochita zake; monga kugulitsa, kubwereketsa, ndi njira zina zopezera.

2-Akhale nacho ndi chitsimikizo cha malonda; ndiko kutsogoza cholinga chopeza phindu, chifukwa ntchito iliyonse imadalira chitsimikizo, ndipo malonda ndi ntchito, choncho nkoyenera kuti malonda alumikizane ndi chitsimikizo monga zimakhalira pa ntchito iliyonse.

3-Kuti mtengo wake ufike pa Niswabu ya golide kapena siliva.

4-Kukwanira kwa chaka pa icho, ndiko kudutsa kwa chaka chonse.

Katulutsidwe ka Zakat ya katundu wa malonda:

Katundu wa malonda amawerengedwa mtengo wake pakukwanira kwa chaka, ndi imodzi mwa ndalama ziwiri, golide kapena siliva, Ndipo ngati atafika pa mulingo wake poyerekeza ndi mtengo wa golide kapena siliva; apereke gawo limodzi mwa magawo makumi anayi (2.5%) la mtengo wake onsewo.

Chachisanu: Zakat ya Fitri:

Ndi sadaka yokakamizidwa pa kutha kwa mwezi wa Ramadhan, Inalamuridwa m'chaka chachiwiri chisamukireni Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kupita ku Madina.

Lamulo lake:

Zakat ya Fitr ndi yokakamizidwa kwa Msilamu aliyense amene ali ndi chakudya pa tsiku la Eid ndi usiku wake, choposa chimene chingamukwanire iye ndi banja lake. Ndipo ndi yokakamiza kwa Msilamu wina aliyense; wamwamuna kapena wamkazi, wamng'ono kapena wamkulu, mfulu kapena kapolo, kamba ka kuyankhula kwa Mtumiki:

«فَرَضَ رَسُولُ اللَّهِ ﷺ زَكَاةَ الْفِطْرِ عَلَى الْعَبْدِ وَالْحُرِّ، وَالذَّكَرِ وَالْأُنثَى، وَالصَّغِيرِ وَالْكَبِيرِ، مِنَ الْمُسْلِمِينَ».

«Analamulira Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- Zakat ya fitri kwa kapolo ndi mfulu, wamwamuna ndi wamkazi, wamng'ono ndi wamkulu, mwa Asilamu»45. Ndipo Faradhwi tanthauzo lake:adakakamiza.

Cholinga choikhanzikitsira:

Adanena mwan Abbas - Allah asangalasidwe nawo onse awiri-:

 

«فَرَضَ رَسُولُ اللَّهِ ﷺ زَكَاةَ الْفِطْرِ؛ طُهْرَةً لِلصَّائِمِ مِنَ اللَّغْوِ وَالرَّفَثِ، وَطُعْمَةً لِلْمَسَاكِينِ».

{Mtumiki wa Allah-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-adalamulira zopereka Zakat Fitr; monga choyeretsa kwa osala kudya ku zoyankhula zopanda pake komanso zonyansa, ndi cholinga chowadyesa anthu osauka}46.

Nthawi ya kukakamizika kwake ndi kupereka kwake:

Kupeleka Zakat ya Fitr kumakhala kokakamizika dzuwa likalowa usiku wa Eid. Ndi bwino kuipereka tsiku la Eid leni lenilo asanapite kokapemphera Eidyo. Ndipo si zololedwa kuichedwetsa pambuyo pa Swala ya Eid, Ngati aichedwetsa pambuyo pa swala ya Eid ayenera kuipereka ngati kulipira, ndipo adzakhala ochimwa chifukwa choichedwetsa pa nthawi yake.

Ndipo nkololedwa kuipereka tsiku limodzi kapena awiri lisanafike tsiku la Eid.

Muyezo wake ndi zinthu zomwe imatulutsidwamo:

Swa'a imodzi ya chakudya chozoloŵereka cha anthu a kudelako; monga mpunga, tende, tirigu kapena zina. Ndipo muyeso wa Swa'a': ndi pafupifupi makilogalamu atatu. Ndipo sikololedwa kupereka ndalama m'malo mwake, chifukwa ndikosemphana ndi lamulo la Mtumiki wa Allah-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.

Kutulutsa Zakat ndi owapatsa ake:

Nthawi yotulutsira:

Ndi chokakamiza kutulutsa Zakat nthawi yomweyo pamene nthawi yake yokakamizika yafika, Ndipo sizovomerezeka kuichedwetsa kupatula ngati pali chifukwa chomveka, monga ngati chuma chili m'dziko lakutali ndi iye ndipo palibe amene angamuimilire.

Malo ake otulutsira:

Zabwino ndiko kupereka Zakat m'dziko limene muli chumacho, Koma ndi zololedwa kuisamutsa kuchokera m'dziko limene muli chumacho kupita ku dziko lina pa nthawi izi:

A-Ngati m'dzikomo mulibe ofunikira Zakat.

b-Kupezeka kwa wachibale osauka m'dziko lina.

c-Ngati kwapezeka chifukwa chovomerezeka m'malamulo achisilamu choti isamutsidwe, monga: kuisamutsira kumadera a Asilamu omwe agwidwa ndi mavuto a njala ndi kusefukira kwa madzi.

Zakat ndi yokakamizidwa mu chuma cha mwana wamng'ono ndi wamisala, chifukwa cha umboni umene sukupatula aliyense, ndipo amene amayenera kuwaperekera ndi owaimira wawo pa chuma. Sikuloledwa kupeleka Zakat popanda chitsimikizo, Kamba ka Mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale kwa iye-:

«إِنَّمَا الْأَعْمَالُ بِالنِّيَّاتِ».

«Ndithu ntchito ina iliyonse idzalipidwa motengera chitsimikizo»47.

Olandira Zakat:

Mitundu ya anthu amene amapatsidwa Zakat alipo asanu ndi atatu:

Gulu loyamba:Osauka:

Ndipo iwo ndi amene sapeza zofunikira zawo zokwanira monga malo okhala, chakudya, ndi zovala, Ndipo mlingo wa Zakat umene amapatsidwa ndi umene ungawakwanire iwo ndi amene amawasamalira kwa chaka chimodzi.

Mtundu wachiwiri: masikini

Ndiwo anthu amene amapeza zinthu zowakwanira zambiri, koma osati kotheratu. mwachisanzo: munthu amene ali ndi malipiro, koma samukwanira chaka chonse.

Mulingo umene amapatsidwa wa Zakat: ndi chowakwaniritsira iwo ndi amene akuwasamalira kwa chaka chimodzi.

Mtundu wachitatu: Ogwira ntchito ya Zakat:

Ndiwo amene mtsogoleri amawapatsa udindo wosonkhetsa Zakat, kapena kuisunga, kapena kuifikitsa kwa osowa.

Mulingo umene amapatsidwa kuchokela ku Zakat: ndi mulingo wa malipiro awo pa ntchito yawo, ngati alibe malipiro ochokera ku boma.

Mtundu wachinayi: Oyikopa mitima yawo:

Awa ndi wina aliyense yemwe akuganiziridwa kuti akapatsidwa: alowa Chisilamu, kapena chikhulupiliro chake chilimba, kapena asiya kuwazunza Asilamu.

Mulingo opatsidwa wa Zakat: ulingane ndi zomwe zingakope mitima yawo.

Mtundu wachisanu: kumasula akapolo:

Tanthauzo lake ndi: kumasula akapolo ndi amene ali pa mgwirizano odziombola ku mabwana awo.

Ndipo Mukatab: ndiye kapolo amene wagwirizana ndi bwana wake zodziombola, Ndipo kumalowamo kuwombola Asilamu ogwidwa pa nkhondo.

Mtundu wa chisanu ndi umodzi: Angongole, ndipo ali mitundu iwiri:

Woyamba: Munthu amene ali ndi ngongole pa zosowa zake za iye mwini, ndipo sapeza cholipilira ngongole yakeyo. Ndipo amapatsidwa zokwanira kulipira ngongole yake.

Wachiwiri: amene ali ndi ngongole chifukwa choyanjanitsa anthu, Ndipo amapatsidwa chokwanira kulipira ngongole yake, ngakhale atakhala olemera.

Mtundu wachisanu ndi chiwiri: panjira ya Allah:

Ndipo iwo ndi amene amamenya nkhondo pa njira ya Allah.

Mulingo umene amapatsidwa kuchokera mu Zakat: ndi okwanira pa kumenya nkhondo pa njira ya Allah; monga zoyendera, zida, chakudya, ndi zina zotero.

Mtundu wa chisanu ndi chitatu: munthu wapa ulendo:

Iye ndi munthu wapaulendo amene ndalama zake zoyendetsera ulendo zatha, kapena waberedwa, ndipo sanatsale ndi ndalama zomwe zingamufikitse ku dziko lake.

Mulingo wa Zakat umene amapatsidwa: ndi mulingo umene ungamufikitse ku dziko lake, ngakhale atakhala ochita bwino kumeneko.

CHACHINAYI: SWAUMU (KUSALA KUDYA):

Kusala kudya ndiko:

Kumugwadira Allah posiya zonse zomasulitsa kuyambira kutuluka kwa m'bandakucha mpakana kulowa kwa dzuwa.

Ndipo iyi ndi nsanamila mu nsanamila za Chisilamu, Ndipo ndi chimodzi mwa malamulo okakamizidwa ndi Allah wapamwamba, Ndi nkhani yodziwika kwambiri m’chipembedzo. Ndipo umboni pa kukakamizidwa kwake ndi buku la Allah, chiphunzitso cha mtumiki wa Allah, ndiponso mgwirizano wa Asilamu.

Allah wapamwamba akuyankhula kuti:

﴿‌شَهۡرُ رَمَضَانَ ٱلَّذِيٓ أُنزِلَ فِيهِ ٱلۡقُرۡءَانُ هُدٗى لِّلنَّاسِ وَبَيِّنَٰتٖ مِّنَ ٱلۡهُدَىٰ وَٱلۡفُرۡقَانِۚ فَمَن شَهِدَ مِنكُمُ ٱلشَّهۡرَ فَلۡيَصُمۡهُ...﴾

{Mwezi wa Ramadhan ndi umene Qur'an idayamba kubvumbulutsidwa kwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- mu usiku wa Lailatul- Qadr,Allah adaibvumbulutsa Qur'an kuti ikhale yowawongelera anthu ku zinthu zabwino, ndipo mkati mwa buku limeneli muli ma umboni achiwongoko owonekera kwambiri,komanso bukuli ndi chisiyanitso cha zinthu zoona ndi zabodza, choncho kwa amene mwezi wa Ramadhan wamupeza kumachita kuti ali pa khomo,ndi wangwiro sakudwala,wakakamizidwa kusala kudya...}

[Al-Baqarah:185].

Zoyenera kuti kusala kudya mwezi wa Ramadhan kukhale kokakamiza:

1- Chisilamu; siyilandilridwa kwa osakhulupilira.

2- Kutha msinkhu, si kokakamizika kwa mwana, Kusala kudya kumavomerezeka kwa mwana ozindikira, ndipo kwa iye kumakhala kosakakamizidwa.

3-Nzeru, kusala kudya sikokakamizidwa kwa munthu wa misala, ndipo sikuvomerezeka kwa iye; chifukwa chakusowa nzeru zochitira chitsimikizo.

4- Kukwanitsa kusala kudya, Choncho, kusala kudya sikokakamizidwa kwa odwala amene akulephera kusala kudyako, Komanso sikokakamizidwa kwa munthu wa paulendo, Ndipo munthu odwala ndi wa paulendo akuyenera kudzabweza vuto lawo likazatha: matenda ndi kubwelera ku ulendo. Ndipo mwa zofunikira za kuvomerezeka kwake kwa mkazi: ndi kutha kwa magazi a matenda achizimai ndi a matenda a ubereki.

Kumatsimikizika kulowa kwa mwezi wa Ramadhan m'njira ziwiri izi:

A. Kuwoneka kwa mwezi wa Ramadhan, Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye:

«صُومُوا لِرُؤْيَتِهِ، وَأفْطِرُوا لِرُؤْيَتِهِ».

"Yambani kusala mukauona mwezi wa Ramadhan, komanso siyani kusala mukauona mwezi wa Shawwal"48.

B- Kukwaniritsa kuwerenga masiku makumi atatu a mwezi wa Sha'ban, zimenezi zimachitika ngati sudaoneke mwezi wa Ramadhan, kapena pali cholepheretsa pakuwonekako monga mitambo kapena fumbi kapena china chonga icho, chifukwa cha mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-oti:

«فَإِنْ غُمَّ عَلَيْكُمْ؛ فَأَكْمِلُوا عِدَّةَ شَعْبَانَ ثَلَاثِينَ يَوْمًا».

«Ngati kwaphimbidwa kwa inu; kwaniritsani chiwerengero cha Sha'ban masiku makumi atatu»49.

Kutsimikiza zokhuzana ndi kusala kudya:

Kusala kudya kuli ngati mapemphero ena aliwonse,sikumakhala kolondola popanda chitsimikizo, Nthawi yopangira chitsimikizo chosala kudya kokakamidzidwa, imakhala yosiyana ndi nthawi yosala kudya kosakakamizidwa, ndipo kufotokoza kwake kuli motere:

Choyamba: Kusala kudya kokakamiza; monga kusala kwa mwezi wa Ramadhan, kapena kubwenza masiku omwe anakudutsa, kapena kusala kudya koti unachita lonjezo, ndi kokakamizidwa kutsimikiza nthawi ya usiku m'bandakucha usanatuluke, Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-oti:

«مَن لَمْ يُبَيِّتْ الصِّيَامَ مِنَ اللَّيْلِ فَلَا صِيَامَ لَهُ».

«Kwa munthu amene sachita chitsimikizo chosala kudya nthawi ya usiku,kusala kwake kukhala kosalondola»50.

Chachiwiri: kusala kosakakamizidwa, ndipo nkololedwa kuti munthu apange chitsimikizo chake chake masana, Bola ngati sadachite chomasulitsa pambuyo poti m'bandakucha waonekera.

Zowononga kusala kudya:

Choyamba: Kugonana: munthu akagonana ndi mkazi, kusala kudya kwake kumawonongeka, ndipo akuyenera kudzabwenza kusala kudya tsiku limene anagonanalo, Pamodzi ndi kubwenza tsiku lomwe anamasula,akukakamizidwa kuchita chimodzi mu zinthu zochotsa uchimo wapangawo zomwe ndi: kumasula kapolo, Ngati sapeza chomwe angamasulire kapolo, asale kudya miyezi iwiri motsatizana, Ndipo ngati atalephera kutero pa chifukwa chovomerezeka m’chipembedzo, ayenera kudyetsa anthu osauka makumi asanu ndi limodzi, munthu osauka aliyense apasidwe theka la manja anayi a chakudya chomwe chimadyedwa m'deralo.

Chachiwiri: kutulutsa umuna: chifukwa cha kupyopyonana, kapena kugwirana, kapena kudziseweretsa, kapena kubwereza kuyang'ana, ndiye akuyenera kulipira kokha popanda kupereka Kaffara; chifukwa Kaffara imakhala pa kugonana kokha. Koma yemwe wagona akadzilotera ndikutulutsa umuna, sachita kalikonse, chifukwa zimenezo sadachite mwakufuna kwake, angosamba janaba basi.

Chachitatu: Kudya kapena kumwa mwadala: Malinga ndi mau a Allah wapamwamba:

﴿...وَكُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ حَتَّىٰ يَتَبَيَّنَ لَكُمُ ٱلۡخَيۡطُ ٱلۡأَبۡيَضُ مِنَ ٱلۡخَيۡطِ ٱلۡأَسۡوَدِ مِنَ ٱلۡفَجۡرِۖ ثُمَّ أَتِمُّواْ ٱلصِّيَامَ إِلَى ٱلَّيۡلِ...﴾

{Idyani ndipo imwani kufikira nthawi yomwe zaonekera kwa inu kuwala kwa m'bandakucha ndikuchoka kwa mdima wa usiku; kenako pitirizani kusala kudya posiya zonse zomasulitsa kusala kudya kufikira pomwe usiku wayamba polowa dzuwa...}. [Surat Al-Baqarah:187].

Koma amene wadya kapena kumwa chifukwa choiwala; palibe cholakwika chilichonse kwa iye. kamba ka kuyankhula uku:

«مَن نَسِيَ وَهُوَ صَائِمٌ، فَأَكَلَ أَوْ شَرِبَ، فَلْيُتِمَّ صَوْمَهُ، فَإِنَّمَا أَطْعَمَهُ اللَّهُ وَسَقَاهُ».

«Munthu ameme waiwala ali mkati mosala kudya, ndipo wadya kapena kumwa, apitirize kusala kudya kwakeko chifukwa choti Allah ndi amene wamudyetsa ndi kumumwesa»51.

Chachinayi: Kusanza mwadala, koma amene masanzi am'gonjetsa popanda kufuna kwake; siziwononga kusala kwake, Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-:

«مَنْ ذَرَعَهُ الْقَيءُ فَلَيْسَ عَلَيْهِ قَضَاءٌ، وَمَن اسْتَقَاءَ عَمْدًا فَلْيَقْضِ».

“Munthu amene wagonjetsedwa ndi masanzi, sayenera kubweza (swaum) ndipo amene wadzisanzitsa mwadala, abweze.”52.

5-Kutulutsa magazi mthupi; monga pochita Hijama, kapena kudula mtsempha n’kutulutsa magazi, kapena kupopa magazi n’cholinga chopereka kwa wodwala; ndipo zonsezi zimaononga kusala kudya. Koma kutulutsa magazi ochepa amene amatengedwa kuti akayezedwe, izi siziwononga kusala kudya, Ndiponso kutuluka kwa magazi mopanda kufuna munthu; monga kamfuno, kapena chifukwa cha zilonda, kapena kugulula dzino; izi siziononga kusala kudya.

Amene amaloledwa kumasula mu mwezi wa Ramadhan:

Gao loyamba: Anthu amene amaloledwa kumasula, komanso amakakamizidwa kubweza, ndipo iwo ndi awa:

Woyamba: Odwala amene akuyembekezeka kuchila, ndipo kusala kudya kumamupezesa vuto kapena kumulemela

Wachiwiri: munthu wapaulendo; kaya wakumane ndi zovuta pa ulendo kapena sadakumane nazo.

Umboni wa ziwirizi ndi mau a Allah wapamwamba:

﴿...وَمَن كَانَ مَرِيضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٖ فَعِدَّةٞ مِّنۡ أَيَّامٍ أُخَرَ...﴾

{...Kwa munthu amene angakhale kuti akudwala kapena ali pa ulendo ndipo kusala kudya kukumupezesa vuto,atha kumasula, ndipo akamasula akuyenera kudzabweza masiku omwe adamasulawo...} [Al-Baqarah:185].

Wachitatu: mkazi wapakati kapena oyamwitsa, ngati kusala kudya kukuwavuta, kapena kuwavulaza iwowo kapena ana awo, ndipo amawerengedwa ngati odwala, iwowa amaloledwa kumasula, Koma onse awiri akuyenera kubweza kusala kudya kwawo pa nthawi ina.

Wachinayi: Akazi omwe akudwala matenda achizimai komanso omwe akudwala matenda a ubereki, kumasula kwawo ndi chinthu chokakamizidwa, Ndipo kusala kwawo nkosavomerezeka, ndipo alamulidwa kubweza m’masiku ena.

Gao lachiwiri: Amene amaloledwa kusala, ndipo n'chokakamizika kwa iwo kupereka chiombolo popanda kubweza, ndipo iwo ndi:

Woyamba: odwala amene kuchira kwake sikuyembekezereka.

Wachiwiri: Nkhalamba imene singakwanitse kusala kudya.

Choncho anthu amenewa samasala, ndipo amadyetsa munthu osauka pa tsiku lililonse la mwezi wa Ramadhan, Ndipo munthu wachikulire akafika pa ukalamba otayisa nzeru, udindo otsatira malamulo a chipembedzo umamuchokera; choncho amaloledwa kumasula ndipo palibe chilichonse pa iye.

Nthawi yobwezera ndi lamulo lochedwetsa kubwezako:

Ndi kokakamiza kubweza kusala kwa mwezi wa Ramadhan, mwezi wina wa Ramadhan usanadze, Ndipo zabwino ndiko kufulumira kubweza, Ndipo sizololedwa kuchedwetsa kubweza mpaka kudutsa Ramadhan otsatira. Nkhani ikuchokera kwa Aisha-Allah asangalasidwe naye-amene adati:

«كَانَ يَكُونُ عَلَيَّ الصَّوْمُ مِنْ رَمَضَانَ، فَمَا أَسْتَطِيعُ أَنْ أَقْضِيَ إِلَّا فِي شَعْبَانَ لِمَكَانِ رَسُولِ اللهِ ﷺ».

«Ndinkakhala ndi ngongole ya kusala kwa Ramadhan, koma sindinkatha kubweza kupatula mwezi wa Sha'ban, chifukwa chotanganidwa ndi Mtumiki wa Allah-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye»53.

Kwa munthu amene wachedwetsa kubweza mpaka kudutsa Ramadhan otsatira, akuyenera kuchita chimodzi mu zinthu ziwiri izi:

1-Kuchedwetsa chifukwa cha vuto lovomerezeka ndi chipembedzo, monga: munthu kudwalabe mpaka kufika mwezi wina wa Ramadhan, ameneyu amangobweza basi.

2-Kuchedwetsa popanda chifukwa chovomerezeka ndi chipembedzo, munthu wotere amachimwa chifukwa cha kuchedwetsako ndipo ayenera kulapa, komanso abweze, ndi kudyetsa munthu osauka pa tsiku lililonse.

Kusala kudya kosakakamizidwa kwa munthu amene ali ndi ngongole yosala kudya:

Amene ali ndi ngongole ya Ramadhan; chabwino ndiko kuyamba kubweza ngongoleyo asanayambe kusala kudya kosakakamizidwa, Koma ngati kusala kwa Sunnah kuli kwa masiku amene nthawi yake imadutsa -monga kusala kudya tsiku la Arafah ndi Ashura-; ndiye asale masikuwo asanabweze ngongole chifukwa nthawi yobwezera kusala kudya ndi yotambasuka, koma masiku a Ashura ndi Arafah amadutsa. Koma sakuyenera kusala kudya masiku asanu ndi limodzi a Shawwal pokha pokha atatha kubweza ngongole yake.

Kusala kudya Koletsedwa:

1- Kusala tsiku la Eid Al-Fitr, ndi tsiku la Eidu Al-Adhuha; chifukwa ndi zoletsedwa.

2- Kusala kudya masiku odzinga zinyama a mwezi wa Dhul-Hijjah, Kupatula kwa munthu amene anayamba ndi Umrah kenako Hajj, ndiponso amene anaphatikiza Hajj ndi Umrah, ngati sanapeze chiweto choti adzinge, Masiku odzinga zinyama ndi: tsiku la khumi ndi chimodzi (11), tsiku la khumi ndi chiwiri (12), ndi tsiku la khumi ndi chitatu (13) mu mwezi wa Dhul-Hijjah.

3- Tsiku lokaikitsa chifukwa cha kukaikira -za kuoneka kwa mwezi- lomwe ndi tsiku la makumi atatu la mwezi wa Sha'aban, Ngati usiku wake uli wa mitambo kapena fumbi zomwe zimalepheretsa kuona mwezi.

Kusala kudya Kosayenera:

A-Kuwupatula mwesi wa Rajab pakusala mwezi umenewo okha. B-Kusala pa tsiku la chisanu lokha, chifukwa ndikoletsedwa, Tsono ngati asala tsiku la patsogolo pake kapena la pambuyo pake, kudedwako kumatha.

Kusala kudya kosakakamizidwa:

A-Masiku asanu ndi limodzi a mwezi wa Shawwal. B-Kusala masiku asanu ndi anayi a mwezi wa Dhul-Hijjah, ndipo lofunika kwambiri mwa masikuwa ndi tsiku la Arafa, kupatula kwa munthu ochita Hajj; pakuti iye si Sunnah kusala. Ndipo kusala tsikuli kumafafaniza machimo a zaka ziwiri. C-Kusala masiku atatu mwezi ulionse, ndipo zabwino n'kuti azikhala masiku oyera, omwe ndi: la khumi ndi chitatu, la khumi ndi chinayi, ndi la khumi ndi chisanu. D-Kusala tsiku lolemba ndi lachinayi pa sabata lililonse, chifukwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- adali kuwasala; chifukwa ntchito za akapolo zimaonetsedwa m'masiku amenewa kwa Allah.

Kusala kosakakamizidwa:

A-Kusala kudya komwe amasala mneneri Daud -mtendere ukhale pa iye-adali kusala kudya tsiku limodzi ndi kumasula tsiku lina.

B-Kusala mwezi wa Allah wa Muharram, umene ndi mwezi wabwino zedi kusala, ndipo chotsimikizika kwambiri mmenemo: kusala tsiku la Ashura, limene ndi la khumi la Muharram, ndipo amasalanso la chisanu ndi chinayi pamodzi nalo; chifukwa cha mawu ake a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-:

«لَئِنْ بَقِيتُ إِلَى قَابِلٍ لَأَصُومَنَّ التَّاسِعَ».

«Ngati nditakhale ndi moyo mpaka chaka chamawa, ndithu ndidzasala tsiku la chisanu ndi chinayi»54. Ndipo imafafaniza machimo a chaka chomwe chapita.

CHACHISANU: HAJJ NDI UMRAH

Hajj m'chiyankhulo: ndicho chifuniro. Ndiko kufuna kupita ku nyumba yopatulika ya Allah ndi malo Ake opatulika panthawi yapadera, ndikukachita mapemphero apadera.

Ndipo Umrah, m'chiyankhulo, ndiko kuyendera.

Kuyendera nyumba yopatulika ndikukachita mapemphero apadera munthawi iliyonse.

Ndipo Hajj ndi imodzi mwa nsanamila za Chisilamu ndi maziko ake akulu akulu, Ndipo inalamulidwa mu chaka chachisanu ndi chinayi cha chisamukire Mtumiki kupita ku Madinah, Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-adapanga Hajj imodzi yokha; yomwe ndi Hajj yomwe imadziwika kuti (Hajj yotsanzikana ndi Asilamu).

Ndipo Hajj ndi yokakamizidwa kamodzi pa moyo kwa yemwe ali ndi kuthekela, Ndipo Hajj yowonjezera pamenepo ndi yosakakamizidwa. Pomwe Umrah lamulo lake ndi loti yokakamizidwa potengera kuyankhula kwa anthu ophunzira ochuluka, Umboni wake ndi mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- pamene adafunsidwa kuti: “Kodi azimayi nawo akuloledwa kumenya nawo nkhondo?” ndipo adayankha kuti:

«نَعَمْ، عَلَيْهِنَّ جِهَادٌ لَا قِتَالَ فِيهِ: الْحَجُّ وَالْعُمْرَةُ».

""Inde, kwa iwo (akazi) alamuridwa kumenya nkhondo yopanda kumenyana yomwe ndi: Hajj ndi Umrah"55."

Malamulo opangitsa Hajj ndi Umrah kukhala Zokakamizidwa:

1- Chisilamu

2- Nzeru

3- Kutha Nsinkhu

4-Ufulu

5- Kukhala ndikuthekera kopanga mapempherowo

Ndipo kwa munthu wa mkazi pakuwonjezedwa chofunikira chachisanu ndi chimodzi; ndiko kupezeka kwa Mahram wake amene amayenda naye ulendo wokachita mapempherowa, Chifukwa sizovomerezeka kwa mkazi kuyenda ulendo wa Hajj kapena wina ulionse popanda munthu oti sangakwatirane naye, Kamba ka mau a Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-:

«لَا تُسَافِرُ الْمَرْأَةُ إِلَّا مَعَ ذِي مَحْرَمٍ، وَلَا يَدْخُلُ عَلَيْهَا رَجُلٌ إِلَّا وَمَعَهَا مَحْرَمٌ».

"Mkazi asayende ulendo pokha pokha ali ndi munthu oti sangakwatirane naye, ndipo mwamuna asalowe kwa iye pokha pokha ngati ali naye munthu oti sangakwatirane naye"56.

Ndipo munthu amene sangakwatirane ndi mkazi anthu wa mkazi ndi: mamuna wake amakhala gulu loyenda naye kamba koti ndi mamuna wake, kapena munthu amene ndi oletsedwa kumukwatira kwamuyaya; Mwa achibale; monga mchimwene wake, abambo ake, mchimwene wa abambo ake, mwana wamwamuna wa mchimwene wake, komanso mchimwene wa amayi ake, Kapena pa chifukwa chovomerezeka monga kukhala m’bale oyamwa naye bere limodzi, kapena kudzera mu ukwati monga mwamuna wa amayi ake ndi mwana wamwamuna wa mwamuna wake.

Kuthekera: ndiye mphamvu za chuma ndi za m’thupi, akhale okwanitsa kukwera chokwera ndi kupilira nawo ulendo, ndiponso kupeza chuma chokwanira kugwiritsa ntchito popita ndi pobwelera, Komanso apeze thandizo lokwanira la ana ake ndi onse amene amakakamizidwa kuwasamalira, kufikira adzabwelere kwa iwo.

Ndipo njira yopita ku Hajj ikhale yotetezeka pa moyo wake ndi chuma chake.

Ndipo yemwe ali ndi kuthekera ndi chuma chake koma osati ndi thupi lake, monga pokhala nkhalamba yokalamba kwambiri kapena wodwala matenda amgonamgona amene palibe chiyembekezo choti angachire; akukakamizidwa kuti apeze munthu oti akamuchitire Hajj ndi Umrah.

Kwa munthu amene akuimira wina pa Hajj ndi Umrah kuti kuimira kwake kukhale kovomerezeka, pamafunika zinthu ziwiri:

1-Ayenera kukhala oyenera kupanga pemphero lokakamizidwa la Hajj, ndipo ameneyu ndi Msilamu, otha nsinkhu komanso wanzeru.

2-Akhale atachita kale Hajj yake yoyamba ya Chisilamu.

Malo ndi nthawi yochitira chitsimikizo cha Hajj ndi Umrah:

Al-Mawaqeet: ndi mau ochulutsa a Miqat, ndipo m’chiyankhulo tanthauzo lake ndi: Malire. Pomwe pachipembedzo: ndi malo ochitira chitsimikizo cha Hajj ndi Umrah kapena nthawi yake.

Pemphero la Hajj lili ndi nthawi zake zokhazikitsidwa, komanso malo ake okhazikitsidwa ochitira chitsimikizo:

A- Mawaqeet a nthawi: Allah watchula ndi mau ake oti:

﴿ٱلۡحَجُّ أَشۡهُرٞ مَّعۡلُومَٰتٞۚ فَمَن فَرَضَ فِيهِنَّ ٱلۡحَجَّ...﴾

{Mapemphero Hajj ali ndi miyezi yodziwika, (yomwe ndi: Shawwal, Dhul Qa’da ndi Dhul Hijjah). Choncho, kwa amene watsimikiza kuchita Hajj m’miyezi imeneyo...}. [Al-Baqarah:197].

Ndipo miyeziyi ndi: Shawwal, Dhu Al-Qa'adah, ndi masiku khumi a mwezi wa Dhu Al-Hijjah.

b- Al-Mawaqeet a malo: awa ndi malire amene munthu wopanga Hajj sayenera kuwoloka kupita ku mzinda wa Makkah popanda kuchita chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira Hajj, Ndipo malowo ndi awa:

1- Dhul Hulayfa: Miqaat ya anthu a ku Madina.

2- Al-Juhfah: Miiqaat ya anthu a ku Shami, Egypt ndi Morocco.

3- Qarnul-Manazil: pomwe tsopano pakudziwika kuti As-Sayl; Miqaat ya anthu a ku Najd.

4- Dhaati 'Irqi: Miqaat ya anthu a ku Iraq.

5- Yalamlamu: Miqat ya anthu a ku Yemen.

Kwa munthu amene malo ake okhala ali mkati mwa malo amenewa; munthu ameneyo akuyenera kuchitira chitsimikizo komanso kuvala zovala zochitira Hajj kapena Umrah pa malo pake pomwe akukhalapo. Tsono kwa anthu a mzinda wa Makkah: akuyenera kuchita chitsimikizo ali mu mzinda wa Makkah, ndipo safunika kutuluka kupita ku malo ochitira chitsimikizo kuti akachite chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira Hajj. Koma akamafuna kuchita Umrah: akuyenera kutuluka ndikupita ku malo ochitira chitsimikizo omwe ali pafupi, ndikuvalira zovala zochitira Umrah. Ndipo munthu amene akufuna kuchita Hajj kapena Umrah akuyenera kuchita chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira mapempherowa kuchokera ku malo amene adawaika Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-, ndipo awa ndi malo a Al-Mawaaqeet amene afotokozedwa kale. Ndipo sizovomerezeka kwa amene akufuna kuchita Hajj kapena Umrah kuti adutse malo amenewa osachita chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira mapempherowo.

- Munthu aliyense amene akudutsa pa Miqaat yosakhala yake, akuyenera kuchitira chitsimikizo ndikuvala zovala zake zochitira Hajj kapena Umrah kuchokera pamalo amenewo.

Kwa munthu amene njira yake ikulowera ku Makkah, ndipo sakudutsa pa malo aliwonse mwa malo aja otchulidwa ochitira chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira mapempherowo, kaya pa mtunda, pa nyanja, kapena mu mlengalenga: akuyenera kuchitira chitsimikizo ndikuvala zovala zochitira mapempherowo pamene wayang'anizana ndi malo ochitira chitsimikizo amene ali pafupi naye. Malinga ndi mau a Umar mwana wa Khattabi - Allah asangalasidwe naye-: "Yang'anani malo oyang'anizana nao kuchokera m'njira yanu."57

-Kwa munthu amene ulendo wake ndi wopita kukachita mapemphero a Hajj kapena Umrah pogwiritsa ntchito ndege, akukakamizidwa kuchita chitsimikizo ndi kuvala zovala zochitira mapempherowa pamene ndege ikudutsa moyang'anizana ndi malo ochitira chitsimikizo amene ali pa njira yake, Ndipo sizovomerezeka kwa iye kuchedwesa chitsimikizo kufikira pomwe watsika pa bwalo la ndege.

Al-Ihram:

Uku ndiko kuchita chitsimikizo cholowera m'mapemphero (a Hajj kapena Umrah). Tsono pa Hajj: ndiko kuchita chitsimikizo cholowera m'mapemphero a Hajj, Tsono pa Umrah: ndiko kuchita chitsimikizo cholowera m'mapemphero a Umrah. Ndipo sakhala kuti wachita Ihram pokhapokha atachita chitsimikizo cholowa m'mapempherowo. Koma kungovala chabe zovala zochitira Hajj kapena Umrah popanda kuchita chitsimikizo, sikumawerengedwa kuti ndi Ihram.

Zinthu zolimbikitsidwa pochita Ihram:

1- Kusamba thupi lonse asanapange Ihram.

2- Kupaka mafuta onunkhiritsa kwa mwamuna pathupi pake, osati pa zovala zake za Ihram.

3- Kupanga kwake Ihram povala chovala choyera cha gawo la thupi la pansi komanso kumtunda, ndi ngwawira

4- Apange ihram atakwera, atayang'ana ku Qibla.

Mitundu ya mapemphero a Hajj:

Munthu amene akupanga Ihram amapatsidwa ufulu wosankha mtundu umene wafuna pa mitundu itatu ya mapemphero a Hajj, yomwe ndi iyi:

1- Tamattu'u; ndiko kuti munthu amachita chitsimikizo chopanga Umrah mu miyezi yokonzekera za Hajj, n'kuimaliza, kenako ndikudzachitanso chitsimikizo chochita Hajj chaka chomwecho.

2- Al-Ifraadu; kumeneko ndi kutsimikiza zochita Hajj yokha kuchokera ku Miiqaat, ndipo amakhalabe mu Ihram yake kufikira pomwe achite mapemphero a Hajj.

3- Al-Qiranu: kumeneko ndikuchita chitsimikizo chopanga Hajj ndi Umrah limodzi, kapena kuchita chitsimikizo chopanga Umrah, kenako nkuphatikizirapo Hajj asanayambe kuzungulira kwake, ndipo amachita chitsimikizo chopanga Umrah ndi Hajj kuchokera ku Miqat, kapena asanayambe kuzungulira kwa Umrah, ndipo amazungulira ndi kuyenda mwa ndawala kamba ka zonse ziwiri.

Ndipo pa Mutamatti'i ndi Qaarin pali Fidiya (kulipira), ngati iwo sali mwa anthu okhala pafupi ndi mzikiti opatulika (wa Ka'aba)

Ndipo pa mitundu itatu iyi ya mapemphero a Hajj, womwe uli wabwino kwambiri ndi: Tamattu'u; chifukwa Mtumiki-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- adawalamulira ophunzira ake kuti azichita mtundu wa Hajj umeneu58. Kenako Qiraanu; chifukwa umaphatikiza mapemphero a Hajj ndi a Umrah. Kenako Ifraadu.

c) Akapanga chitsimikizo cha chimodzi mwa mitundu imeneyi ya mapemphero; amatchula Talbiyah akangomaliza, ndipo amanena kuti:

«لَبَّيْكَ اللَّهُمَّ لَبَّيْكَ، لَبَّيْكَ لَا شَرِيكَ لَكَ لَبَّيْكَ، إِنَّ الْحَمْدَ وَالنِّعْمَةَ لَكَ وَالْمُلْكَ لَا شَرِيكَ لَكَ».

«Labbayka Allahumma labbayka, labbayka laa shariika laka labbayka, inna al-hamda wan-ni'mata laka wal-muluku, laa shariika laka»59.

Ndipo iyi ndi Sunnah, ndipo ndibwino kuitchula mochulukitsa, mwamuna azinena mokweza, ndipo akazi azinena chapansipansi.

Nthawi yake: Nthawi yake imayamba pambuyo pa Ihram, ndipo mapeto a nthawi yake ali motere:

Choyamba: Munthu amene akuchita Umrah amasiya kuchita talbiyah asanayambe kuzungulira Ka'aba.

Chachiwiri: ochita Hajj amaleka kuyankhula pamene wayamba kuponya miyala pa chipilala chachikulu tsiku la Eid.

Zinthu zoletsedwa kuzichita munthu amene wachita wavala nsalu ya Ihram:

Choletsedwa choyamba: Kumeta tsitsi la m'mutu, kapena kuliyepula, kapena kuzula tsitsi kuchokera malo alionse apa thupi pake.

Choletsedwa chachiwiri: Kuwenga zikhadabo kapena kuziyepula kuchokera ku dzanja kapena phazi popanda chifukwa, koma ngati chikhadabo chathyoka ndipo wachichotsa, palibe kulipira pa iye.

Choletsedwa chachitatu: Kuphimba mutu wa mwamuna ndi chinthu chogundana nao mutuo, monga: chipewa kapena nsalu.

Choletsedwa chachinayi: Kuvala kwa mwamuna chovala chosokedwa pathupi pake kapena mbali ina yathupi; monga malaya, nduwira, kapena thalauza. Al-Makheet: Ndi chilichonse chomwe chakonzedwa molingana ndi chiwalo, monga masokosi ovalira ngwawira, magolovesi, ndi masokosi wamba, Ndipo mkazi amavala zovala zimene wafuna pa nthawi ya Ihram chifukwa chofunikira kudzibisa, koma asavale Burqa, ndipo aphimbe nkhope yake ndi chovala china monga mpango kapena nsalu ya mkanjo wake akakumana ndi amuna adera. Asavale magolovesi m'manja mwake.

Choletsedwa chachisan: Kuzola mafuta onunkhira; chifukwa munthu amene ali mu Ihram amafunikira kuti apewe zinthu zapamwamba, zokometsera za dziko la pansi, ndi zosangalatsa zake, ndipo alunjike ku moyo wa tsiku lachimaliziro.

Choletsedwa cha chisanu ndi chimodzi: Kupha nyama yapamtunda ndi kuisaka, choncho munthu amene ali mu Ihram asasake nyama yapamtunda, asathandizirenso pa kuisaka kwake, ndiponso asaizinge.

Zaletsedwa kwa munthu amene ali mu Ihram kudya nyama yomwe waisaka, kapena yomwe yasakidwira iye, kapena yomwe wathandizira pa kuisaka, chifukwa kwa iye ili ngati chibudu.

Koma ponena za nyama za m'nyanja; sikoletsedwa kwa munthu amene ali mu Ihram kuzisaka. Ndipo sikoletsedwa kwa iye kuzinga nyama zapakhomo monga nkhuku ndi ziweto; chifukwa si nyama zosaka.

Choletsedwa chachisanu ndi ziwiri: Kudzimangitsira ukwati kapena kumangitsira wina, kapena kukhala mboni.

Choletsedwa chachisanu ndi zitatu: Kugonana; amene wagonana asanatuluke mu Hajj koyamba, Hajj yake yawonongeka, ndipo akuyenera kupitiriza ndikumaliza zochita zake za Hajj, ndipo azabweze chaka chotsatira, komanso akuyenera kupereka nsembe ya Ngamila. Ndipo ngati zachitika atatuluka mu Hajj koyamba; Hajj yake siionongeka, ndipo ayenera kulipira chiwombolo pozinga chiweto.

Ndipo mkazi pa zimenezi ali ofanana ndi mwamuna, ngati wachita mwakufuna kwake.

Choletsedwa chachisanu ndi chinayi: Kukhuzana thupi popanda kuchita ukwati. Sikuloledwa kwa munthu amene ali mu Ihram kukhuzana ndi mkazi, chifukwa ndi njira yomwe imatsogolera ku ukwati woletsedwa, ndipo tanthauzo la kukhuzanaku ndi kugwirana ndi mkazi mwa chilakolako.

UMRAH:

A-Nsanamila za Umrah:

1- Kuvala nsalu ya Ihram.

2- Kuzungulira Ka'aba.

3- Kuyenda ndawala pakati pa Safa ndi Marwa.

B- ZOKAKAMIZA KUCHITA NTHAWI YA UMRAH:

1- Kuvala nsalu ya Ihram pa malo olamuridwa pa malamulo.

2- Kumeta kapena kuyepula tsitsi.

C- KACHITIDWE KA UMRAH:

Chinthu choyamba chimene ochita Umrah amayamba nacho, ndiko kuzungulira kasanu ndi kawiri, ayambire pa mwala wakuda ndipo amarizirenso pomwepo, Nthawi yochita Tawaf yake akhale oyeresedwa ku umve, abise maliseche ake kuyambira pa mchombo mpaka ku mawondo, Ndi Sunnah kwa iye pa nthawi yonse yozungulira Ka'aba; kuvundukula phewa lake lakumanja, ndikudutsitsa nsalu yake ya kumtunda pansi pa nkhwapa yake, ndipo tsonga za nsaluyo nkuika pamwamba pa phewa lake lakumanzere, Ndipo akakwaniritsa kuzungulira kwachisanu ndi chiwiri, asiye kuvundukula ndipo aphimbe mapewa ake onse awiri ndi nsalu yake.

Ndipo alunjike ku mwala wakuda, ngati angakwanise kuupyopyona aupyopyone, ngati sangakwanise, augwire ndi dzanja lake lakumanja ngati zingatheke, ndikupyopyona dzanja lake, Ndipo ngati sizingatheke kuugwira mwalawo, akuyenera kuulozera ndikukweza dzanja lake lakumanja uku akunena kuti: «Allah Akbar» kamodzi, ndipo sakuyenera kupyopyona dzanja lake, komanso asaime. Kenako apitirize kuzungulira kwake, uku akuika nyumba ya Allah (Ka'aba) kudzanja lake lamanzere, ndipo ndisunnah kuti ayende mofulumira pakuzungulira koyamba mpaka kwachitatu, Al-Ramli: ndiko kuyenda mofulumira uku akuyandikisa mapazi.

Ndipo akadutsa pa ngodya yakumanja -ndipo imeneyi ndi ngodya yachinayi ya Ka'aba- ngati zingatheke kwa iye, aigwire ndi dzanja lake lakumanja popanda kunena Takbir kapena kuipyopyona, ndipo ngati sizingatheke kuigwira, apitirire osailozera kapenanso osanena Takbiir. Ndipo anene pakati pa ngodya yakumanja ndi ya mwala wakuda:

﴿...رَبَّنَآ ءَاتِنَا فِي ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٗ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ حَسَنَةٗ وَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ﴾

{...Ambuye wathu Allah tipatseni mtendere wa dziko lapansi komanso mutipange kukhala ogwira ntchito zabwino pa dziko la pansi lino ndipo ku umoyo omwe ukudza mukatipange kukhala opambana pokatilowesa ku minda ya mtendere ndikukatipulumutsa ku zilango zaku moto}.

[Al-Baqarah:201].

Akamariza kuzungulira nyumba ya Allah, apemphere maraka awiri kumbuyo kwa malo omwe ankaima Abraham nthawi yomanga Kaaba ngati kuli kotheka, ndipo ngati sizingatheke, apemphelere malo ena alionse mu mzikiti opatulika Ndi Sunnah kuti pa raka yoyamba, pambuyo powerenga Al-Fatiha, awerenge Surah (Al-Kafirun). Pa raka yachiwiri, pambuyo powerenga Al-Fatiha, awerenge Surah (Al-Ikhlas). Kenako apite ku malo okayendera ndawala, n’kukayenda ndawala pakati pa Safa ndi Marwa kuyenda maulendo okwanira asanu ndi awiri; kupita kwake ndiulendo umodzi ndipo kubwelera kwake ndi ulendo wina.

Kuyenda ndawala kumayambira pa Safa, n'kukwera pamwamba pake kapena kuima pompo, ndipo kukwera pamwamba pa Safa ndi kwabwino kwambiri ngati nkotheka. Kenako awerenge mau a Allah wapamwamba:

﴿‌إِنَّ ٱلصَّفَا وَٱلۡمَرۡوَةَ مِن شَعَآئِرِ ٱللَّهِ...﴾

{Ndithudi mapiri awiri odziwika kuti Safa ndi Marwa omwe awandikana ndi Kaaba ndi zina mwa zizindikiro zoonekera za malamulo a Chisilamu...} [Al-Baqarah:158].

Ndipo ndi bwino kuti ayang'ane ku Qibla, kenako amutamande Allah, ndi kumkuza, ndikuyankhula mau awa:

«لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ، وَاللَّهُ أَكْبَرُ، لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيكَ لَهُ، لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ، يُحْيِي وَيُمِيتُ، وَهُوَ عَلَى كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ، لَا إِلٰهَ إِلَّا اللَّهُ وَحْدَهُ، أَنْجَزَ وَعْدَهُ، وَنَصَرَ عَبْدَهُ، وَهَزَمَ الْأَحْزَابَ وَحْدَهُ».

"Laa ilaaha illa Allah, wallahu akbaru, laa ilaaha illa Allah wahdahu la sharika lahu, lahul-muliku walahul-hamdu, yuhyi wayumiitu, wahuwa a'la kulli shay'in qadiru, laa ilaaha illa Allah wahdahu, anjaza wa'adahu, wanaswara abudahu, wahazama al'ahzaba wahdahu"60. Kenako apemphe zomwe zapepuka atanyamula manja ake, ndipo abwereze dhikri imeneyi komanso kupempha pempholo kokwana katatu. Kenako atsike, ndipo ayende kupita ku Marwa, mpaka akafike pa chizindikiro choyamba, pamenepo mwamuna ayende mofulumira kwambiri kufikira akafike pa chizindikiro chachiwiri, Koma kwa mzimayi, si zolamuridwa kuyenda mofulumira pakati pa zizindikiro ziwirizi chifukwa thupi lake liyenera kubisidwa, ndipo chovomerezeka kwa iye ndi kuyenda mwa chizolowezi pa maulendo onsewo. Kenako ayende, ndipo akwere phiri la Marwa kapena ayime pomwepo, ndipo kukwera pa phirilo ndibwino kwambiri ngati zingatheke. Achite ndikunena ali pa phiri la Marwa zofanana ndi zomwe anachita ndikunena ali pa phiri la Safa, kupatula kuwerenga ndime yomwe ndi mau ake a Allah oti:

﴿‌إِنَّ ٱلصَّفَا وَٱلۡمَرۡوَةَ مِن شَعَآئِرِ ٱللَّهِ...﴾

{Ndithudi mapiri awiri odziwika kuti Safa ndi Marwa omwe awandikana ndi Kaaba ndi zina mwa zizindikiro zoonekera za malamulo a Chisilamu...} Ndipo izi ndi zolamuridwa pokwera pa Safa pa ulendo oyamba okha. Kenako atsike, ayende pa malo oyenda, ndi kuyenda mofulumira pa malo oyenda mofulumira kufikira atafika ku Safa, Achite zimenezo kasanu ndi kawiri, kupita kwake ndi ulendo umodzi, ndiponso kubwelera kwake ndi ulendo wina. Pa nthawi ya Sa'i yake, azichulukitsa dhikri (kumukumbukira Allah) ndi kupempha pempho lomwe lingapepuke. Ndipo akhale odziyeretsa ku unve waukulu ndi wa ung'ono, ngakhale atayenda popanda chiyero, zimenezo ndi zokwanira kwa iye. Momwemonso, ngati mkazi akumuyamba matenda a msambo kapena a uchembere atamaliza kuzungulira nyumba ya Allah; amatha kuyenda pakati pa Safa ndi Marwa, ndipo zimenezo n'zovomerezeka kwa iye; chifukwa kuziyeretsa si lamulo lokakamiza pa kuyenda kumeneko, koma ndi chinthu chokondedwa kutero.

Akamariza kuyenda; amete tsitsi la m'mutu mwake kapena kuliyepula, ndipo kumeta kwa mwamuna ndi komwe kuli kwabwino.

Zikatero amakhala wamariza mapemphero a Umrah.

HAJJ:

a-Nsanamila za Hajj:

1-Kuchita Ihram.

2-Kuima pa Arafa.

3- Kupanga Tawaf AI-ifadhwa (Kuzungulira Ka'aba pambuyo poponya timyala pa Jamaratul Aqaba).

4- Kuyenda pakati pa Safa ndi Marwa.

b- Zokakamizidwa za Hajj:

1- Kuchita Ihram pa Miqaat.

2- Kuima pa malo otchedwa Arafah pa tsiku la chisanu ndi chinayi la mwezi wa Dhul-Hijjah kufikira kulowa kwa dzuwa, kwa amene waimapo masana.

3-Kugona pa malo otchedwa Muzdalifah usiku wa tsiku la khumi la mwezi wa Dhul-Hijjah mpaka pakati pa usiku.

4- Kugona usiku pa malo otchedwa Mina pa masiku ozinga zinyama.

5- Kuponya timyala.

6- Kumeta kapena kuyepula tsitsi.

7- Kuzungulira Ka'aba kotsanzikana nayo.

C- KACHITIDWE KA MAPEMPHERO A HAJJ

Msilamu ayenera kuchita chitsimikizo cha Hajj yokha akafika pa Miqat, ngati nthawi ili yochepa. Ndipo akafika mu mzinda wa Makkah azungulire nyumba ya Allah ndikukayenda pakati pa Safa ndi Marwa, ndipo akuyenera kukhalabe mu Ihram yake kufikira pomwe adzapite ku phiri la Arafa pa tsiku la Arafa lomwe ndi tsiku la chisanu ndi chinayi, ndipo akhalebe komweko kufikira dzuwa litalowa,

Kenako achokeko uku akuchita talbiyah kupita ku Muzdalifah, ndipo akuyenera kukhala komweko kufikira atapemphera Fajr, kenako apitirize kukhala komweko akupanga ma dhikri,akuvomera kuitana kwa Allah ndi kumapempha mapempho kufikira pomwe kuyera kuonekere.

Kukayera, apite ku Mina dzuwa lisanatuluke, akaponye timyala tisanu ndi tiwiri pa Jamaratul Aqaba (chomwe ndi chipilala chachikulu), kenako amete kapena kuyepula tsitsi, kumeta ndi komwe kuli kwabwino.

Kenako akazungulire nyumba ya Allah (Tawaf al-Ifadwah), ndipo kumamukwanira kuyenda kwa pakati pa Safa ndi Marwa komwe anachita poyamba, zikatero mapemphero ake a Hajj amakhala atha, ndipo amapeza kumasuka kotheratu.

Ndipo zimamutsalira kuponya timyala pa tsiku la khumi ndi chimodzi ndi la khumi ndi chiwiri, ngati akufuna kunyamuka msanga; choncho agende zipilala zitatu, chipilala chilichonse ndi timyala tisanu ndi tiwiri, ndikuyankhula mau oti Allah Akbar poponya kamwala kalikonse. Ayambe ndi chipilala chaching'ono chomwe chili pafupi ndi mzikiti wa Al-Khaif, kenako chapakati, kenako chipilala cha Jamaratul Aqaba chomwe ndichotsiriza, ndipo chipilala chilichonse achigende ndi timyala tisanu ndi tiwiri. Ndipo ngati atafuna kuchedwa pambuyo pa tsiku la khumi ndi chiwiri (12), adzaponya timyala pa tsiku la khumi ndi chitatu (13) monga mmene anaponyera pa tsiku la khumi ndi chiwiri (12) ndi tsiku la khumi ndi chimodzi (11).

Nthawi yoponya timyala: Pambuyo popendama kwa dzuwa m'masiku onse atatu.

Ndipo ngati atanyamuka pa tsiku la khumi ndi chiwiri(12) dzuwa lisanabile palibe vuto, ndipo ngati atakhala mpaka ataponya timyala pa tsiku la khumi ndi chitatu(13) pambuyo popendama kwa dzuwa, zimenezo ndizo zomwe zili zabwino, kamba ka mau a Allah oti:

﴿‌...فَمَن تَعَجَّلَ فِي يَوۡمَيۡنِ فَلَآ إِثۡمَ عَلَيۡهِ وَمَن تَأَخَّرَ فَلَآ إِثۡمَ عَلَيۡهِۖ لِمَنِ ٱتَّقَىٰ...﴾

{....Kwa munthu amene akufun kuchoka mofulumira ku Mina pambuyo pogenda miyala pa 12 zul-hijjah,atha kutero palibe mchimo angapeze, kwa munthunso amene akufuna kuchedwa ndikuchoka ku Mina pa 13 zul-hijjah ndikumariza kugenda miyala,atha kutero vutonso palibe,zimenezi zikulolezedwa kwa munthu oopa Allah amene wachita mapemphero ake a Hajj moyenera ndi chiphunzitso cha Allah komanso Mtumiki wake....}.

[Surat Al-Baqarah:203].

Ndipo ngati akufuna kunyamuka ulendo obwerera kwao;azungulire Ka'aba kotsanzikana kasanu ndi kawiri, popanda kuyenda pakati pa Safa ndi Marwa.

Ndipo chabwino koposa - ngati munthu sanatenge chiyama chopereka nsembe - ndi chakuti achite chitsimikizo chopanga Umrah, kenako nkuchitanso chitsimikizo chochita Hajj pa tsiku lachisanu ndi chitatu, ndikuchita ntchito za Hajj zomwe zafotokozedwa kale (ndipo kachitidwe aka kamatchedwa Tammattu'u). Ngati atachita chitsimikizo chochita Hajj ndi Umrah limodzi, vuto palibe, ndipo imatchedwa Qiranu, ndipo kumeneko ndi kuchita chitsimikizo chopanga Umrah ndi Hajj limodzi, ndi kuchita Twawaf imodzi ndi sa'yi imodzi ya Ummah ndi Hajj.

Mutu wachitatu:

Zokhuza zochitika

Anthu ophunzira -Allah wapamwamba awachitire chifundo -alongosola maphunziro amene ali okakamizidwa pa munthu aliyense kuphunzira, Ndipo adanena za mlingo umene uli wokakamizika kwa Msilamu aliyense payekha kuti aphunzire, Ndipo adatchulapo mwa izo: kuphunzira malamulo a zamalonda kwa amene amachita malonda, kuti asagwere mu zoletsedwa kapena katapila mosadziwa. Ndipo padapezekanso umboni ochokera kwa ena mwa ophunzira a Mtumiki - Allah asangalasidwe nawo - otsimikizira zimenezo.

Umar mwana wa Khattabi- Allah asangalasidwe naye - adati: “Asagulitse aliyense mumsika wathu, koma yekhayo amene waphunzira bwino malamulo a chipembedzo”61.

Ali bin Abi Talib - Allah asangalasidwe naye - adanena kuti: "Amene angachite zamalonda asanaphunzire kaye malamulo ake, amira mu katapila, kenako n'kumiranso, kenako n'kumiranso. Tanthauzo lake: agwera mu katapila"62.

Ibn Aabidiin adanena posimba kuchokera kwa Al-Allami: "Ndipo kwakakamizidwa kwa munthu aliyense okutha nsinkhu wa mwamuna ndi wa mkazi, pambuyo pophunzira maphunziro a za chipembedzo ndi chiongoko, kuphunzira maphunziro a za wudhu, kusamba, Swala, ndi Swaum; ndi maphunziro a za Zakat kwa amene wakwanitsa mulingo, ndi Hajji kwa amene ili yokakamizika kwa iye, ndiponso za malonda kwa amalonda, kuti adziteteze ku zinthu zokayikitsa ndi zodedwa m'zochitika zawo zonse. Momwemonso kwa amisiri, ndipo aliyense amene akuchita ntchito iliyonse, nkwachikakamizo kwa iye kudziwa maphunziro ake ndi malamulo ake kuti apewe zoletsedwa m'menemo63."

Nawawi - Allah amuchitire chisoni -adanena kuti: Ndipo malonda, ukwati, ndi zofanana nazo zomwe si zokakamizika pachiyambi pake, ndikoletsedwa kuzichita kupatula atadziwa malamulo ake64.

Awa ndi ena mwa malamulo okhudzana ndi zochitika zandalama, omwe anakhanzikitsidwa ndi chilamuli cha Chisilamu:

1-Kuloleza chilichonse chimene chili ndi phindu lenileni kapena lochulukirapo; monga kugulitsa zinthu zololedwa ndi kuzigula, kulemba ganyu, ndi As-shuf'a (ufulu woyamba kugula)65.

2-Kuloledwa kwa zinthu zonse zotsimikizira ndi kusunga zofunika za anthu; monga Ar-Rahnu (Kupereka chikole) ndi Al-Ish-haadu (Kuikapo mboni).

3- Kulolezeka kwa zinthu zonse zaphindu kwa ogwirizana; monga Al-iqaala (kuthetsa mgwirizano), Al-khiyaar (Kuika mpata osankha), ndi kuika malamulo pa malonda.

4-Kuletsa chilichonse chomwe chikupezekamo kupondereza anthu, ndi kudya chuma chawo mopanda chilungamo, monga katapila, kulanda ndi kubisa katundu.

5-Kuvomerezeka kwa chilichonse chimene chili ndi kuthandizana pa zabwino: monga ngongole, kubwerekana zinthu, ndi kusungitsana zinthu.

6-Kuletsa zonse zomwe zikupezekamo kudya chuma popanda kugwira ntchito kapena kupeza phindu kapena kukhetsera thukuta; monga njuga ndi katapila.

7-Kuletsa zochitika zonse zamalonda zimene mwadzadza kusadziwa ndi chinyengo; monga munthu kugulitsa chinthu chimene sichili chake, ndiponso kugulitsa chinthu chosadziwika.

8-Kuletsa chilichonse chozembera Ku zinthu zoletsedwa; monga kugulitsa kwa malonda a Al-Inah66.

9-Kuletsa zinthu zosokoneza ku ntchito yomvera Allah; monga kugulitsa pambuyo pa Adhan yachiwiri ya tsiku la chisanu(Jumua).

10-Kuletsa chilichonse chobweretsa vuto, kapena kuyambitsa udani pakati pa Asilamu; monga kugulitsa zinthu zoletsedwa, komanso munthu kulowerera malonda a Msilamu nzake.

Ndipo pamene Msilamu wapeza chosamveka bwino pa chigamulo cha nkhani inayake; ayenera kufunsa Akatswiri a za Chisilamu, ndipo asachite kalikonse pa nkhaniyo mpaka atadziwa chigamulo cha Sharia chomwe chili pa nkhaniyo. Monga adanena Allah wapamwamba:

﴿‌...فَاسْأَلُوا ‌أَهْلَ ‌الذِّكْرِ إِنْ كُنْتُمْ لَا تَعْلَمُونَ﴾

{..Choncho afunseni eni kuzindikira ngati inu simukudziwa}. [Al-Nahl:43].

Izi ndizomwe zatheka kuzisonkhanitsa, Tikupempha Allah kuti atipatse mamphuziro othandiza ndi ntchito zabwino, ndithu Iye ndi owolowa manja, olemekezeka. Mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa Mtumiki wathu Muhammad, aku banja kwake ndi ophunzira ake, ndipo [Allah] apereke mtendere ochuluka kwambiri.

***

Mndandanda wa zolembedwa

 

MAU OYAMBA: 2

Gawo Loyamba: 3

Zokhudzana ndi chikhulupiliro 3

Mutu woyamba: Tanthauzo la Chisilamu ndi nsanamira zake: 3

Kufunika kwa chikhulupiliro cha umodzi wa Allah: 4

Tanthauzo la kuikira umboni kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu mmodzi yekha: 6

Tsono malamulo a mau a umboni oti: palibe oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu mmodzi yekha ndi awa: 7

Tanthauzo la mau oikira umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu ndi loti: 9

Mutu Wachiwiri: Tanthauzo la Chikhulupiliro ndi Nsanamila zake: 11

1) Kukhulupilira mwa Mulungu wapamwamba ndipo mkati mwake muli zinthu zitatu: 12

1- Kukhulupilira mwa Umbuye wake: 12

2- Kukhulupilira zoyenera kupembedzedwa kwake: 15

3- Kukhulupilira mu maina a Mulungu ndi mbiri zake: 19

2) Kukhulupilira mwa angelo 28

3) Kukhulupilira mabuku: 29

4) Kukhulupilira mwa Atumiki-mtendere ukhale pa iwo: 31

5) Kukhulupilira za tsiku lomariza: 32

A- Kukhulupilira za kuukitsidwa: 32

B- Kukhulupilira za chiwerengero ndi malipiro: 33

C- Kukhulupilira zoti kuli Minda ya mtendere ndi Moto: 33

6) Kukhulupilira za Chikonzero zabwino ndi zoipa zake: 34

Mutu wachitatu: Kupanga ubwino: 36

Nkhani yachinayi: Chidule cha maziko a ahali sunnah wal jamaa: 37

Gawo lachiwiri: Zokhudzana ndi mapemphero 39

Mutu Woyamba: Kudziyeretsa: 39

CHOYAMBA: MAGAWO A MADZI: 39

CHACHIWIRI: NYASI 40

CHACHITATU: ZIMENE ZILI ZOLETSEDWA KUCHITA KWA MUNTHU AMENE ALI NDI UVE: 43

CHACHINAYI: MIYAMBO YA NTHAWI YODZITHANDIZA KUCHIMBUZI: 46

CHACHISANU: MALAMULO A KUDZISUKA NDI KUDZIPUKUTA: 47

CHACHISANU NDI CHIMODZIMODZI: MALAMULO A UDHU: 48

CHACHISANU NDI CHIWIRI: MALAMULO A KUPAKA MADZI PA KHUFFU NDI SOKOSI: 50

CHACHISANU NDI CHITATU: MALAMULO A TAYAMMAM: 53

CHACHISANU NDI CHINAYI: MALAMULO A MSAMBO NDI MAGAZI A PAMBUYO POBEREKA 56

Mutu Wachiwiri: Swala: 58

CHOYAMBA: MALAMULO A ADHANA NDI IQAMA 58

CHACHIWIRI: ULEMELERO WA SWALA NDI UBWINO WAKE: 62

CHACHITATU: MALAMULO A SWALA: 64

Chachinayi: Nsanamira za Swala: 66

Chachisanu: Zinthu Zokakamizidwa Kuchita Popemphera: 72

Chachisanu ndi chimodzi: ma Sunnah a Swala: 73

CHACHISANU NDI ZIWIRI: KAPEMPHEREDWE KA SWALA: 76

Chachisanu ndi chitatu: zonyasa kuchita nthawi ya swala: 82

Chachisanu ndi chinayi: zowononga swala: 82

Chakhumi: Sujud ya kuiwala 83

Chakhumi ndi chimozi: Nthawi zoletsedwa kupemphera swala: 85

Chakhumi ndi chiwiri: swala yapagulu: 86

Chakhumi ndi chitatu: Swala ya mantha: 90

Kapempheredwe ka Swala ya mantha: 90

Chakhumi ndi chinayi: Swala ya tsiku la chisanu: 92

Chachisanu: Masunnah a tsiku la chisanu: 94

Kulipeza pemphero la lachisanu: 95

Chakhumi ndi chisanu: Swala ya anthu oti ali ndi vuto: 96

Cha Khumi ndi chisanu ndi chimodzi: Swala ya Eid ziwiri (Zisangalalo ziwiri): 100

Chakhumi ndi chisanu ndi chiwiri: Swala ya kadamsana: 103

Chakhumi ndi chisanu ndi chitatu: Swala ya kupempha mvula: 105

Cha Khumi ndi Chisano ndi Zinayi: Malamulo a Maliro: 107

Nkhani yachitatu: Zakat: 111

1- Tanthauzo la Zakat ndi ulemelero wake: 111

2- Zoyenera kuti Zakat ikhale yokakamizika: 112

3-Mitundu ya chuma imene Zakat imakakamizidwa pa iyo: 113

CHACHINAYI: SWAUMU (KUSALA KUDYA): 127

Zoyenera kuti kusala kudya mwezi wa Ramadhan kukhale kokakamiza: 128

CHACHISANU: HAJJ NDI UMRAH 138

Malamulo opangitsa Hajj ndi Umrah kukhala Zokakamizidwa: 140

Malo ndi nthawi yochitira chitsimikizo cha Hajj ndi Umrah: 142

Al-Ihram: 145

UMRAH: 150

HAJJ: 155

Mutu wachitatu: 158

Zokhuza zochitika 158

 

***

 

ny227v3.0 - 01/10/2026


Anaitulutsa Ahmad mu Musnad wake, nambala yake ndi (6072), komanso Tirmidhi (1535) ndipo adati: "nkhani yabwino."

Nkhaniyi anaitulutsa Bukhar mu buku lake la Al-Adab Al-Mufrad, nambala yake ndi (716), komanso Ahmad mu buku lake la Musnad, nambala yake ndi (19606), komanso Ad-Dhiyaa Al-Maqdisi mu buku lake la Al-Ahaadeeth Al-Mukhtaarah (1/150), ndipo Al-Albani adaitsimikiza kuti ndi yolondola mu buku la Sahih Al-Jaami' As-Swaghiir, nambala yake ndi (3731).

Idatulutsidwa ndi Muslim nambala yake (121), komanso ndi Ahmad mu Musnad nambala yake (10434).

5- (AL MADHIYI): Ndi madzi opyapyala opanda mtundu omwe amatuluka nthawi yoseweretsana, kapena pokumbukila za kugonana, kapena pofuna kutero, kapena poyang'ana kapena zinthu zina zotere. Ndipo amatuluka mwadontho-dontho, ndipo nthawi zina munthu samva kutuluka kwake. (AL WADIYI): Ndi madzi okhuthala oyera amene amatuluka pambuyo pokodza, kapena ponyamula chinthu cholemera.

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim ndipo nambala yake ndi (224).

Anaitulutsa Malik mu Al Muwatta nambala (680 ndi 219), komanso Al-Darimi nambala (312) ndi Abdulrazaq mu Musannaf wake nambala (1328), ndipo anatsimikiza za kuona kwake ndi Al Albaniy mu Irwa' al Ghalil nambala (122).

Anaitulutsa ndi Nasai (12808), komanso Ahmad (15423), ndipo Al-Albani adatsimikiza kulondola kwake mu buku la Irwaul Ghalil (121).

Anaitulutsa Ibn Majah, nambala yake ndi (594), komanso Ibn Hibban, nambala yake ndi (799), ndipo adaifooketsa Al-Albani m'buku la Dhaif Sunan At-tirmidhi, nambala yake ndi (146).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (142), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (122).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake mu bukumo ndi (7288), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (6066).

Ananena Sheikh wolemekezeka Abdul Aziz bin Baz (Allah awachitire chisoni) m'buku lake la mafatwa ake (29/ 141) kuti: (A Baihaq anawonjezera ndi njira yodalirika kuchokera kwa Jabir pambuyo pa mau akuti: «alladhiy wa'adtahu», mawu akuti: «innaka la tukhliful mi'ad»).

Anaitulutsa Al Tirmidhi,nambala yake ndi (2635).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake(82).

Nkhani ikupezeka mu buku la Tirmidhi, nambala yake ndi (265), ndipo adati: Ndi Hasan Swahih Gharib, ndipo Al-Albani adaitsimikiza kukhala Swahih mu buku la Swahih At-Targhib wat-Tarhib.

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar,nambala yake (1117).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar,nambala yake(6251),komanso mu buku la Muslim,nambala yake(884).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (756), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (872).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake mu bukumo ndi (793), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (398).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar,nambala yake ndi (812),komanso mu buku la Muslim,nambala yake ndi (490).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake (498).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (724), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (398).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar ndipo nambala yake ndi (797) komanso mu buku la Muslim ndipo nambala yake ndi (402).

Anaitulutsa Al tirmidhi, nambala yake ndi (839).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake (6008).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake (1110).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake (835).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (743), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (399).

Hadisi ikupezeka mu buku la Tirmidhi, nambala yake ndi (266).

Nkhani imeneyi ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake(588).

Anaitulutsa Abu Dawood, nambala yake (5168).

Nkhani ikupezeka mu buku la Tirmidhi, nambala yake ndi (284).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake(1484).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (609), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (602).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (4130), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (842).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake (865).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (934), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (851).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake(1081), komanso mu buku la Muslim, nambala yake(693).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1012), komanso mu buku la Muslim ndipo nambala yake ndi (894).

Anaitulutsa Abu Daud (3201), ndi Tirmidhi (1024), ndipo adati: Iyi ndi nkhani yabwino komanso yolondola.

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim,nambala yake(962).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (8), komanso mu buku la Muslim ndipo nambala yake ndi (111).

Nkhani ikupezeka mu buku la Ibn Majah, nambala yake ndi (1792), komanso mu buku la Tirmidhi, nambala yake ndi (63) ndi (631).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1402), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (2287).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1432), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (984).

Anaitulutsa Abu Daud, nambala yake (1609), ndi Ibn Maajah, nambala yake (1827), ndipo Al-Albani anaitsimikiza kukhala yolondola mu Sahih Abi Daud, nambala yake (1609).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (1907).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1810), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (1086).

Ikupezeka mu buku la Bukhar (1909).

Anaitulutsa Ahmad (26457), komanso Abu Daud (2454), ndi Al-Nasaiu (2331) ndipo mauwo ndi ake.

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (6669), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (2709).

Anaitulutsa Abu Daud (2380), Tirmidhi (719), komanso Ibn Majah (676).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1849), komanso mu buku la Muslim, nambala yake ndi (1846).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake (1134).

Anaitulutsa Ahmad (25198), komanso Al-Nasai (2627) ndi Ibn Majah (2901).

Ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1862), komanso mu buku la Muslim, ndipo nambala yake ndi (1341).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake ndi (1531).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake (1211).

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, nambala yake (1549).

Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, nambala yake (1218).

Anaitulutsa Tirmidhi pa nambala (487), ndipo anati:nkhaniyi ndi yabwino koma yachilendo. ndipo Al-Albani adatsimikiza kuti ndi yabwino.

Onani: Mughni al-Muhtaj (2/22).

Hashiyat Ibn Abidin (1/ 42).

Onani: Al Majmuu (1/50).

Ash-Shufa: Kukhala ndi ufulu munthu wothandizana pa umwini wa chinthu kutenga gao la mzake lomwe waligulitsa kwa wina pomubwenzera wogulayo ndalama zake zomwe wagulira.

Malonda otchedwa Al-Iinah: Ndi pamene munthu akumugulitsa nzake chinthu pa ngongole ndikumupatsa chinthucho, kenako iye mwini n'kuchigulanso chinthucho asanalandire malipiro aja, pa mtengo wotsika kuposa oyamba uja komanso olipira pompo pompo.

Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar,nambala yake (8).